Levitiko 10:1-20

  • Moto wochokera kwa Yehova unapha Nadabu ndi Abihu (1-7)

  • Malamulo opita kwa ansembe okhudza kumwa ndi kudya (8-20)

10  Ndiyeno Nadabu ndi Abihu,+ omwe ndi ana a Aroni, aliyense anatenga chofukizira, nʼkuikamo moto ndi zofukiza+ pamwamba pake. Atatero anayamba kupereka zofukiza pamoto wosaloledwa+ ndi Yehova, umene iye sanawalamule.  Choncho moto unatsika kuchokera kwa Yehova nʼkuwawotcha,+ moti anafa pamaso pa Yehova.+  Kenako Mose anauza Aroni kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Anthu amene ali pafupi ndi ine+ azikumbukira kuti ndine woyera, ndipo anthu onse adzandipatsa ulemerero.’” Koma Aroni anangokhala chete.  Zitatero, Mose anaitana Misayeli ndi Elizafana, ana a Uziyeli,+ bambo aangʼono a Aroni, nʼkuwauza kuti: “Bwerani muchotse abale anu patsogolo pa malo oyera, mupite nawo kunja kwa msasa.”  Iwo anabweradi nʼkuwanyamula osawavula mikanjo yawo ndipo anapita nawo kunja kwa msasa, mogwirizana ndi zimene Mose ananena.  Atatero Mose anauza Aroni ndi ana ake ena, Eleazara ndi Itamara kuti: “Musasiye tsitsi lanu osalisamala kapena kungʼamba zovala zanu+ kuti mungafe ndiponso kuti Mulungu angakwiyire gulu lonseli. Abale anu omwe ndi nyumba yonse ya Isiraeli ndi amene alire anthu amene Yehova wawapha ndi moto.  Musachoke pakhomo la chihema chokumanako kuopera kuti mungafe, chifukwa mwadzozedwa ndi mafuta odzozera a Yehova.”+ Choncho iwo anachita mogwirizana ndi zimene Mose ananena.  Kenako Yehova anauza Aroni kuti:  “Mukamabwera kuchihema chokumanako, iwe ndi ana ako musamamwe vinyo kapena zakumwa zina zoledzeretsa,+ kuti mungafe. Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale. 10  Mukamachita zimenezi mudzatha kusiyanitsa pakati pa chinthu chopatulika ndi choipitsidwa ndiponso pakati pa chodetsedwa ndi choyera.+ 11  Komanso mudzatha kuphunzitsa Aisiraeli malamulo onse amene Yehova wanena kwa iwo kudzera mwa Mose.”+ 12  Ndiyeno Mose analankhula ndi Aroni komanso Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni amene anatsala kuti: “Tengani nsembe yambewu imene yatsala pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova, ndipo muidye yopanda zofufumitsa pafupi ndi guwa lansembe,+ chifukwa nsembeyo ndi yopatulika koposa.+ 13  Mudye nsembeyo mʼmalo oyera,+ chifukwa ndi gawo lanu komanso ndi gawo la ana anu kuchokera pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova. Zimenezi nʼzimene ndalamulidwa. 14  Mudyenso chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku ndi mwendo wa gawo lopatulika.+ Muzidyere pamalo amene ayeretsedwa, inuyo, ana anu aamuna ndi ana anu aakazi.+ Muzichita zimenezi chifukwa zinthu zimenezi zaperekedwa kwa inu monga gawo lanu ndi gawo la ana anu kuchokera pa nsembe zamgwirizano za Aisiraeli. 15  Iwo azibweretsa mwendo wa gawo lopatulika ndi chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku, pamodzi ndi mafuta a nsembe zowotcha pamoto, kuti woperekayo aziyendetse uku ndi uku pamaso pa Yehova. Zimenezi zizikhala gawo lanu ndi gawo la ana anu mpaka kalekale,+ mogwirizana ndi zimene Yehova walamula.” 16  Ndiyeno Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yamachimo,+ koma anaona kuti yonse inali itawotchedwa pamoto. Choncho iye anakwiyira Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni amene anatsala, ndipo anati: 17  “Nʼchifukwa chiyani simunadye nsembe yamachimo mʼmalo oyera?+ Nsembe imeneyi ndi yopatulika koposa, ndipo Mulungu wakupatsani kuti munyamule zolakwa za gulu lonse, ndi kuphimba machimo a gulu lonseli pamaso pa Yehova. 18  Taonani, simunabweretse magazi ake mkati, mʼmalo oyera.+ Munafunika kudya nsembeyo mʼmalo oyera, mogwirizana ndi zimene Mulungu anandilamula.” 19  Aroni anayankha Mose kuti: “Lero apereka nsembe yawo yamachimo ndi nsembe yawo yopsereza kwa Yehova,+ komabe zinthu izi zandigwera. Ndiye ndikanati ndadya nsembe yamachimo lero, kodi Yehova zikanamusangalatsa?” 20  Mose atamva zimenezi, anakhutira.

Mawu a M'munsi