Hoseya 6:1-11

  • Anawauza kuti abwerere kwa Yehova (1-3)

  • Anthu anasonyeza chikondi chokhulupirika chosakhalitsa (4-6)

    • Chikondi chokhulupirika chimaposa nsembe (6)

  • Anthu anali ndi khalidwe lochititsa manyazi (7-11)

6  “Bwerani, tiyeni tibwerere kwa Yehova,Chifukwa iye watikhadzulakhadzula,+ koma adzatichiritsa. Wativulaza, koma adzamanga mabala athu.   Iye adzatithandiza kuti titsitsimuke pakatha masiku awiri. Pa tsiku lachitatu adzatidzutsa,Ndipo tidzakhalanso ndi moyo pamaso pake.   Ife tidzamudziwa Yehova ndipo tidzayesetsa kuti timudziwe bwino. Nʼzosakayikitsa kuti adzatulukira ngati mmene mʼbandakucha umafikira.Adzabwera kwa ife ngati mvula yambiri,Ngati mvula yomalizira imene imanyowetsa kwambiri nthaka.”   “Kodi ndikuchite chiyani iwe Efuraimu? Nanga iwe Yuda, ndikuchite chiyani? Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika chili ngati mitambo yamʼmawa,Ndiponso ngati mame amene sachedwa kuuma.   Nʼchifukwa chake anthu amenewa ndidzawadula pogwiritsa ntchito aneneri.+Ndidzawapha ndi mawu amʼkamwa mwanga.+ Chiweruzo chimene mudzalandire chidzakhala ngati kuwala.+   Chifukwa ndimakondwera ndi chikondi chokhulupirika,* osati nsembe.Ndimakondweranso ndi kudziwa Mulungu, osati nsembe zopsereza zathunthu.+   Koma iwo, mofanana ndi anthu wamba, aphwanya pangano.+ Kumeneko andichitira zosakhulupirika.   Giliyadi ndi tauni ya anthu ochita zoipa,+Yodzaza ndi zidindo za mapazi amagazi.+   Gulu la ansembe lili ngati gulu la achifwamba lobisalira munthu panjira. Amapha anthu mumsewu ku Sekemu+Chifukwa khalidwe lawo ndi lochititsa manyazi. 10  Ndaona zinthu zonyansa kwambiri mʼnyumba ya Isiraeli. Efuraimu akuchita zachiwerewere mmenemo.+Isiraeli wadziipitsa.+ 11  Komanso, inu anthu a ku Yuda, nthawi yoti mukololedwe yakhazikitsidwa.Ine ndidzasonkhanitsanso anthu anga amene anatengedwa kupita kudziko lina.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “chifundo.”