Hoseya 14:1-9

  • Anapemphedwa kuti abwerere kwa Yehova (1-3)

    • Kutamanda Mulungu ndi pakamwa (2)

  • Aisiraeli osakhulupirika anachiritsidwa (4-9)

14  “Inu Aisiraeli, bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,+Popeza mwapunthwa chifukwa cha zolakwa zanu.   Bwererani kwa Yehova ndi mawu amenewa.Uzani Mulungu kuti, ‘Tikhululukireni zolakwa zathu.+ Landirani zinthu zathu zabwino,Ndipo tidzakutamandani ndi pakamwa pathu+ ngati mmene tingaperekere nsembe kwa inu ana a ngʼombe amphongo.   Dziko la Asuri silidzatipulumutsa.+ Ife sitidzakwera pamahatchi.+Ndipo sitidzauzanso ntchito ya manja athu kuti: “Inu Mulungu wathu!”Chifukwa inu ndi amene mumachitira chifundo mwana wamasiye.’+   Ndidzathetsa kusakhulupirika kwawo.+ Ndidzawakonda mwa kufuna kwanga,+Chifukwa ndasiya kuwakwiyira.+   Ine ndidzakhala ngati mame kwa Isiraeli,Ndipo iye adzaphuka ngati maluwa okongola.Mizu yake idzazama ngati mitengo ya ku Lebanoni.   Nthambi zake zidzatambalala,Ulemerero wake udzakhala ngati wa mtengo wa maolivi.Ndipo fungo lake lonunkhira lidzakhala ngati la mtengo wa ku Lebanoni.   Iwo adzakhalanso mumthunzi wake. Adzadzala mbewu ndipo adzaphuka ngati mpesa.+ Adzatchuka* ngati vinyo wa ku Lebanoni.   Efuraimu adzanena kuti, ‘Mafano alibenso ntchito kwa ine.’+ Ine ndidzamva ndipo ndidzamuyangʼanira.+ Ndidzakhala ngati mtengo wa mkungudza wobiriwira bwino. Ndipo mudzapeza zipatso kwa ine.”   Ndani ali ndi nzeru? Amvetse zinthu zimenezi. Wochenjera ndani? Adziwe zimenezi. Njira za Yehova ndi zowongoka.+Ndipo anthu olungama adzayendamo,Koma olakwa adzapunthwa mʼnjira zimenezo.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Adzakumbukiridwa.”