Levitiko 13:1-59

  • Malamulo okhudza khate (1-46)

  • Khate lapachovala (47-59)

13  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose ndi Aroni kuti:  “Munthu akatuluka chotupa, kapena nkhanambo,* kapena chikanga, moti ingathe kukhala nthenda ya khate*+ pakhungu lake, azibwera naye kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ake omwenso ndi ansembe.+  Wansembeyo aziona nthenda imene yatuluka pakhunguyo. Ngati cheya chapamalopo chasanduka choyera ndipo pakuoneka kuti nthendayo yalowa mpaka mkati mwa khungu, ndiye kuti limenelo ndi khate. Wansembe aziona nthendayo nʼkugamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa.  Koma ngati chikangacho chikuoneka choyera ndipo sichinalowe mkati mwa khungu, komanso cheya sichinasanduke choyera, wansembe azimuika munthuyo kwayekha kwa masiku 7.+  Ndiyeno wansembe azionanso munthuyo pa tsiku la 7, ndipo ngati nthendayo ikuoneka kuti yatha, moti sinafalikire pakhungu, wansembe azimuika munthuyo kwayekha kwa masiku enanso 7.  Wansembe azionanso munthuyo kachiwiri pa tsiku la 7. Ngati nthendayo yatheratu ndipo sinafalikire pakhungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera.+ Inangokhala nkhanambo basi. Kenako munthuyo azichapa zovala zake nʼkukhala woyera.  Koma ngati nkhanambo yafalikira pakhungu la munthu pambuyo poti anaonekera kwa wansembe ndipo anagamula kuti ndi woyera, munthuyo azikaonekeranso kachiwiri kwa wansembe.  Wansembe azionanso munthuyo ndipo ngati nkhanambo yake yafalikira pakhungu, wansembeyo azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate.+  Munthu akagwidwa ndi nthenda ya khate, azimubweretsa kwa wansembe. 10  Wansembe azimuona+ ndipo ngati pakhungupo pali chotupa moti khungu ndi cheya zayera, ndipo pachotupapo pali chilonda,+ 11  limenelo ndi khate lokhalitsa pakhungu lake, ndipo wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Asamuike kwayekha*+ chifukwa ndi wodetsedwa. 12  Koma ngati khate layamba pakhungu lake, moti wansembe akuchita kuoneratu kuti lafalikira pathupi lonse la munthuyo, kuyambira kumutu mpaka kumapazi, 13  ndipo wansembe wamuona, nʼkutsimikizira kuti khatelo lafalikiradi thupi lonse, pamenepo azigamula kuti munthuyo ndi woyera.* Khungu lake lonse latuwa, choncho ndi woyera. 14  Koma akadzatuluka zilonda, ndiye kuti adzakhala wodetsedwa. 15  Wansembe akaona zilondazo, azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa+ chifukwa cha zilondazo. Limenelo ndi khate.+ 16  Koma ngati zilondazo zasandukanso zoyera, munthuyo azibwera kwa wansembe. 17  Ndiyeno wansembe azimuona+ ndipo ngati khungu lake latuwa, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera. 18  Ngati munthu anali ndi chithupsa pakhungu lake, ndiye kenako chapola, 19  koma pamene panali chithupsapo patuluka chotupa choyera kapena chikanga chotuwa mofiirira, munthuyo azikaonekera kwa wansembe. 20  Wansembe aziona chotupacho.+ Ngati chikuoneka kuti chayambira mkati mwa khungu ndipo cheya chake chasanduka choyera, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate ndipo yatuluka pachithupsacho. 21  Koma wansembe akachiona nʼkupeza kuti palibe cheya choyera ndipo sichinayambire mkati mwa khungu komanso chikuoneka kuti chikutha, wansembe azimuika kwayekha kwa masiku 7.+ 22  Ngati chikangacho chafalikiradi pakhungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda. 23  Koma ngati chikangacho chili pamalo amodzi ndipo sichinafalikire, kumeneko ndi kutukusira kwa chithupsa. Wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera.+ 24  Kapena ngati pakhungu pali bala lamoto, ndipo mnofu wapabalapo wayamba kuoneka wotuwa mofiirira kapena woyera, 25  wansembe aziona balalo. Ngati cheya cha pamalopo chasanduka choyera ndipo balalo likuoneka lozama kuposa khungu, limenelo ndi khate. Latuluka pabala, ndipo wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate. 26  Koma ngati wansembe waona balalo, nʼkupeza kuti palibe cheya choyera ndipo balalo si lozama kuposa khungu komanso likutha, wansembe azimuika kwayekha kwa masiku 7.+ 27  Wansembe aziona munthuyo pa tsiku la 7. Ngati nthendayo yafalikiradi pakhungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate. 28  Koma ngati chikangacho chili pamalo amodzi ndipo sichinafalikire pakhungu komanso chikutha, kumeneko ndi kutupa kwa bala. Wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera chifukwa kumeneko ndi kutukusira kwa bala. 29  Mwamuna kapena mkazi akagwidwa ndi nthenda ina yake pamutu kapena pachibwano, 30  wansembe aziona nthendayo.+ Ngati pamalopo pakuoneka kuti nthendayo yalowa mkati mwa khungu, komanso tsitsi lachita chikasu ndipo lili patalipatali, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya pamutu ndi ndevu. Ndi khate lakumutu kapena kuchibwano. 31  Koma ngati wansembe waona kuti nthendayo sinalowe mkati mwa khungu, ndipo palibe tsitsi lakuda, wansembe aziika munthuyo kwayekha kwa masiku 7.+ 32  Wansembe azionanso nthendayo pa tsiku la 7. Ngati nthendayo sinafalikire, komanso pamalopo sipanamere tsitsi lachikasu ndipo pakuoneka kuti sinalowe mkati mwa khungu, 33  munthuyo azimetedwa tsitsi lake, koma asamamʼmete pamene pali nthendapo. Kenako wansembe azimuika munthuyo kwayekha kwa masiku 7. 34  Pa tsiku la 7 wansembe azionanso nthendayo. Ngati nthenda yapamutu ndi yapandevu sinafalikire pakhungu, ndipo zikuoneka kuti nthendayo sinalowe mkati mwa khungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera. Akatero munthuyo azichapa zovala zake nʼkukhala woyera. 35  Koma ngati nthendayo yafalikiradi pakhungu pambuyo poti munthuyo wagamulidwa kuti ndi woyera, 36  wansembe azionanso munthuyo. Ngati nthendayo yafalikira pakhungu, wansembe sakuyenera kufufuzanso tsitsi lachikasu. Munthuyo ndi wodetsedwa. 37  Koma ngati nthendayo ikuoneka kuti sinafalikire ndipo pamalopo pamera tsitsi lakuda, ndiye kuti nthendayo yatha. Munthuyo ndi woyera ndipo wansembe azigamula kuti ndi woyera.+ 38  Mwamuna kapena mkazi akagwidwa ndi zikanga zotuwa pakhungu lake, 39  wansembe aziziona.+ Ngati zikangazo zayamba kutha, imeneyo ndi nthenda yosaopsa imene yatuluka pakhungu lake. Munthuyo ndi woyera. 40  Mwamuna akayamba kutha tsitsi kumutu nʼkuchita dazi, ndi woyera. 41  Ngati tsitsi latha patsogolo pa mutu wake nʼkuchita dazi, ndi woyera. 42  Koma ngati padazi lake kapena pamphumi pake patuluka chilonda chotuwa mofiirira, limenelo ndi khate, latuluka pamutu pake kapena pamphumi pake. 43  Wansembe aziona munthuyo, ndipo ngati kutupa kwa chilondacho kukuoneka kotuwa mofiirira padazipo kapena pamphumi pake, ndipo zikuoneka ngati pakhungu lakelo pali khate, 44  ameneyo ali ndi khate. Munthuyo ndi wodetsedwa, ndipo wansembe azigamula kuti ndi wodetsedwa chifukwa cha nthenda imene ili pamutu pake. 45  Munthu amene ali ndi khateyo, zovala zake zizingʼambidwa ndipo asamakonze tsitsi lake. Koma aziphimba ndevu zake zapamlomo nʼkumafuula kuti, ‘Wodetsedwa, wodetsedwa!’ 46  Azikhala wodetsedwa pa nthawi yonse imene akudwala nthendayo. Chifukwa chakuti ndi wodetsedwa, azikhala kwayekha. Azikhala kunja kwa msasa.+ 47  Ngati nthenda ya khate yadetsa chovala, kaya chovalacho ndi chaubweya wa nkhosa kapena chansalu, 48  kaya ili mulitali kapena mulifupi* mwa chovala chansalu kapena chaubweya wa nkhosa, kapenanso pachikopa kapena pa chilichonse chopangidwa ndi chikopa, 49  ndipo nthendayo ikuoneka yobiriwira mopitira ku chikasu kapena yofiirira pachovala kapena pachikopa, mulitali kapena mulifupi mwa nsalu, kapena pachinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, imeneyo ndi nthenda ya khate ndipo chinthucho muyenera kukachionetsa kwa wansembe. 50  Wansembe aziona nthendayo, ndipo azisunga chinthucho kwachokha kwa masiku 7.+ 51  Akaona nthendayo pa tsiku la 7 nʼkupeza kuti yafalikira pachovala, mulitali kapena mulifupi, kapena pachikopa (kaya chikopacho amachigwiritsa ntchito yotani), nthendayo ndi khate loopsa ndipo chinthucho nʼchodetsedwa.+ 52  Aziwotcha chovalacho, nsalu ya ubweya wa nkhosa kapena nsalu ina iliyonse, kapena zilizonse zopangidwa ndi chikopa, zimene zagwidwa ndi nthenda ya khateyo, chifukwa khate limenelo ndi loopsa. Ziziwotchedwa pamoto. 53  Koma wansembeyo akaona, nʼkupeza kuti nthendayo sinafalikire pachovalacho, mulitali kapena mulifupi, kapena pa chilichonse chopangidwa ndi chikopa, 54  wansembe azilamula kuti achape chinthu chogwidwa ndi nthendacho ndipo azichisunga kwachokha kwa masiku enanso 7. 55  Wansembe aziona chinthu chimene chili ndi nthendacho, chinthucho chitachapidwa. Ngakhale kuti nthendayo ikuonekabe chimodzimodzi ndipo sinafalikire, chinthucho ndi chodetsedwa. Muzichiwotcha pamoto chifukwa chadyedwa ndi nthendayo kuyambira mkati kapena kuyambira kunja kwake. 56  Koma ngati wansembe waona chinthucho, nʼkupeza kuti nthenda ija yatha chinthucho chitachapidwa, azingʼamba mbali yogwidwa ndi nthendayo pachovalacho kapena pachikopacho. 57  Koma ngati nthendayo ikuonekabe mbali ina ya chovalacho, mulitali kapena mulifupi, kapena pa chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ndiye kuti nthendayo ikufalikira. Chilichonse chimene chagwidwa ndi nthendayi muzichiwotcha pamoto.+ 58  Koma ngati nthendayo yatha mutachapa chovalacho kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, muzichichapanso kachiwiri, ndipo chidzakhala choyera. 59  Limeneli ndi lamulo lokhudza nthenda ya khate yopezeka pachovala chaubweya wa nkhosa kapena chansalu, mulitali kapena mulifupi, kapena pachinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, kuti wansembe adziwe chinthu choyenera kugamula kuti nʼchoyera kapena nʼchodetsedwa.”

Mawu a M'munsi

Amenewa ndi matenda amene amachititsa kuti khungu liume nʼkumakanganuka ngati mmene zimakhalira bala likamapola.
Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “khate” amatanthauza zambiri kuphatikizapo matenda apakhungu osiyanasiyana opatsirana. Angaphatikizenso matenda ena opezeka mʼzovala ndi mʼnyumba.
Sankafunikanso kumuika kwayekha kwa masiku 7 ngati mmene ankachitira nthawi zonse, kuti atsimikizire ngati ali ndi khate kapena ayi, chifukwa zinali zodziwikiratu kuti munthuyo ali ndi khate.
Kapena kuti, “azigamula kuti nthendayo sangapatsire ena.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ili mu ulusi wowombera nsalu woyenda mulitali kapena mulifupi.”