Hoseya 12:1-14

  • Efuraimu ayenera kubwerera kwa Yehova (1-14)

    • Yakobo analimbana ndi Mulungu (3)

    • Yakobo analira kuti apeze madalitso a Mulungu (4)

12  “Efuraimu akudya mphepo. Akuthamangitsa mphepo yakumʼmawa tsiku lonse. Iye akuchulukitsa mabodza ndi chiwawa. Wachita pangano ndi Asuri+ ndipo wapititsa mafuta ku Iguputo.+   Pali mlandu umene Yehova akufuna kuimba Yuda.+Adzalanga Yakobo mogwirizana ndi njira zake.Ndipo adzamubwezera mogwirizana ndi zochita zake.+   Pamene Yakobo anali mʼmimba anagwira chidendene cha mʼbale wake.+Iye analimbana ndi Mulungu ndi mphamvu zake zonse.+   Anapitiriza kulimbana ndi mngelo ndipo anapambana. Analira komanso anachonderera kuti amudalitse.”+ Mulungu anamupeza ku Beteli ndipo kumeneko Mulungu analankhula nafe.*+   Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba,+Amakumbukiridwa ndi dzina lakuti Yehova.+   “Choncho bwerera kwa Mulungu wako.+Uzisonyeza chikondi chokhulupirika ndi chilungamo,+Ndipo nthawi zonse uziyembekezera Mulungu wako.   Koma mʼmanja mwa wamalonda muli masikelo achinyengo.Iye amakonda kuba mwachinyengo.+   Efuraimu akupitiriza kunena kuti, ‘Inetu ndalemeradi,+Ndapeza chuma.+ Pa ntchito zanga zonse, palibe amene angapeze cholakwa kapena tchimo.’   Koma ine ndine Yehova Mulungu wako kuchokera pamene unali ku Iguputo.+ Ndidzakuchititsa kukhalanso mʼmatenti,Ngati pa masiku achikondwerero. 10  Ndinalankhula ndi aneneri,+Ndipo ndinawaonetsa masomphenya ambiri.Ndinalankhula mafanizo kudzera mwa aneneri. 11  Ku Giliyadi anthu akuchita zachinyengo*+ ndiponso akulankhula mabodza. Ku Giligala, akupereka nsembe ngʼombe zamphongo.+Ndipo maguwa awo ansembe ali ngati milu yamiyala mʼmunda.+ 12  Yakobo anathawira mʼdera la Aramu.*+Ndipo Isiraeli+ ankagwira ntchito kumeneko kuti apeze mkazi,+Ankalondera nkhosa kuti apeze mkazi.+ 13  Yehova anagwiritsa ntchito mneneri kutulutsa Aisiraeli ku Iguputo,+Ndipo mneneri ankalondera Aisiraeli.+ 14  Efuraimu wakhumudwitsa kwambiri Mulungu.+Mlandu wake wamagazi uli pa iyeyo,Ndipo Ambuye adzamubwezera kunyoza kwake.”+

Mawu a M'munsi

Ayenera kuti akutanthauza mbadwa za Yakobo.
Kapena kuti, “zamatsenga.”
Kapena kuti, “Siriya.”