Levitiko 24:1-23

  • Mafuta a nyale zamuchihema (1-4)

  • Mitanda ya mkate wachionetsero (5-9)

  • Munthu wonyoza dzina la Mulungu aziponyedwa miyala (10-23)

24  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:  “Lamula Aisiraeli kuti akubweretsere mafuta ounikira oyenga bwino kwambiri a maolivi, kuti nyale ziziyaka nthawi zonse.+  Aroni azikhazika nyale kunja kwa katani ya Malo Oyera Koposa mʼchihema chokumanako. Nyalezo ziziunikira pamaso pa Yehova nthawi zonse kuyambira madzulo mpaka mʼmawa. Limeneli ndi lamulo kwa inu mpaka kalekale mʼmibadwo yanu yonse.  Nyalezo azikhazike pachoikapo nyale+ chagolide woyenga bwino, ndipo zizikhala pamaso pa Yehova nthawi zonse.  Utenge ufa wosalala nʼkuphika mikate 12 yozungulira yoboola pakati. Mkate uliwonse uzipangidwa ndi ufa wokwanira magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.*  Ndipo usanjikize mikateyo mʼmagulu awiri. Gulu lililonse likhale ndi mikate 6.+ Uike mikateyo patebulo lagolide woyenga bwino pamaso pa Yehova.+  Pagulu lililonse la mikateyo uike lubani weniweni. Lubaniyo aziperekedwa nsembe yowotcha pamoto+ kwa Yehova kuimira nsembe yonseyo.  Pa tsiku lililonse la Sabata azikhazika mkatewo pamaso pa Yehova nthawi zonse.+ Limeneli ndi pangano pakati pa ine ndi Aisiraeli mpaka kalekale.  Mkatewo uzikhala wa Aroni ndi ana ake,+ ndipo aziudyera mʼmalo oyera,+ chifukwa waperekedwa kwa iye monga chinthu choyera koposa kuchokera pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova. Limeneli likhale lamulo mpaka kalekale.” 10  Ndiyeno panali mnyamata wina amene mayi ake anali a Chiisiraeli, koma bambo ake anali a ku Iguputo.+ Mnyamatayu anayamba kumenyana ndi munthu wina wa Chiisiraeli mumsasa. 11  Mnyamatayo anayamba kunyoza* ndi kutukwana dzina la Mulungu.*+ Ndiye anapita naye kwa Mose.+ Dzina la mayi ake linali Selomiti, mwana wa Dibiri wa fuko la Dani. 12  Ndiyeno anamutsekera kudikira kuti Yehova apereke chigamulo pa nkhaniyo.+ 13  Kenako Yehova anauza Mose kuti: 14  “Munthu wotemberera dzina la Mulungu uja, mupite naye kunja kwa msasa. Onse amene anamumva akutemberera aike manja awo pamutu pake ndipo gulu lonse limuponye miyala.+ 15  Ndiyeno uuze Aisiraeli kuti, ‘Ngati munthu aliyense watemberera Mulungu wake, aziyankha mlandu wa tchimo lakelo. 16  Choncho munthu amene wanyoza dzina la Yehova aziphedwa ndithu.+ Gulu lonse lizimuponya miyala. Kaya ndi mlendo wokhala pakati panu kapena nzika, aziphedwa chifukwa chonyoza Dzinalo. 17  Munthu aliyense amene wapha munthu, nayenso aziphedwa ndithu.+ 18  Munthu amene wamenya nʼkupha chiweto cha mnzake, azibweza chiweto china, chiweto kulipira chiweto.* 19  Munthu akavulaza mnzake, zimene wachitira mnzakezo iyenso muzimʼchitira zomwezo.+ 20  Kuthyola fupa kulipira kuthyola fupa, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino. Mmene wavulazira mnzake nayenso muzimʼvulaza chimodzimodzi.+ 21  Munthu amene wamenya nʼkupha chiweto cha mnzake azilipira,+ koma amene wamenya nʼkupha munthu nayenso aziphedwa.+ 22  Chigamulo chilichonse chizigwira ntchito mofanana kwa mlendo wokhala pakati panu ndi kwa nzika,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu.’” 23  Kenako Mose anafotokoza zimenezi kwa Aisiraeli, ndipo iwo anatulutsa munthu wotemberera uja kunja kwa msasa nʼkumuponya miyala.+ Choncho Aisiraeli anachita zonse mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

Mawu a M'munsi

Magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi ofanana ndi malita 4.4. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “kutemberera.”
Pamenepa akutanthauza dzina lakuti Yehova mogwirizana ndi vesi 15 ndi 16.
Kapena kuti, “moyo kulipira moyo.”