Hoseya 2:1-23
2 “Uzani azichimwene anu kuti, ‘Ndinu anthu anga.’*+
Ndipo azichemwali anu muwauze kuti, ‘Ndinu akazi osonyezedwa chifundo.’*+
2 Imbani mlandu mayi anu. Aimbeni mlandu.Chifukwa iwowo si mkazi wanga+ ndipo ine si mwamuna wawo.
Mayi anuwo asiye uhule*Komanso asiye kuchita chigololo.*
3 Apo ayi, ndiwavula kuti akhale maliseche ngati tsiku limene anabadwa.Ndiwachititsa kukhala ngati chipululu,Komanso ngati dziko lopanda madzi,Nʼkuwapangitsa kuti afe ndi ludzu.
4 Ana awo sindiwachitira chifundo,Popeza ndi ana obadwa chifukwa cha uhule.*
5 Chifukwa mayi awo amachita uhule.*+
Mayi amene anatenga pakati nʼkuwabereka achita zinthu zochititsa manyazi+ ndipo anena kuti,‘Nditsatira amuna ondikonda kwambiri+Ndiponso amene amandipatsa chakudya ndi madzi,Amandipatsanso zovala za ubweya wa nkhosa, nsalu, mafuta ndi zakumwa.’
6 Choncho nditseka njira yawo ndi mpanda waminga.Ndipo ndiwamangira mpanda wamiyalaKuti asowe podutsa.
7 Mayiyu adzathamangira amuna omukonda kwambiriwo, koma sadzawapeza.+Adzawafunafuna, koma osawapeza.
Ndiyeno adzanena kuti, ‘Ndibwerera kwa mwamuna wanga woyamba,+Chifukwa zinthu zinkandiyendera bwino nthawi imeneyo kusiyana ndi pano.’+
8 Iye sanazindikire kuti ndine amene ndinkamupatsa mbewu,+ vinyo watsopano ndiponso mafuta.Sanazindikirenso kuti ndine amene ndinamupatsa siliva wambiri,Ndiponso golide amene anthu ankamugwiritsa ntchito polambira Baala.+
9 ‘Choncho ndidzatembenuka nʼkulanda mbewu zanga pa nthawi yokolola.Ndidzalandanso vinyo wanga watsopano pa nthawi yopanga vinyo.+Mayiyu ndidzamulandanso zovala zanga za ubweya wa nkhosa ndiponso nsalu zanga zimene amabisira maliseche ake.
10 Ndidzamuvula kuti akhale maliseche amuna omukonda kwambiriwo akuona.Ndipo palibe mwamuna amene adzamupulumutse mʼmanja mwanga.+
11 Ndidzathetsa chisangalalo chake chonse.Ndidzathetsa zikondwerero zake,+ chikondwerero cha masiku amene mwezi watsopano waoneka, cha masabata ndiponso nthawi yake ya zikondwerero.
12 Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi ya mkuyu imene iye wanena kuti:
“Amenewa ndi malipiro amene amuna ondikonda kwambiri anandipatsa.”Koma ine mitengoyo ndidzaisandutsa kukhala nkhalango,Ndipo zilombo zakutchire zidzaidya.
13 Ndidzamuimba mlandu chifukwa cha masiku amene anapereka nsembe kwa zifaniziro za Baala.+Pamene ankavala mphete* ndi zinthu zina zodzikongoletsera ndipo ankatsatira amuna omukonda kwambiri.Koma ine anandiiwala,’+ watero Yehova.
14 ‘Choncho ndidzamunyengerera,Ndidzamupititsa kuchipululu,Ndipo ndidzalankhula naye momufika pamtima.
15 Kuyambira nthawi imeneyo kupita mʼtsogolo ndidzamubwezera minda yake ya mpesa.+Ndidzamupatsanso chigwa cha Akori+ kuti chikhale ngati khomo lachiyembekezo.Kumeneko adzayankha ngati mmene ankayankhira ali mtsikana,Ngatinso pa tsiku limene anatuluka mʼdziko la Iguputo.’+
16 Yehova wanena kuti,‘Pa tsiku limenelo adzanditchula kuti Mwamuna wanga ndipo sadzanditchulanso kuti Mbuyanga.*
17 Sindidzamulola kutchulanso mayina a zifaniziro za Baala,+Ndipo sadzakumbukiranso mayina awo.+
18 Pa tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi zilombo zakutchire mʼmalo mwa anthu anga,+Komanso ndi mbalame zouluka mumlengalenga ndi zinthu zokwawa panthaka.+Ndidzathyola uta ndi lupanga ndipo ndidzathetsa nkhondo mʼdzikolo.+Ndipo ndidzachititsa kuti azikhala mwamtendere.+
19 Ndidzalonjeza kukukwatira kuti ukhale wanga mpaka kalekale.Ndidzalonjeza kukukwatira motsatira chilungamo,Komanso chifukwa cha chikondi chokhulupirika ndi chifundo changa.+
20 Ndidzalonjeza kukukwatira nʼkukhala wokhulupirikaNdipo udzadziwadi Yehova.’+
21 Yehova wanena kuti: ‘Pa tsiku limenelo ndidzakuyankha.Ndidzayankha zopempha zakumwambaNdipo kumwambako kudzayankha zopempha za dziko lapansi.+
22 Ndiyeno dziko lapansi lidzayankha mbewu, vinyo watsopano ndi mafuta,Ndipo zimenezi zidzayankha Yezereeli.*+
23 Mayiyu ndidzamudzala ngati mbewu zanga padziko lapansi.+Ndidzachitira chifundo amene sanasonyezedwe chifundo.*Ndipo ndidzauza anthu amene si anthu anga kuti: “Ndinu anthu anga,”*+
Iwo adzayankha kuti: “Inu ndinu Mulungu wathu.”’”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “chiwerewere.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “achotse zochita zake zachigololo pakati pa mabere ake.”
^ Kapena kuti, “chiwerewere.”
^ Kapena kuti, “chiwerewere.”
^ Nʼkuthekanso kuti zinali ndolo zovala pamphuno kapena pakhutu.
^ Kapena kuti, “Baala wanga.”
^ Kutanthauza “Mulungu Adzadzala Mbewu.”