Hoseya 7:1-16

  • Zoipa za Efuraimu (1-16)

    • Sangathawe ukonde wa Mulungu (12)

7  “Nthawi zonse ndikafuna kuchiritsa Isiraeli,Zolakwa za Efuraimu zimaonekera,+Ndiponso zoipa za Samariya.+ Chifukwa iwo amachita zachinyengo.+Anthu akuba amathyola nyumba ndipo gulu la achifwamba limasakaza panja.+   Koma mumtima mwawo saganiza nʼkomwe kuti ndidzakumbukira zoipa zawo zonse.+ Tsopano zochita zawo zawazungulira.Ndipo zili pamaso panga.   Iwo amasangalatsa mfumu ndi zoipa zawo.Ndiponso amasangalatsa akalonga ndi chinyengo chawo.   Anthu onsewo ndi achigololo.Ali ngati uvuni imene wophika mkate wayatsa.Ndipo wasiya kuisonkhezera pamene akudikira kuti ufa umene wakanda ufufume.   Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu, akalonga adwala.Ndipo ali ndi ukali chifukwa cha vinyo.+ Mfumuyo yatambasulira dzanja lake anthu onyoza.   Chifukwa anthuwo afika ndi mitima yoyaka ngati uvuni.* Wophika mkate amagona usiku wonse.Mʼmawa uvuniwo umayaka moto walawilawi.   Onsewo akutentha ngati uvuni wamoto,Ndipo amameza atsogoleri* awo. Mafumu awo onse agwa.+Palibe aliyense amene akundiitana.+   Efuraimu amagwirizana ndi anthu a mitundu ina.+ Iye ali ngati mkate wozungulira wopsa mbali imodzi yokha.   Alendo alanda mphamvu zake,+ koma iye sakudziwa. Ndipo mʼmutu mwake monse muli imvi, koma iye sakudziwa. 10  Kunyada kwa Aisiraeli kwakhala umboni wowatsutsa,+Koma iwo sanabwerere kwa Yehova Mulungu wawo.+Ndiponso sanamufunefune ngakhale kuti pali zonsezi. 11  Anthu a ku Efuraimu ali ngati nkhunda yopusa, yopanda nzeru.+ Iwo apempha thandizo ku Iguputo+ ndiponso apita kudziko la Asuri.+ 12  Kulikonse kumene iwo angapite, ndidzawatchera ukonde. Ndidzawagwira ngati mbalame zouluka mumlengalenga. Ndidzawalanga mogwirizana ndi chenjezo limene ndinkawauza ndikawasonkhanitsa.+ 13  Tsoka kwa iwo chifukwa andithawa! Adzawonongedwa chifukwa andilakwira. Ndinali wokonzeka kuwawombola, koma andinamizira mabodza.+ 14  Sanapemphe ndi mtima wonse kuti ndiwathandize,+Ngakhale kuti ankalira mofuula ali pamabedi awo. Ankadzicheka kuti apeze chakudya ndi vinyo watsopano.Iwo anditembenukira. 15  Ngakhale kuti ndinawalangiza ndiponso kulimbitsa manja awo,Akunditsutsa ndipo akukonza chiwembu. 16  Anabwerera, koma sanapite kuchipembedzo choona.Anakhala osadalirika ngati uta wosakungika.+ Akalonga awo adzaphedwa ndi lupanga chifukwa cha malilime awo amwano. Nʼchifukwa chake iwo adzanyozedwa mʼdziko la Iguputo.”+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “Chifukwa mitima yawo ili ngati uvuni pamene akufika ndi mapulani awo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “oweruza.”