Hoseya 8:1-14

  • Zotsatira za kulambira mafano (1-14)

    • Kufesa mphepo, kukolola mphepo yamkuntho (7)

    • Aisiraeli anaiwala amene anawapanga (14)

8  “Ika lipenga la nyanga ya nkhosa pakamwa pako.+ Mdani akubwera ngati chiwombankhanga kudzaukira nyumba ya Yehova.+Chifukwa Aisiraeli aphwanya pangano langa+ ndiponso sanatsatire malamulo anga.+   Iwo akundilirira kuti, ‘Inu Mulungu wathu, ife Aisiraeli tikukudziwani!’+   Aisiraeli akana kuchita zabwino,+ Choncho mdani awathamangitse.   Iwo asankha mafumu, koma osati mwa kufuna kwanga. Asankha akalonga, popanda ine kuvomereza. Pogwiritsa ntchito siliva ndi golide wawo apanga mafano,+Ndipo zimenezi zidzawawonongetsa.+   Iwe Samariya, fano lako la mwana wa ngʼombe lakanidwa.+ Ndakwiyira kwambiri anthu ako.+ Kodi iwo adzalephera kukhala osalakwa mpaka liti?   Zimenezi zachokera ku Isiraeli. Mmisiri ndi amene anapanga fano limeneli, ndipo fanoli si Mulungu.Fano la ku Samariya lidzangokhala ngati nkhuni zowazawaza.   Iwo akungofesa mphepo,Ndipo adzakolola mphepo yamkuntho.+ Mbewu zawo sizidzakula mpaka kukhwima.+Ndipo zimene zidzakule, sizidzawapatsa ufa. Ngati zina zingabereke, alendo adzazimeza.+   Aisiraeli adzamezedwa.+ Moti adzakhala pakati pa anthu a mitundu ina,+Ngati chiwiya chosafunika.   Iwo akafika mpaka kudziko la Asuri+ ngati bulu wamʼtchire. Efuraimu walipira akazi kuti azigona nawo.+ 10  Ngakhale kuti akulipira akazi a mitundu ina,Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi.Adzayamba kuvutika+ chifukwa choponderezedwa ndi mafumu ndiponso akalonga. 11  Efuraimu wapanga maguwa ansembe ambiri ndipo wachimwa.+ Akugwiritsa ntchito maguwa akewa kuti azichimwa.+ 12  Ndinamulembera zinthu zambiri zokhudza malamulo* anga,Koma anangoziona ngati zachilendo.+ 13  Iwo amapereka nsembe kwa ine ndipo amadya nyama yake,Koma ine Yehova sindikondwera nazo.+ Tsopano ndidzakumbukira zolakwa zawo ndipo ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo.+ Iwo anabwerera* ku Iguputo.+ 14  Isiraeli anaiwala amene anamupanga+ ndipo wamanga akachisi.+Yuda nayenso wamanga mizinda yambiri yokhala ndi mipanda yolimba.+ Koma ine ndidzatumiza moto mʼmizinda yakeNdipo udzawotcha nsanja zamumzinda uliwonse.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malangizo.”
Mabaibulo ena amati, “adzabwerera.”