Hoseya 11:1-12
11 “Isiraeli ali mnyamata ndinamukonda,+Ndipo ndinaitana mwana wangayu kuti atuluke mu Iguputo.+
2 Pamene iwo* ankawaitana kwambiri,Mʼpamenenso iwo ankawathawa kwambiri.+
Ankapereka nsembe kwa zifaniziro za Baala,+Ndipo nsembezo ankaziperekanso kwa zifaniziro zogoba.+
3 Koma ndine amene ndinaphunzitsa Efuraimu kuyenda,+ ndipo ndinkamunyamula mʼmanja mwanga+Koma iye sanavomereze kuti ndinamuchiritsa.
4 Ndinkawakoka mokoma mtima ndiponso mwachikondi,*+Kwa iwo ndinali ngati wochotsa goli mʼkhosi* mwawo,Ndipo mwachikondi ndinkabweretsera aliyense chakudya.
5 Iwo sadzabwerera kudziko la Iguputo, koma Asuri adzakhala mfumu yawo,+Chifukwa anakana kubwerera kwa ine.+
6 Lupanga lidzazungulira mʼmizinda yake+Ndipo lidzawononga mipiringidzo nʼkupha anthu chifukwa cha zoipa zimene ankafuna kuchita.+
7 Anthu anga atsimikiza kuti akhale osakhulupirika kwa ine.+
Ngakhale kuti anawaitanira kumwamba,* palibe amene anaimirira.
8 Kodi ndikusiye chifukwa chiyani iwe Efuraimu?+
Kodi ndikupereke kwa adani chifukwa chiyani iwe Isiraeli?
Kodi ndikuchitire zinthu ngati Adima chifukwa chiyani?
Kodi ndikusinthirenji kukhala ngati Zeboyimu?+
Koma ndasintha maganizoNdipo ndayamba kukumvera chisoni.+
9 Sindidzasonyeza mkwiyo wanga woyaka moto.
Sindidzawononganso Efuraimu+Chifukwa ndine Mulungu, osati munthu.Ndine Woyera pakati panu,Ndipo sindidzabwera kwa inu nditakwiya.
10 Iwo adzatsatira Yehova ndipo iye adzabangula ngati mkango.+Ndipo akadzabangula, ana ake adzabwera akunjenjemera kuchokera kumadzulo.+
11 Iwo adzabwera akunjenjemera ngati mbalame akamadzachokera ku Iguputo.Adzabwera ngati njiwa kuchokera kudziko la Asuri.+Ndipo ndidzawachititsa kukhazikika mʼnyumba zawo,” watero Yehova.+
12 “Efuraimu amandiuza mabodza okhaokha.Kulikonse kumene ndingayangʼane, ndikuona chinyengo cha Isiraeli.+
Koma Yuda akuyendabe ndi Mulungu,Ndipo iye ndi wokhulupirika kwa Woyera Koposa.”+
Mawu a M'munsi
^ Kutanthauza aneneri ndi anthu ena amene ankatumidwa kuti akalangize Aisiraeli.
^ Kapena kuti, “zingwe za kukoma mtima,” ngati zimene kholo limagwiritsa ntchito likamaphunzitsa mwana kuyenda.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “munsagwada.”
^ Kapena kuti, “anawaitana kuti ayambirenso kulambira koona.”