Levitiko 1:1-17

  • Nsembe yopsereza (1-17)

1  Yehova anaitana Mose kuchokera mʼchihema chokumanako,+ nʼkumuuza kuti:  “Uza Aisiraeli* kuti, ‘Ngati munthu aliyense akufuna kupereka chiweto kwa Yehova kuti ikhale nsembe, azipereka ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi.+  Ngati akupereka ngʼombe kuti ikhale nsembe yake yopsereza, azipereka yamphongo, yopanda chilema.+ Aziipereka kwa Yehova mwa kufuna kwake,+ pakhomo la chihema chokumanako.  Iye aziika dzanja lake pamutu pa nsembe yopserezayo ndipo idzalandiridwa kuti iphimbe machimo ake.  Kenako azipha ngʼombe yaingʼono pamaso pa Yehova. Ndiyeno ana a Aroni ansembe,+ azibweretsa magazi ake nʼkuwawaza mbali zonse za guwa lansembe,+ limene lili pakhomo la chihema chokumanako.  Nyama ya nsembe yopserezayo aziisenda nʼkuiduladula.+  Ana a Aroni, ansembe, aziika moto paguwa lansembelo+ nʼkuyalapo nkhuni.  Ndiyeno ana a Aroni ansembe, aziyala nyama yoduladulayo+ pankhuni zimene zili pamoto wapaguwa lansembepo. Aziyala nyamayo pamodzi ndi mutu ndiponso mafuta.*  Matumbo ake ndi ziboda zake azizitsuka ndi madzi. Akatero wansembe aziwotcha nyama yonse kuti paguwa lansembe pakhale utsi, ndipo ikhale nsembe yopsereza. Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto, yakafungo kosangalatsa* yoperekedwa kwa Yehova.+ 10  Ngati akupereka nkhosa kapena mbuzi+ kuti ikhale nsembe yake yopsereza, azipereka mwana wamphongo wopanda chilema.+ 11  Ndipo aziipha pamaso pa Yehova kumbali yakumpoto ya guwa lansembe. Akatero ana a Aroni ansembe, aziwaza magazi ake mbali zonse za guwa lansembe.+ 12  Kenako nyamayo aziiduladula ndipo azichotsa mafuta ake* ndi mutu wake. Akatero wansembe aziyala nyama yoduladulayo pankhuni zimene zili pamoto wapaguwa lansembe. 13  Ndiyeno azitsuka matumbo komanso ziboda ndi madzi. Kenako wansembe aziwotcha nyama yonse kuti paguwa lansembe pakhale utsi, ndipo ikhale nsembe yopsereza. Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* yoperekedwa kwa Yehova. 14  Koma ngati akupereka mbalame kuti ikhale nsembe yake yopsereza yoperekedwa kwa Yehova, azipereka njiwa kapena ana a nkhunda.+ 15  Wansembe azibweretsa mbalameyo paguwa lansembe nʼkudula* mutu wake. Akatero aziiwotcha paguwa lansembe kuti pakhale utsi, koma magazi ake aziwakhetsera pansi pambali pa guwa lansembelo. 16  Azichotsa chithokomiro ndi nthenga zake nʼkuziponya potayira phulusa,*+ chakumʼmawa, pafupi ndi guwa lansembe. 17  Ndiyeno aziingʼamba pakati chamʼmapiko mwake, koma osailekanitsa. Kenako wansembe aziiwotcha paguwa lansembe pamwamba pa nkhuni zimene zili pamoto kuti pakhale utsi. Imeneyi ndi nsembe yopsereza, nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* yoperekedwa kwa Yehova.’”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”
Kapena kuti, “mafuta okuta impso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “mafuta ake okuta impso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
“Kudula” kumeneku ankadula ndi zikhadabo ndipo sankachotseratu mutu.
Kapena kuti, “phulusa lamafuta,” kutanthauza phulusa losakanikirana ndi mafuta a nsembe.
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”