Levitiko 23:1-44

  • Masiku opatulika komanso zikondwerero (1-44)

    • Sabata (3)

    • Pasika (4, 5)

    • Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa (6-8)

    • Nsembe za zipatso zoyambirira (9-14)

    • Zikondwerero za Masabata (15-21)

    • Kakololedwe koyenera (22)

    • Mwambo Woliza Lipenga (23-25)

    • Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo (26-32)

    • Chikondwerero cha Misasa (33-43)

23  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:  “Uza Aisiraeli kuti, ‘Muzilengeza+ zikondwerero+ za Yehova zimene ndi misonkhano yopatulika. Izi ndi zikondwerero zanga:  Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale sabata lopuma pa ntchito zanu zonse.+ Limeneli ndi tsiku la msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse chifukwa limeneli ndi sabata la Yehova kulikonse kumene mungakhale.+  Zikondwerero za Yehova, kapena kuti misonkhano yopatulika imene muyenera kulengeza pa nthawi yake yoikidwiratu ndi iyi:  Mʼmwezi woyamba, pa tsiku la 14 la mweziwo,+ madzulo kuli kachisisira,* lizikhala tsiku la Pasika wa Yehova.+  Pa tsiku la 15 la mwezi umenewu, muzichitira Yehova Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda zofufumitsa kwa masiku 7.+  Pa tsiku loyamba la chikondwererocho muzichita msonkhano wopatulika+ ndipo musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa.  Kwa masiku 7, muzipereka kwa Yehova nsembe zowotcha pamoto. Pa tsiku la 7 muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa.’”  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 10  “Uza Aisiraeli kuti, ‘Mukadzalowa mʼdziko limene ndikukupatsani, nʼkukolola mbewu zamʼdzikomo, muzidzabweretsa kwa wansembe+ mtolo umodzi wa zipatso zanu zoyambirira.+ 11  Ndipo wansembe azidzayendetsa mtolowo uku ndi uku pamaso pa Yehova kuti Mulungu asangalale nanu. Sabata likatha, wansembe azidzayendetsa mtolowo uku ndi uku pa tsiku lotsatira. 12  Pa tsiku loyendetsa mtolo wanu uku ndi uku, muzipereka mwana wa nkhosa wopanda chilema, wosapitirira chaka chimodzi, kuti akhale nsembe yopsereza yoperekedwa kwa Yehova. 13  Popereka nsembe imeneyi muziperekanso nsembe yambewu. Nsembeyo izikhala ufa wosalala wothira mafuta, muyezo wake magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* kuti ikhale nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova, yakafungo kosangalatsa.* Muziperekanso vinyo wa nsembe yachakumwa, muyezo wake gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.* 14  Musamadye mkate, mbewu zokazinga kapena mbewu zatsopano mpaka tsiku limeneli litafika komanso mutabweretsa nsembe ya Mulungu wanu. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale ku mibadwo yanu yonse, kulikonse kumene mungakhale. 15  Kuchokera pa tsiku lotsatana ndi Sabata, pamene munabweretsa mtolo kuti ukhale nsembe yoyendetsa uku ndi uku,+ muziwerenga masabata 7, ndipo sabata iliyonse izikhala ndi masiku okwanira. 16  Muziwerenga masiku 50+ kukafika pa tsiku lotsatizana ndi tsiku limene Sabata la 7 lathera, kenako muzipereka nsembe yambewu zatsopano kwa Yehova.+ 17  Muzibweretsa mitanda iwiri ya mkate wamʼnyumba mwanu kuti ikhale nsembe yoyendetsa uku ndi uku. Mitandayo izikhala yopangidwa ndi ufa wosalala wokwanira magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* Poiphika izikhala ndi zofufumitsa,+ ndipo muziipereka kwa Yehova monga zipatso zoyambirira kucha.+ 18  Popereka mitanda ya mkateyi muziperekanso ana a nkhosa amphongo opanda chilema okwana 7, aliyense wa chaka chimodzi, komanso ngʼombe imodzi yaingʼono yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.+ Zimenezi ziziperekedwa monga nsembe yopsereza, nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova. Ziziperekedwa pamodzi ndi nsembe yambewu ndi nsembe zachakumwa kuti zikhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova. 19  Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo,+ ndi ana a nkhosa amphongo awiri, aliyense wachaka chimodzi, monga nsembe yamgwirizano.+ 20  Wansembe aziyendetsa uku ndi uku ana a nkhosa awiriwo pamodzi ndi mitanda ya mkate ya zipatso zoyambirira kucha, monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku yoperekedwa kwa Yehova. Zimenezi zizikhala zinthu zopatulika kwa Yehova ndipo zizikhala za wansembe.+ 21  Pa tsiku limeneli muzilengeza+ kuti kuli msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale kulikonse kumene mungakhale mʼmibadwo yanu yonse. 22  Mukamakolola zinthu zamʼmunda mwanu, musamachotseretu zonse mʼmphepete mwa mundawo, ndipo musamachite khunkha mʼmunda mwanumo.+ Zotsalazo muzisiyira wosauka*+ ndi mlendo wokhala pakati panu.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’” 23  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 24  “Lankhula ndi Aisiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘Mʼmwezi wa 7, pa tsiku loyamba la mweziwo, muzipuma pa ntchito zanu zonse. Limeneli ndi tsiku la chikumbutso, ndipo lipenga likalira+ muzisonkhana kuti mulambire Mulungu. 25  Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa pa tsikuli, ndipo muzipereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova.’” 26  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 27  “Tsiku la 10 mʼmwezi wa 7 umenewu, ndi Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo.+ Muzichita msonkhano wopatulika ndipo muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni*+ chifukwa cha machimo anu ndipo muzipereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova. 28  Pa tsiku limeneli musamagwire ntchito iliyonse, chifukwa ndi tsiku lochita mwambo wophimba machimo+ anu pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 29  Munthu aliyense amene sadzasonyeza kuti akudzimvera chisoni* chifukwa cha machimo ake pa tsiku limeneli adzaphedwe kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.+ 30  Munthu aliyense wogwira ntchito iliyonse pa tsiku limeneli, ndidzamuwononga nʼkumuchotsa pakati pa anthu a mtundu wake. 31  Musamagwire ntchito iliyonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale ku mibadwo yanu yonse, kulikonse kumene mungakhale. 32  Ili ndi sabata lopuma pa ntchito zanu zonse, ndipo muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni+ chifukwa cha machimo anu madzulo pa tsiku la 9 la mweziwo. Muzisunga sabata kuyambira madzulo mpaka madzulo tsiku lotsatira.” 33  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 34  “Uza Aisiraeli kuti, ‘Tsiku la 15 la mwezi wa 7 umenewu, ndi tsiku lochitira Yehova Chikondwerero cha Misasa kwa masiku 7.+ 35  Pa tsiku loyamba la chikondwererocho muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa. 36  Kwa masiku 7 muzipereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova. Pa tsiku la 8 muzichita msonkhano wopatulika,+ ndipo muzipereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova. Umenewu ndi msonkhano wapadera. Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa. 37  Zimenezi ndi zikondwerero+ za Yehova zimene muyenera kulengeza monga misonkhano yopatulika+ yoperekera nsembe zowotcha pamoto kwa Yehova. Imeneyi ndi misonkhano yoperekera nsembe zopsereza,+ nsembe zambewu+ ndi nsembe zachakumwa+ motsatira ndandanda ya tsiku ndi tsiku. 38  Muzichita zimenezi kuwonjezera pa zimene mumapereka pa masabata a Yehova,+ mphatso zanu,+ nsembe zanu zimene mumapereka pokwaniritsa lonjezo+ ndi nsembe zanu zonse zaufulu+ zimene mukuyenera kupereka kwa Yehova. 39  Pa tsiku la 15 la mwezi wa 7, mukakolola zinthu zamʼmunda mwanu, muzichita chikondwerero cha Yehova masiku 7.+ Tsiku loyamba la chikondwererocho ndi tsiku lopuma pa ntchito zanu zonse, ndipo muzipumanso pa ntchito zanu zonse pa tsiku la 8.+ 40  Pa tsiku loyambali muzitenga zipatso zabwino kwambiri, masamba a kanjedza,+ nthambi za masamba ambiri ndi mitengo ya msondodzi yamʼchigwa.* Mukatero muzisangalala+ kwa masiku 7 pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+ 41  Muzichitira Yehova chikondwerero chimenechi kwa masiku 7 pa chaka,+ mʼmwezi wa 7. Limeneli ndi lamulo mʼmibadwo yanu yonse mpaka kalekale. 42  Muzikhala mʼmisasa masiku 7.+ Mbadwa zonse za Isiraeli zizikhala mʼmisasa, 43  kuti mibadwo yanu ya mʼtsogolo idzadziwe+ kuti ine ndinachititsa Aisiraeli kukhala mʼmisasa powatulutsa mʼdziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’” 44  Choncho Mose anafotokozera Aisiraeli za zikondwerero za Yehova.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa madzulo awiri.”
Magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi ofanana ndi malita 4.4. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Muyezo wa hini ndi wofanana ndi malita 3.67. Onani Zakumapeto B14
Magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi ofanana ndi malita 4.4. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “wovutika.”
Ankasonyeza chisoni chimenechi posala kudya ndiponso kudzimana zinthu zina.
Mabaibulo ena amati, “amene sakusala kudya.”
Kapena kuti, “yamʼkhwawa.”