Levitiko 21:1-24

  • Ansembe azikhala oyera komanso osadetsedwa (1-9)

  • Mkulu wa ansembe asamadzidetse (10-15)

  • Ansembe asamakhale ndi chilema (16-24)

21  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: “Uza ansembe, ana a Aroni kuti, ‘Aliyense wa inu asadzidetse chifukwa cha munthu amene wamwalira pakati pa anthu a mtundu wake.+  Koma angathe kudzidetsa ngati wamwalirayo ndi wachibale wake wapafupi, mayi ake, bambo ake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi ndi mchimwene wake.  Angathenso kudzidetsa ngati wamwalirayo ndi mchemwali wake, amene ndi namwali wosakwatiwa yemwe amakhala naye limodzi.  Koma sakuyenera kudzidetsa chifukwa cha mkazi wamwini pakati pa anthu a mtundu wake nʼkudziipitsa.  Asamamete mpala mitu yawo,+ asamamete ndevu zamʼmasaya mwawo ndipo asamadzitemeteme thupi lawo.+  Azikhala oyera kwa Mulungu wawo+ ndipo asamadetse dzina la Mulungu wawo,+ chifukwa iwowa amapereka kwa Yehova nsembe zowotcha pamoto, zomwe ndi chakudya cha Mulungu wawo, choncho azikhala oyera.+  Wansembe asamakwatire hule+ kapena mkazi amene wataya unamwali wake. Asamakwatirenso mkazi amene mwamuna wake anamusiya ukwati,+ chifukwa wansembeyo ndi woyera kwa Mulungu wake.  Muzimuona kuti ndi woyera+ chifukwa ndi amene amapereka chakudya cha Mulungu wanu. Azikhala woyera kwa inu, chifukwa ine Yehova, amene ndikukupatulani, ndine woyera.+  Mwana wamkazi wa wansembe akadzidetsa pochita uhule, ndiye kuti akudetsa bambo ake. Aziphedwa kenako nʼkumuwotcha.+ 10  Mkulu wa ansembe wokhala pakati pa abale ake ansembe, amene anamuthira mafuta odzozera unsembe pamutu pake,+ nʼkuikidwa kukhala wansembe* kuti azivala zovala zaunsembe,+ asalekerere tsitsi lake osalisamala ndipo asangʼambe zovala zake.+ 11  Iye asayandikire munthu aliyense wakufa+ ndipo asamadzidetse ngakhale amene wamwalirayo atakhala bambo ake kapena mayi ake. 12  Asamatuluke mʼmalo opatulika ndipo asamadetse malo opatulika a Mulungu wake,+ chifukwa pamutu pake pali chizindikiro cha kudzipereka, chomwe ndi mafuta odzozera a Mulungu wake.+ Ine ndine Yehova. 13  Mkulu wa ansembe akafuna kukwatira, azikwatira namwali.+ 14  Asakwatire mkazi wamasiye kapena amene mwamuna wake anamusiya ukwati, mkazi amene wataya unamwali wake kapena hule, koma azikwatira namwali pakati pa anthu amtundu wake. 15  Asadetse ana ake* pakati pa anthu a mtundu wake,+ chifukwa ine ndine Yehova amene ndamuyeretsa.’” 16  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 17  “Lankhula ndi Aroni kuti, ‘Munthu aliyense mwa ana ako,* ku mibadwo yawo yonse, amene ali ndi chilema asayandikire malo opatulika kudzapereka chakudya cha Mulungu wake. 18  Munthu akakhala ndi chilema chilichonse, asayandikire malo opatulika. Kaya akhale ndi vuto losaona, wolumala, wankhope yopotoka,* wamkono kapena mwendo wautali kwambiri kuposa unzake, 19  wothyoka phazi kapena dzanja, 20  wa linunda, wamfupi kwambiri,* wa diso lolumala, wa zikanga, wa zipere ndi wa mavalo owonongeka.+ 21  Munthu aliyense mwa ana a Aroni* wansembe, amene ali ndi chilema, asamayandikire guwa lansembe kudzapereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova. Asamayandikire guwa lansembe kudzapereka chakudya cha Mulungu wake chifukwa ali ndi chilema. 22  Iye angathe kudya chakudya cha Mulungu wake kuchokera pa zinthu zopatulika koposa+ ndi pa zinthu zopatulika.+ 23  Koma asamayandikire katani+ ndiponso guwa lansembe,+ chifukwa iye ali ndi chilema. Asadetse malo anga opatulika,+ chifukwa ine ndine Yehova amene ndikuwayeretsa.’”+ 24  Choncho Mose anafotokoza zimenezi kwa Aroni ndi ana ake, ndiponso kwa Aisiraeli onse.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkudzaza dzanja lake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yako.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wamphuno yokhadzuka.”
Mabaibulo ena amati, “munthu woonda kwambiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu ya Aroni.”