Levitiko 12:1-8

  • Kudziyeretsa pambuyo pobereka mwana (1-8)

12  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:  “Uza Aisiraeli kuti, ‘Mkazi akakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna, azikhala wodetsedwa kwa masiku 7. Azikhala wodetsedwa ngati mmene amakhalira pa nthawi imene akusamba.+  Pa tsiku la 8, mwanayo azidulidwa.+  Mkaziyo azipitiriza kudziyeretsa ku magazi ake kwa masiku enanso 33. Asamakhudze chilichonse chopatulika komanso asamalowe mʼmalo oyera mpaka atakwanitsa masiku a kuyeretsedwa kwake.  Akabereka mwana wamkazi, azikhala wodetsedwa kwa masiku 14 ngati mmene amakhalira pa nthawi imene akusamba. Mkaziyo azipitiriza kudziyeretsa ku magazi ake kwa masiku enanso 66.  Masiku a kuyeretsedwa kwake chifukwa chobereka mwana wamwamuna kapena wamkazi akakwana, azibweretsa kwa wansembe, pakhomo la chihema chokumanako, nkhosa yaingʼono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopsereza.+ Azibweretsanso mwana wa nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yamachimo.  Wansembeyo aziipereka kwa Yehova ndi kumʼphimbira machimo ndipo mkaziyo adzakhala woyera pa kukha magazi kwake. Limeneli ndi lamulo lokhudza mkazi amene wabereka mwana wamwamuna kapena wamkazi.  Koma ngati sangakwanitse kupeza nkhosa, azipereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.+ Mbalame imodzi izikhala ya nsembe yopsereza, inayo izikhala ya nsembe yamachimo. Akatero wansembe adzamuphimbira machimo ndipo mkaziyo adzakhala woyera.’”

Mawu a M'munsi