Levitiko 3:1-17

  • Nsembe yamgwirizano (1-17)

    • Musamadye mafuta kapena magazi (17)

3  “‘Ngati akupereka nsembe yamgwirizano*+ kwa Yehova ndipo akufuna kupereka ngʼombe yamphongo kapena yaikazi, azipereka yopanda chilema.  Ndiyeno aziika dzanja lake pamutu pa ngʼombeyo ndipo iziphedwa pakhomo la chihema chokumanako. Akatero ana a Aroni ansembe, aziwaza magazi ake mbali zonse za guwa lansembe.  Azipereka mbali ina ya nsembe yamgwirizanoyo ngati nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.+ Azipereka mafuta+ okuta matumbo ndi mafuta onse amene ali pamatumbo.  Aziperekanso impso ziwiri ndi mafuta okuta impsozo omwe ali pafupi ndi chiuno. Koma mafuta apachiwindi aziwachotsa pamodzi ndi impsozo.+  Kenako ana a Aroni aziwotcha zinthu zimenezi paguwa lansembe, pamwamba pa nsembe yopsereza yomwe ili pankhuni zimene zili pamoto.+ Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* yoperekedwa kwa Yehova.+  Ngati akupereka nkhosa kapena mbuzi monga nsembe yamgwirizano kwa Yehova, azipereka yamphongo kapena yaikazi, yopanda chilema.+  Ngati akupereka nkhosa yaingʼono yamphongo monga nsembe yake, aziibweretsa kwa Yehova.  Kenako aziika dzanja lake pamutu pa nkhosayo ndipo iziphedwa patsogolo pa chihema chokumanako. Akatero ana a Aroni aziwaza magazi ake mbali zonse za guwa lansembe.  Ndipo pansembe yamgwirizanoyo azitengapo mafuta ake ndi kuwapereka kwa Yehova+ monga nsembe yowotcha pamoto. Azichotsa mchira wonse wamafuta pafupi ndi fupa la msana ndiponso mafuta okuta matumbo ndi mafuta onse amene ali pamatumbo. 10  Azichotsanso impso ziwiri zomwe zili pafupi ndi chiuno ndi mafuta okuta impsozo. Komanso azichotsa mafuta apachiwindi pamodzi ndi impsozo.+ 11  Ndipo wansembe aziwotcha zinthu zonsezi paguwa lansembe monga chakudya,* kuti zikhale nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.+ 12  Ngati akupereka mbuzi monga nsembe yake, aziibweretsa pamaso pa Yehova. 13  Ndiyeno aziika dzanja lake pamutu pa mbuziyo ndipo iziphedwa patsogolo pa chihema chokumanako. Akatero ana a Aroni aziwaza magazi ake mbali zonse za guwa lansembe. 14  Ndipo pambuziyo azitengapo mafuta okuta matumbo ndi mafuta onse amene ali pamatumbo,+ nʼkuwapereka kwa Yehova ngati nsembe yowotcha pamoto. 15  Aziperekanso impso ziwiri zomwe zili pafupi ndi chiuno ndi mafuta okuta impsozo. Komanso azichotsa mafuta apachiwindi pamodzi ndi impsozo. 16  Wansembe aziwotcha zinthu zonsezi paguwa lansembe monga chakudya.* Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa.* Mafuta onse ndi a Yehova.+ 17  Musamadye mafuta kapena magazi alionse.+ Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale, kulikonse kumene mungakhale.’”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “nsembe yamtendere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkate,” kutanthauza chakudya cha Mulungu chochokera pansembe yamgwirizano.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkate,” kutanthauza chakudya cha Mulungu chochokera pansembe yamgwirizano.
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”