Hoseya 13:1-16

  • Efuraimu anaiwala Yehova chifukwa cholambira mafano (1-16)

    • ‘Imfa, kodi mphamvu yako ili kuti?’ (14)

13  “Efuraimu akalankhula, anthu ankanjenjemera.Iye anali wolemekezeka mu Isiraeli,+ Koma anapezeka ndi mlandu wolambira Baala+ ndipo anafa.  2  Tsopano iwo akuchita machimo ena,Ndipo akugwiritsa ntchito siliva wawo popanga zifaniziro zachitsulo.+Amapanga mafano mwaluso, koma zonsezi ndi ntchito za amisiri. Iwo amauza mafanowo kuti, ‘Amuna opereka nsembe akise mafano a ana angʼombe.’+  3  Choncho iwo adzakhala ngati mitambo ya mʼmawa,Ndiponso ngati mame amene sachedwa kuuma.Adzakhalanso ngati mankhusu* amene amauluzika ndi mphepo kuchokera pamalo opunthira mbewu,Ndiponso ngati utsi umene umatuluka mʼchumuni kudenga.  4  Koma ine ndine Yehova Mulungu wako kuchokera pamene unali ku Iguputo.+Palibe Mulungu wina amene unkamudziwa kupatula ine.Palibenso mpulumutsi wina kupatula ine.+  5  Ine ndinakudziwa uli mʼchipululu,+ mʼdziko la chilala.  6  Iwe unakhuta chifukwa unali ndi zakudya zambiri.+Unakhuta ndipo mtima wako unayamba kunyada. Choncho unandiiwala.+  7  Ine ndidzakhala ngati mkango wamphamvu kwa iwo.+Ngati kambuku amene wabisala mʼmbali mwa njira.  8  Ndidzawaukira ngati chimbalangondo chimene ana ake asowa,Ndipo ndidzawangʼamba pachifuwa, Kumeneko ndidzawadya ngati mkango.Chilombo chakutchire chidzawakhadzulakhadzula.  9  Chidzakuwononga iwe IsiraeliChifukwa chakuti unandisiya ine mthandizi wako. 10  Ndiye ili kuti mfumu yako, kuti ikupulumutse mʼmizinda yako yonse?+Olamulira* ako ali kuti amene unawauza kuti,‘Ndipatseni mfumu ndiponso akalongaʼ?+ 11  Ndinakupatsa mfumu nditakwiya,+Ndipo ndidzaichotsa nditakwiya.+ 12  Zolakwa za Efuraimu zakulungidwa,*Ndipo machimo ake asungidwa. 13  Zowawa ngati za mkazi amene akubereka zidzamugwera. Koma iye ndi mwana wopanda nzeru,Chifukwa nthawi yoti abadwe ikakwana, sadzabwera kuti atuluke. 14  Ine ndidzawombola anthu anga ku mphamvu za Manda.*Ndidzawapulumutsa ku imfa.+ Iwe Imfa amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?+ Iwe Manda, kodi mphamvu yako yowononga ili kuti?+ Koma Efuraimu sindimumvera chisoni. 15  Ngakhale atakula bwino pakati pa bango,Mphepo yakumʼmawa idzabwera, mphepo ya Yehova.Idzabwera kuchokera kuchipululu nʼkuumitsa chitsime chake ndi kasupe wake. Winawake adzawononga chuma chake chonse chamtengo wapatali.+ 16  Samariya adzaimbidwa mlandu+ chifukwa wagalukira Mulungu wake.+ Iwo adzagwetsedwa ndi lupanga.+Ana awo adzaphwanyidwaphwanyidwa.Ndipo akazi awo apakati adzatumbulidwa.”

Mawu a M'munsi

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Oweruza.”
Kapena kuti, “zasungidwa.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.