Hoseya 10:1-15
10 “Isiraeli ndi mtengo wa mpesa wowonongeka* umene ukubereka zipatso.+
Pamene zipatso zake zikuchuluka, mʼpamenenso akumanga maguwa ambiri.+Pamene zokolola zikuchuluka mʼdziko lake, mʼpamenenso akumanga zipilala zopatulika zokongola kwambiri.+
2 Mtima wawo ndi wachinyengo.Tsopano iwo adzapezeka ndi mlandu.
Pali wina amene adzagwetse maguwa awo ansembe ndiponso zipilala zawo zopatulika.
3 Ndiyeno iwo adzanena kuti, ‘Tilibe mfumu+ chifukwa sitinaope Yehova.
Ndipo kodi mfumu ingatichitire chiyani?’
4 Iwo amalankhula mawu opanda nzeru, amalumbira monama+ ndiponso amachita mapangano.Choncho chiweruzo chimene chikubwera chili ngati zomera zapoizoni mʼmunda.+
5 Anthu a ku Samariya adzachita mantha ndi fano la mwana wa ngʼombe la ku Beti-aveni.+
Anthu ake adzalilirira.Nawonso ansembe a mulungu wachilendo, amene ankasangalala ndi fanolo komanso ulemerero wake, adzalilirira.Chifukwa lidzatengedwa kupita kudziko lina.
6 Wina adzapita nalo kudziko la Asuri nʼkukalipereka ngati mphatso kwa mfumu yaikulu.+
Efuraimu adzachititsidwa manyazi,Ndipo Isiraeli adzachita manyazi chifukwa cha malangizo amene ankatsatira.+
7 Samariya pamodzi ndi mfumu yake adzawonongedwa,*+Ngati kanthambi kothyoledwa mumtengo kamene kakuyandama pamadzi.
8 Malo okwezeka a ku Beti-aveni,+ omwe ndi tchimo la Isiraeli,+ adzawonongedwa.+
Minga ndi zitsamba zobaya zidzamera pamaguwa awo ansembe.+
Anthu adzauza mapiri kuti, ‘Tikwirireni!’
Adzauzanso mapiri angʼonoangʼono kuti, ‘Tigwereni!’+
9 Inu Aisiraeli, mwakhala mukuchimwa kuyambira pa nthawi ya zochitika za ku Gibeya.+
Kumeneko anthu anapitirizabe kuchimwa.
Nkhondo sinawononge anthu onse osalungama ku Gibeya.
10 Ndikadzafuna ndidzawalanga.
Anthu a mitundu ina adzasonkhana kuti alimbane nawo,Pamene adzamangiriridwa goli la zolakwa zawo ziwiri.*
11 Efuraimu anali ngʼombe* yophunzitsidwa bwino yokonda kupuntha mbewu,Choncho ine sindinawononge khosi lake lokongola.
Koma ndidzachititsa kuti wina akwere pamsana pa Efuraimu.+
Yuda adzalima, Yakobo adzamusalazira zibulumwa za dothi.
12 Dzalani mbewu zachilungamo ndipo kololani chikondi chokhulupirika.
Limani munda panthaka yabwino,+Pamene muli ndi nthawi yofunafuna Yehova,+Mpaka iye atabwera nʼkukulangizani mwachilungamo.+
13 Koma mwalima zoipa,Ndipo mwakolola zosalungama.+Mwadya zipatso za chinyengo chanu.Chifukwa mukudalira njira zanu,Ndiponso kuchuluka kwa asilikali anu.
14 Pakati pa anthu a mtundu wanu padzakhala chisokonezo.Ndipo mizinda yanu yonse yokhala ndi mipanda yolimba idzawonongedwa,+Ngati mmene Salimani anawonongera Beti-aribeliPa tsiku lankhondo, pamene azimayi ndi ana awo anawanyenyanyenya.
15 Inu anthu a ku Beteli, wina adzakuchitaninso zimenezi+ chifukwa ndinu oipa kwambiri.
Ndithu, mfumu ya Isiraeli idzawonongedwa* mʼbandakucha.”+