Levitiko 22:1-33

  • Kuyeretsedwa kwa ansembe komanso kudya zinthu zopatulika (1-16)

  • Nyama zopanda chilema zokha ndi zimene ziyenera kuperekedwa nsembe (17-33)

22  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2  “Uza Aroni ndi ana ake kuti azilemekeza* zinthu zopatulika zimene Aisiraeli abweretsa kwa ine,+ kuti asadetse dzina langa loyera.+ Ine ndine Yehova. 3  Uwauze kuti, ‘Mʼmibadwo yanu yonse munthu aliyense wodetsedwa mwa ana anu, amene wakhudza zinthu zopatulika zimene Aisiraeli azipatula kuti azipereke nsembe kwa Yehova, munthu ameneyo aziphedwa kuti asakhalenso pamaso panga.+ Ine ndine Yehova. 4  Mwamuna aliyense mwa ana a Aroni amene ali ndi khate+ kapena nthenda yakukha,+ asadye zinthu zopatulika mpaka atakhala woyera.+ Zikhalenso chimodzimodzi ndi aliyense wokhudza munthu amene wadetsedwa chifukwa cha munthu wakufa,+ kapena mwamuna amene watulutsa umuna,+ 5  kapenanso mwamuna amene wakhudza chilichonse mwa zamoyo zodetsedwa zopezeka zambiri,+ kapena amene wakhudza munthu wodetsedwa pa chifukwa chilichonse amene angachititse kuti akhale wodetsedwa.+ 6  Munthu wokhudza chilichonse mwa zinthu zoterezi azikhala wodetsedwa mpaka madzulo ndipo asamadye chinthu chopatulika chilichonse, koma azisamba thupi lonse.+ 7  Dzuwa likalowa adzakhalanso woyera, ndipo pambuyo pake akhoza kudya zina mwa zinthu zopatulika, chifukwa ndi chakudya chake.+ 8  Sakuyeneranso kudya nyama iliyonse imene waipeza yakufa kapena imene yaphedwa ndi zilombo nʼkukhala wodetsedwa.+ Ine ndine Yehova. 9  Iwo azisunga malamulo anga kuti asachimwe nʼkufa chifukwa chodetsa zinthu zopatulika atalephera kusunga malamulowo. Ine ndine Yehova amene ndikuwayeretsa. 10  Munthu wamba* asadye chinthu chopatulika chilichonse.+ Mlendo wokhala mʼnyumba ya wansembe kapena munthu waganyu, asadye chinthu chopatulika chilichonse. 11  Koma ngati wansembe wagula munthu ndi ndalama zake, munthuyo angathe kudya nawo zinthu zopatulikazo. Akapolo obadwira mʼnyumba ya wansembe, angathenso kudya nawo chakudya chake.+ 12  Mwana wamkazi wa wansembe akakwatiwa ndi munthu amene si wansembe,* asamadye nawo zopereka zopatulika. 13  Koma mwana wa wansembe akakhala mkazi wamasiye kapena ngati anasiyidwa ukwati alibe mwana aliyense, ndipo wabwerera kunyumba kwa bambo ake kumene anali ali mwana, angathe kudya nawo chakudya cha bambo ake.+ Koma munthu wamba* asamadye nawo. 14  Munthu akadya mosadziwa chinthu chopatulika, azibweza chinthucho nʼkuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo 5 a chinthucho. Azipereka chinthu chopatulikacho kwa wansembe.+ 15  Zili choncho kuti ansembe asamadetse zinthu zopatulika za Aisiraeli, zimene amapereka kwa Yehova,+ 16  nʼkuchititsa anthuwo kuti achimwe nʼkulandira chilango chifukwa chakuti adya zinthu zopatulika. Ine ndine Yehova amene ndikuwayeretsa.’” 17  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 18  “Uza Aroni ndi ana ake komanso Aisiraeli onse kuti, ‘Mwamuna aliyense amene ndi wa Chiisiraeli kapena mlendo wokhala mu Isiraeli amene akupereka kwa Yehova nsembe yopsereza+ pofuna kukwaniritsa malonjezo ake kapena kuti ikhale nsembe yake yaufulu,+ 19  azipereka nyama yopanda chilema,+ ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo kapena mbuzi, kuti Mulungu asangalale naye. 20  Musamapereke nsembe nyama iliyonse yachilema,+ chifukwa Mulungu sangasangalale nanu. 21  Ngati munthu akupereka nsembe yamgwirizano+ kwa Yehova kuti akwaniritse lonjezo lake kapena kuti ikhale nsembe yaufulu, azipereka ngʼombe kapena nkhosa yopanda chilema, kuti Mulungu ailandire. Izikhala yopanda chilema chilichonse. 22  Isakhale yakhungu, yothyoka fupa, yotemeka, yokhala ndi njerewere, nkhanambo* kapena zipere. Musamapereke kwa Yehova nyama zoterezi kapena kuwotcha nyama zoterezi paguwa lansembe la Yehova. 23  Mungapereke ngʼombe kapena nkhosa yomwe ili ndi mwendo wautali kwambiri kapena waufupi kwambiri kuposa unzake kuti ikhale nsembe yaufulu. Koma Mulungu sadzailandira ngati mukuipereka ngati nsembe pokwaniritsa lonjezo lanu. 24  Musamapereke kwa Yehova nyama imene mavalo ake ndi owonongeka, ophwanyika kapena yofulidwa. Musamapereke nsembe nyama zoterezi mʼdziko lanu. 25  Ndipo nyama iliyonse mwa nyama zoterezi imene mlendo wakupatsani musamaipereke nsembe kuti ikhale chakudya cha Mulungu wanu, chifukwa ili ndi chilema ndipo Mulungu sadzailandira.’” 26  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 27  “Ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi ikabadwa, izikhala ndi mayi ake masiku 7,+ koma kuyambira tsiku la 8 kupita mʼtsogolo mungaipereke kwa Yehova monga nsembe yowotcha pamoto, ndipo Mulungu adzailandira. 28  Musamaphe ngʼombe kapena nkhosa ndi mwana wake pa tsiku limodzi.+ 29  Mukafuna kupereka nsembe yoyamikira kwa Yehova+ muziipereka mʼnjira yakuti Mulungu asangalale nanu. 30  Muziidya tsiku lomwelo. Musasiye nyama iliyonse mpaka mʼmamawa.+ Ine ndine Yehova. 31  Muzisunga malamulo anga komanso kuwatsatira.+ Ine ndine Yehova. 32  Musamadetse dzina langa loyera,+ mʼmalomwake muzindiona kuti ndine wopatulika pakati pa Aisiraeli.+ Ine ndine Yehova amene ndikukuyeretsani.+ 33  Ndine amene ndakutulutsani mʼdziko la Iguputo kuti ndikusonyezeni kuti ndine Mulungu wanu.+ Ine ndine Yehova.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzipatule pa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mlendo,” kutanthauza mwamuna amene si wa mʼbanja la Aroni.
Kapena kuti, “akakwatiwa ndi mlendo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mlendo,” kutanthauza mwamuna amene si wa mʼbanja la Aroni.
Amenewa ndi matenda amene amachititsa kuti khungu liume nʼkumakanganuka ngati mmene zimakhalira bala likamapola.