Hoseya 5:1-15
-
Chiweruzo cha Efuraimu ndi Yuda (1-15)
5 “Tamvani izi inu ansembe,+Ndipo mvetserani inu a mʼnyumba ya Isiraeli.Inunso a mʼnyumba ya mfumu mvetserani,Popeza chiweruzochi chikukhudza inuyo,Chifukwa mwakhala msampha ku MizipaNdiponso ngati ukonde paphiri la Tabori.+
2 Anthu amene andipandukira apha anthu ambiri,Ndipo ine ndikuwachenjeza onsewo.
3 Inetu ndimamudziwa bwino Efuraimu,Ndipo Isiraeli si wobisika kwa ine.
Iwe Efuraimu wachita zachiwerewere,Ndipo Isiraeli wadziipitsa.+
4 Zochita zawo zikuwalepheretsa kubwerera kwa Mulungu wawo,Chifukwa iwo ali ndi mtima wachiwerewere+Ndipo akana kuzindikira kuti ine Yehova ndine Mulungu wawo.
5 Kunyada kwa Isiraeli kwakhala umboni womutsutsa,+Ndipo Isiraeli ndi Efuraimu apunthwa ndi zolakwa zawo.Nayenso Yuda wapunthwa nawo limodzi.+
6 Iwo anapita kukafunafuna Yehova ali ndi nkhosa ndiponso ngʼombe zawo,Koma sanamupeze.
Chifukwa anali atawachokera.+
7 Akhala osakhulupirika kwa Yehova,+Chifukwa abereka ana achilendo.
Tsopano mwezi udzawadya* limodzi ndi zinthu zawo.*
8 Lizani lipenga la nyanga ya nkhosa+ ku Gibeya ndi lipenga ku Rama!+
Fuulani mfuu ya nkhondo ku Beti-aveni:+ Tsogola iwe Benjamini!
9 Iwe Efuraimu, udzakhala chinthu choopsa pa tsiku limene udzalangidwe.+
Inetu ndauza mafuko a Isiraeli zinthu zimene zidzawachitikiredi.
10 Akalonga a Yuda ali ngati anthu osuntha malire.+
Ndidzawakhuthulira mkwiyo wanga ngati madzi.
11 Efuraimu waponderezedwa ndi chiweruzo,Chifukwa anatsimikiza mtima kutsatira mdani wake.+
12 Choncho ndinali ngati njenjete* kwa Efuraimu,Ndipo ndinachititsa kuti nyumba ya Yuda iwole.
13 Efuraimu ataona matenda ake ndiponso Yuda ataona chilonda chake,Efuraimu anapita ku Asuri+ komanso anatumiza anthu kwa mfumu yaikulu.
Koma mfumuyo sinathe kukuchiritsani.Ndipo sinathe kupoletsa chilonda chanu.
14 Ine ndidzakhala ngati mkango wamphamvu kwa Efuraimu,Ndiponso ngati mkango wamphamvu kwa anthu a mʼnyumba ya Yuda.
Ineyo ndidzawakhadzulakhadzula nʼkuchoka.+Ndidzawatenga nʼkukawataya ndipo palibe adzawalanditse.+
15 Kenako ndidzabwerera kumalo anga mpaka iwo atakumana ndi zotsatira za zolakwa zawo,Ndipo adzayamba kundifunafuna kuti ndiwakomere mtima.+
Akadzakumana ndi mavuto, adzandifuna.”+