Levitiko 15:1-33

  • Kudetsedwa chifukwa cha kukha kumaliseche (1-33)

15  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose ndi Aroni kuti:  “Uza Aisiraeli kuti, ‘Ngati mwamuna ali ndi nthenda ya kukha kumaliseche, nthenda yakeyo ikumupangitsa kukhala wodetsedwa.+  Iye ndi wodetsedwa chifukwa cha zimene zikukhazo, kaya zinthuzo zikupitirizabe kutuluka kapena maliseche ake atsekeka ndi zimene zikukhazo, azikhalabe wodetsedwa.  Bedi lililonse limene munthu amene akukhayo angagonepo lizikhala lodetsedwa, ndipo chilichonse chimene angakhalepo chizikhala chodetsedwa.  Munthu amene wakhudza bedi lakelo azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+  Aliyense wokhala pachinthu chimene munthu amene akukhayo anakhalapo, azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.  Aliyense wokhudza thupi la munthu amene akukhayo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.  Ngati amene akukhayo walavulira munthu woyera, munthuyo azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.  Chishalo chilichonse chimene munthu amene akukhayo anakhalapo chizikhala chodetsedwa. 10  Aliyense wokhudza chilichonse chimene munthuyo wakhalapo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. Ndipo munthu wonyamula zinthu zimenezi azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 11  Ngati munthu amene akukhayo+ wagwira munthu wina asanasambe mʼmanja, munthuyo azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 12  Chiwiya chadothi chimene munthu wanthenda yakukhayo wakhudza chiziswedwa, ndipo chikakhala chamtengo chizitsukidwa.+ 13  Ndiyeno munthuyo akachira nthenda yake yakukhayo, pazipita masiku 7 kuti akhale woyera. Kenako azichapa zovala zake nʼkusamba madzi otunga kumtsinje, ndipo iye adzakhala woyera.+ 14  Pa tsiku la 8 azitenga njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda+ ndipo azibwera nazo pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako, nʼkuzipereka kwa wansembe. 15  Ndiyeno wansembe azipereka nsembe mbalamezo, imodzi monga nsembe yamachimo ndipo inayo monga nsembe yopsereza. Wansembe azimuphimbira machimo pamaso pa Yehova chifukwa cha nthenda yake yakukhayo. 16  Mwamuna akatulutsa umuna, azisamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 17  Azichapa chovala chilichonse ndi chikopa chilichonse chimene pagwera umunawo, ndipo chizikhala chodetsedwa mpaka madzulo. 18  Mwamuna akagona ndi mkazi nʼkutulutsa umuna, onse awiri azisamba thupi lonse, ndipo azikhala odetsedwa mpaka madzulo.+ 19  Ngati mkazi akukha magazi, azikhala masiku 7 ali wodetsedwa chifukwa chakuti akusamba.+ Aliyense amene angamukhudze adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 20  Chilichonse chimene angagonepo pamene ali wodetsedwa chifukwa chakuti akusamba chizikhala chodetsedwa, ndiponso chilichonse chimene wakhalapo chizikhala chodetsedwa.+ 21  Aliyense wokhudza bedi lake azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 22  Aliyense wokhudza chilichonse chimene mkaziyo anakhalira azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 23  Ndipo ngati mkaziyo anakhala pabedi kapena pachinthu china, aliyense wokhudza chinthu chimenecho azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 24  Mwamuna akagona ndi mkazi ameneyu, azikhala wodetsedwa chifukwa chakuti mkaziyo akusamba.+ Zikatero, mwamunayo azikhala wodetsedwa kwa masiku 7, ndipo bedi lililonse limene angagonepo lizikhala lodetsedwa. 25  Mkazi akakha magazi kwa masiku ambiri+ pamene si nthawi yake yosamba,+ kapena akapitiriza kukha magazi nthawi yake yosamba itatha, azikhala wodetsedwa masiku onse amene akukha magaziwo ngati mmene amakhalira pa nthawi yake yosamba. 26  Bedi lililonse limene angagonepo pa nthawi imene akukha magaziwo,+ lizikhala ngati bedi limene amagonapo pa nthawi imene akusamba. Ndipo chinthu chilichonse chimene angakhalepo, chizikhala chodetsedwa ngati mmene chingakhalire chodetsedwa pa nthawi imene akusamba. 27  Aliyense amene angakhudze zinthuzo adzakhala wodetsedwa, ndipo azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 28  Akasiya kukha magaziwo, pazipita masiku 7, kenako azikhala woyera.+ 29  Pa tsiku la 8 azitenga njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda,+ nʼkubwera nawo kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako.+ 30  Wansembe azipereka mbalame imodzi monga nsembe yamachimo ndipo inayo monga nsembe yopsereza. Ndiyeno wansembe azimuphimbira machimo pamaso pa Yehova chifukwa cha kukhako.+ 31  Muzionetsetsa kuti Aisiraeli akupewa chilichonse chodetsa, kuopera kuti angafe chifukwa chodetsa chihema changa chimene chili pakati pawo.+ 32  Limeneli ndi lamulo lokhudza mwamuna amene ali ndi nthenda yakukha kumaliseche, ndi mwamuna amene ndi wodetsedwa chifukwa chakuti watulutsa umuna.+ 33  Lamulo limeneli ndi lokhudzanso mkazi wodetsedwa chifukwa chakuti akusamba,+ mwamuna kapena mkazi aliyense amene ali ndi nthenda yakukha kumaliseche,+ ndiponso mwamuna amene wagona ndi mkazi wodetsedwa.’”

Mawu a M'munsi