Hoseya 4:1-19

  • Yehova anali ndi mlandu woti aimbe Aisiraeli (1-8)

    • Panalibe amene ankadziwa Mulungu mʼdzikolo (1)

  • Aisiraeli ankalambira mafano komanso kuchita chiwerewere (9-19)

    • Mtima wachiwerewere unawasocheretsa (12)

4  Tamverani mawu a Yehova inu Aisiraeli.Yehova ali ndi mlandu ndi anthu amʼdzikoli,+Chifukwa mʼdzikoli mulibe choonadi, chikondi chokhulupirika ndipo anthu ake sadziwa Mulungu.+  2  Kulumbira monama, bodza,+ kuphana,+Kuba ndi chigololo+ zafala mʼdzikoli.Ndipo kukhetsa magazi kukuchitika pafupipafupi.+  3  Nʼchifukwa chake dzikoli lidzalira maliro,+Ndipo aliyense wokhala mmenemo adzalefukiratu.Nyama zakutchire ndi mbalame zamumlengalenga,Ngakhalenso nsomba zamʼnyanja, zidzafa.  4  “Komabe, munthu asakutsutseni kapena kukudzudzulani,+Chifukwa muli ngati anthu otsutsana ndi wansembe.+  5  Choncho mudzapunthwa masanasana.Ndipo mneneri adzapunthwa nanu limodzi ngati kuti ndi usiku. Komanso mayi anu ndidzawakhalitsa chete.*  6  Anthu anga adzakhalitsidwa chete* chifukwa cha kusadziwa. Popeza iwo akana kundidziwa,+Inenso ndidzawakana kuti asamanditumikire ngati wansembe wanga.Komanso chifukwa chakuti iwo aiwala lamulo* la ine Mulungu wawo,+Inenso ndidzaiwala ana awo.  7  Pamene akuchuluka, mʼpamenenso akundichimwira kwambiri.+ Ndidzasintha ulemerero wawo nʼkukhala kunyozeka.*  8  Iwo akupindula mwadyera ndi machimo a anthu anga,Ndipo amalakalaka mwadyera machimo a anthuwo.  9  Zimene zidzachitikire anthuwo zidzachitikiranso ansembe.Onse ndidzawaimba mlandu chifukwa cha njira zawo,Ndipo ndidzachititsa kuti zotsatira za zochita zawo ziwabwerere.+ 10  Iwo adzadya, koma sadzakhuta.+ Adzachita zachiwerewere, koma sadzachulukana,+Chifukwa chakuti sakumvera Yehova. 11  Chiwerewere, vinyo wakale ndiponso vinyo watsopanoZimalepheretsa munthu kuchita zoyenera.+ 12  Anthu anga amafunsira kwa mafano awo amtengo,Ndipo amachita zimene ndodo yawo* yawauza.Chifukwa chakuti mtima wachiwerewere umawasocheretsa,Ndiponso chifukwa cha chiwerewere chawocho, amakana kugonjera Mulungu wawo. 13  Iwo amapereka nsembe pamwamba pa mapiri akuluakulu,+Ndipo amapereka nsembe zautsi pamapiri angʼonoangʼono.Amachitanso zimenezi pansi pa mitengo yokhala ndi nthambi zambiri ndi masamba ambiri, pansi pa mitengo ya mlanje ndiponso pa mtengo uliwonse waukulu,+ Chifukwa mitengo imeneyi imakhala ndi mthunzi wabwino.Nʼchifukwa chake ana anu aakazi amachita uhule Ndipo akazi a ana anu amachita chigololo. 14  Sindidzaimba mlandu ana anu aakazi chifukwa cha chiwerewere chawo,Komanso akazi a ana anu chifukwa cha chigololo chawo. Chifukwa amuna akuyenda ndi mahuleNdipo amapereka nsembe limodzi ndi mahule apakachisi.Anthu osamvetsa zinthu amenewa+ adzawonongedwa. 15  Ngakhale kuti inu Aisiraeli mukuchita chiwerewere,+Yuda asakhale ndi mlandu.+ Musabwere ku Giligala+ kapena ku Beti-aveni,+Ndipo musalumbire kuti, ‘Mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo!’+ 16  Isiraeli wakhala wamakani ngati ngʼombe yomwe ikuchita makani.+ Ndiye kodi Yehova adzawaweta ngati nkhosa yamphongo yaingʼono pamalo odyetsera ziweto? 17  Efuraimu wagwirizana ndi mafano.+ Musiyeni aona! 18  Mowa* wawo ukatha,Amayamba kuchita zachiwerewere. Ndipo atsogoleri awo amakonda kwambiri zinthu zochititsa manyazi.+ 19  Mphepo idzawakulunga mʼmapiko ake,Ndipo adzachita manyazi ndi nsembe zawo.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndidzawawononga.”
Kapena kuti, “adzawonongedwa.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Mabaibulo ena amati, “Asintha ulemerero wanga nʼkukhala kunyozeka.”
Kapena kuti, “ndodo ya munthu wamatsenga.”
Kapena kuti, “Mowa wamasese.”