Levitiko 8:1-36

  • Kuikidwa unsembe kwa anthu a mʼbanja la Aroni (1-36)

8  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:  “Tenga Aroni limodzi ndi ana ake,+ zovala zawo,+ mafuta odzozera,+ ngʼombe yamphongo ya nsembe yamachimo, nkhosa ziwiri zamphongo ndi dengu la mikate yopanda zofufumitsa.+  Ndiyeno usonkhanitse gulu lonse pakhomo la chihema chokumanako.”  Mose anachita mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. Ndipo gulu lonse linasonkhana pakhomo la chihema chokumanako.  Kenako Mose anauza gululo kuti: “Yehova walamula kuti tichite zinthu izi.”  Choncho Mose anaitana Aroni ndi ana ake nʼkuwasambitsa ndi madzi.+  Atatero anaveka Aroni mkanjo+ nʼkumumanga lamba wapamimba.*+ Anamuvekanso malaya odula manja+ komanso efodi+ ndipo anamanga lamba woluka+ wa efodiyo.  Kenako anamuveka chovala chapachifuwa+ nʼkuika Urimu ndi Tumimu+ mʼchovala chapachifuwacho.  Anamuvekanso nduwira+ kumutu kwake, nʼkuika patsogolo pa nduwirayo kachitsulo konyezimira kagolide, chizindikiro chopatulika cha kudzipereka,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 10  Ndiyeno Mose anatenga mafuta odzozera nʼkudzoza chihema ndi zonse zimene zinali mkati mwake,+ kuti zikhale zopatulika. 11  Anawaza ena mwa mafuta odzozerawo maulendo 7 paguwa lansembe nʼkudzoza guwa lansembelo, zipangizo zake zonse, beseni ndi choikapo chake, kuti zikhale zopatulika. 12  Pomaliza Mose anathira ena mwa mafuta odzozera pamutu pa Aroni nʼkumudzoza kuti akhale wopatulika.+ 13  Kenako Mose anaitana ana a Aroni ndipo anawaveka mikanjo, anawamanga malamba apamimba komanso anawakulunga mipango kumutu,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 14  Atatero anabweretsa ngʼombe yamphongo ya nsembe yamachimo ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu pa ngʼombe ya nsembe yamachimoyo.+ 15  Ndiyeno Mose anapha ngʼombeyo nʼkutenga magazi+ ndi chala chake ndipo anawapaka panyanga zonse za guwa lansembe nʼkuyeretsa guwalo ku uchimo. Koma magazi otsalawo anawathira pansi pa guwa lansembe kuti alipatule, kuphimba machimo paguwalo. 16  Atatero Mose anatenga mafuta onse okuta matumbo, mafuta apachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake, nʼkuziwotcha paguwa lansembe.+ 17  Koma ngʼombe yonseyo, chikopa chake, nyama yake ndi ndowe zake anaziwotcha pamoto kunja kwa msasa,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 18  Kenako anatenga nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu pa nkhosayo.+ 19  Ndiyeno Mose anapha nkhosayo nʼkuwaza magazi ake mbali zonse za guwa lansembe. 20  Anaduladula nkhosayo ndipo Mose anatenga mutu wake, nyama yoduladulayo ndi mafuta ake,* nʼkuziwotcha. 21  Anatsuka matumbo ndi ziboda ndipo Mose anawotcha paguwa lansembe nkhosa yonseyo. Inali nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa.* Komanso inali nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 22  Kenako anabweretsa nkhosa yamphongo yachiwiri, nkhosa yowaikira kuti akhale ansembe,+ ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu pa nkhosayo.+ 23  Mose anapha nkhosayo ndi kutengako magazi ake nʼkuwapaka mʼmunsi pakhutu lakumanja la Aroni, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja ndi pachala chake chachikulu cha mwendo wakumanja. 24  Kenako Mose anaitana ana a Aroni nʼkuwapaka magazi mʼmunsi pakhutu lawo lakumanja, pachala chawo chamanthu kudzanja lamanja ndi pachala chawo chachikulu cha mwendo wakumanja. Koma magazi otsalawo, Mose anawawaza mbali zonse za guwa lansembe.+ 25  Atatero anatenga mafuta a nkhosayo, mchira wa mafuta, mafuta onse okuta matumbo, mafuta apachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake ndi mwendo wakumbuyo wakumanja.+ 26  Mʼdengu la mikate yosafufumitsa limene linali pamaso pa Yehova, anatengamo mtanda umodzi wa mkate wozungulira woboola pakati,+ mtanda umodzi wa mkate wozungulira woboola pakati wothira mafuta+ ndi kamtanda kamodzi ka mkate kopyapyala. Anaziika pamwamba pa mafuta ndi mwendo wakumbuyo wakumanja. 27  Atatero anaika zonsezi mʼmanja mwa Aroni ndi mʼmanja mwa ana ake nʼkuyamba kuziyendetsa uku ndi uku monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku yoperekedwa kwa Yehova. 28  Kenako Mose anazitenga mʼmanja mwawo nʼkuziwotcha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza. Zinthu zimenezi zinali nsembe yowaikira kuti akhale ansembe, yakafungo kosangalatsa.* Inali nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova. 29  Kenako Mose anatenga chidale nʼkuchiyendetsa uku ndi uku monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku yoperekedwa kwa Yehova.+ Chidale chimenechi anachitenga pa nkhosa yowaikira kuti akhale ansembe ndipo chinakhala gawo la Mose, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.+ 30  Ndipo Mose anatenga ena mwa mafuta odzozera+ ndi magazi amene anali paguwa lansembe aja nʼkuwaza Aroni ndi zovala zake komanso ana ake ndi zovala zawo. Choncho anapatula Aroni ndi zovala zake komanso ana ake+ ndi zovala zawo.+ 31  Ndiyeno Mose anauza Aroni ndi ana ake kuti: “Wiritsani+ nyamayo pakhomo la chihema chokumanako, ndipo muidyerenso pomwepo pamodzi ndi mkate umene uli mʼdengu logwiritsidwa ntchito poika anthu kuti akhale ansembe, mogwirizana ndi zimene anandilamula kuti, ‘Aroni ndi ana ake adye zimenezi.’+ 32  Ndipo nyama ndi mkate zotsala muziwotche pamoto.+ 33  Musachoke pakhomo la chihema chokumanako kwa masiku 7, mpaka masiku okuikani kuti mukhale ansembe atatha, chifukwa padzatenga masiku 7 kuti muikidwe kukhala ansembe.+ 34  Yehova walamula kuti tichite zomwe tachita lerozi kuti machimo anu aphimbidwe.+ 35  Mukhale pakhomo la chihema chokumanako masana ndi usiku kwa masiku 7.+ Ndipo muyenera kuchita zonse zimene Yehova walamula,+ kuti musafe. Chifukwa ndi zimene ndalamulidwa.” 36  Choncho Aroni ndi ana ake anachita zonse zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “lamba wamʼchiuno.”
Kapena kuti, “mafuta okuta impso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”