Hoseya 3:1-5

  • Hoseya anagula mkazi wake wachigololo (1-3)

  • Aisiraeli adzabwerera kwa Yehova (4, 5)

3  Kenako Yehova anandiuza kuti: “Pita ukayambenso kukonda mkazi amene akukondedwa ndi mwamuna wina ndipo akuchita chigololo.+ Ukamukonde ngati mmene Yehova amakondera Aisiraeli,+ ngakhale kuti iwo amalambira milungu ina+ komanso amakonda makeke a mphesa.”*  Choncho ndinagula mkaziyo ndi ndalama zasiliva 15 ndiponso balere wokwana muyezo umodzi ndi hafu wa homeri.*  Ndiyeno ndinamuuza kuti: “Ukhala wanga masiku ambiri. Usachite uhule* ndipo usagone ndi mwamuna wina. Inenso sindigona nawe.”  Ziyenera kukhala choncho chifukwa chakuti kwa nthawi yaitali Aisiraeli adzakhala opanda mfumu,+ kalonga, nsembe, chipilala chopatulika, efodi+ ndi zifaniziro za aterafi.*+  Kenako Aisiraeli adzabwerera nʼkuyamba kufunafuna Yehova Mulungu wawo+ ndi Davide mfumu yawo.+ Iwo adzabwera kwa Yehova akunjenjemera ndipo adzafunafuna ubwino wake mʼmasiku otsiriza.+

Mawu a M'munsi

Amenewa ndi makeke amene ankawagwiritsa ntchito polambira milungu yabodza.
Homeri imodzi inali yofanana ndi malita 220. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “chiwerewere.”
Kapena kuti, “milungu ya banja; mafano.”