Levitiko 5:1-19

  • Machimo osiyanasiyana komanso nsembe zake (1-6)

    • Kuulula machimo a anthu ena (1)

  • Nsembe zimene anthu osauka ankapereka (7-13)

  • Nsembe yakupalamula imene munthu amapereka chifukwa chakuti wachimwa mosadziwa (14-19)

5  “‘Munthu akaona wina akuchita tchimo, kapena wamva kuti wina wachita tchimo, munthu ameneyo ndi mboni. Akamva chilengezo kuti akachitire umboni+ za tchimolo* koma iye osapita kukanena, ndiye kuti wachimwa. Ayenera kuyankha mlandu wa cholakwa chakecho.  Munthu akakhudza chinthu chodetsedwa, kaya ikhale nyama yakufa yakuthengo, nyama yakufa yoweta kapena kamodzi mwa tizilombo topezeka tambiri,+ ngakhale kuti sanazindikire, iye ndi wodetsedwa ndipo wapalamula mlandu.  Kapena munthu akakhudza mosadziwa chodetsa chilichonse chochokera kwa munthu,+ kutanthauza chinthu chilichonse chodetsedwa chimene chingamuchititse kuti akhale wodetsedwa ndipo wadziwa zimenezi, ndiye kuti wapalamula mlandu.  Kapenanso munthu akafulumira kulumbira kuti achita chinachake, kaya chabwino kapena choipa koma sanazindikire, kenako nʼkuzindikira kuti analumbira mofulumira, ndiye kuti wapalamula mlandu.*+  Akapalamula mlandu wokhudzana ndi chimodzi mwa zinthu zimenezi, aziulula tchimo+ limene wachita.  Azibweretsanso kwa Yehova nsembe yake yakupalamula chifukwa cha tchimo limene wachita.+ Azibweretsa nkhosa yaingʼono yaikazi kapena mbuzi yaingʼono yaikazi kuti ikhale nsembe yamachimo. Akatero wansembe aziphimba tchimo la munthuyo.  Koma ngati sangakwanitse kupereka nkhosa, azibweretsa kwa Yehova njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda+ kuti zikhale nsembe zakupalamula chifukwa cha tchimo limene wachita. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.+  Azibweretsa mbalamezi kwa wansembe, ndipo wansembeyo azipereka nsembe yamachimo choyamba, ataicheka pakhosi koma osaduliratu mutu wake.  Kenako azidontheza ena mwa magazi a nsembe yamachimo mʼmbali mwa guwa lansembe, koma magazi otsalawo aziwathira pansi pa guwa lansembelo.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo. 10  Mbalame inayo aziipereka ngati nsembe yopsereza motsatira ndondomeko ya nthawi zonse.+ Choncho wansembe aziphimba machimo amene munthuyo wachita, ndipo adzakhululukidwa.+ 11  Koma ngati sangakwanitse kupereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, azibweretsa ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa*+ kuti ukhale nsembe yamachimo chifukwa cha tchimo lake. Asauthire mafuta ndipo asaikemo lubani chifukwa imeneyi ndi nsembe yamachimo. 12  Akatero azibweretsa ufawo kwa wansembe, ndipo wansembeyo autape kudzaza dzanja limodzi kuimira nsembe yonseyo. Kenako auwotche paguwa lansembe pamwamba pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yamachimo. 13  Wansembeyo aziphimba tchimo limene munthuyo wachita. Aziphimba tchimo lililonse mwa machimo amenewa ndipo adzakhululukidwa.+ Zinthu zimene zatsala pa nsembeyo zizikhala za wansembe+ mofanana ndi nsembe yambewu.’”+ 14  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 15  “Munthu akachita mosakhulupirika pochimwira zinthu zopatulika kwa Yehova mosadziwa,+ azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo yopanda chilema kuti ikhale nsembe yake yakupalamula.+ Potchula mtengo wa nkhosayo azigwiritsa ntchito masekeli* asiliva ofanana ndi sekeli lakumalo oyera.*+ 16  Ndiyeno chifukwa choti wachimwira malo oyera, azilipira ndipo aziwonjezerapo limodzi mwa magawo 5 a malipirowo.+ Malipirowo aziwapereka kwa wansembe limodzi ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yakupalamula, kenako wansembeyo aziphimba machimo+ a munthuyo ndipo adzakhululukidwa.+ 17  Munthu akachimwa pochita chimodzi mwa zinthu zimene Yehova analamula kuti asachite, ngakhale kuti anachita mosazindikira, wapalamulabe mlandu ndipo aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho.+ 18  Azibweretsa kwa wansembe nkhosa yopanda chilema kuti ikhale nsembe yakupalamula.+ Mtengo wa nkhosayo uzikhala wofanana ndi mtengo wake woikidwiratu. Ndiyeno wansembe aziphimba machimo a munthuyo chifukwa cha cholakwa chimene anachita mosadziwa ndipo adzakhululukidwa. 19  Imeneyi ndi nsembe yakupalamula. Munthu ameneyo wapalamula mlandu chifukwa wachimwira Yehova.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Akamva mawu otemberera (lumbiro).” Nʼkutheka kuti chinali chilengezo chokhudza tchimo chimene ankatchulanso mawu otemberera munthu wochimwayo kapena mboni imene ikudziwa za nkhaniyo ngati italephera kudzapereka umboni wake.
Apa zikuonetsa kuti munthuyo sanakwaniritse zimene analumbira.
Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi lofanana ndi malita 2.2. Onani Zakumapeto B14.
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”