Levitiko 9:1-24

  • Aroni anapereka nsembe (1-24)

9  Pa tsiku la 8,+ Mose anaitana Aroni, ana ake ndi akulu a Isiraeli.  Iye anauza Aroni kuti: “Tenga ngʼombe yaingʼono kuti ikhale nsembe yamachimo+ ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza. Nyama zonsezi zikhale zopanda chilema ndipo uzipereke kwa Yehova.  Koma Aisiraeli uwauze kuti, ‘Tengani mbuzi yamphongo kuti ikhale nsembe yamachimo. Mutengenso mwana wa ngʼombe ndi nkhosa yaingʼono yamphongo, zonsezi zikhale za chaka chimodzi, zopanda chilema, kuti zikhale nsembe yopsereza.  Mutengenso ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo kuti muzipereke kwa Yehova monga nsembe zamgwirizano.+ Komanso mubwere ndi nsembe yambewu+ yothira mafuta chifukwa lero Yehova aonekera kwa inu.’”+  Choncho anthuwo anatenga zimene Mose analamula nʼkupita nazo kuchihema chokumanako. Kenako gulu lonse linayandikira nʼkuima pamaso pa Yehova.  Ndiyeno Mose anati: “Izi ndi zimene Yehova wakulamulani kuti muchite, kuti ulemerero wa Yehova uonekere kwa inu.”+  Kenako Mose anauza Aroni kuti: “Pita kuguwa lansembe ndi kupereka nsembe yako yamachimo+ ndi nsembe yako yopsereza, kuti uphimbe machimo ako+ ndi a nyumba yako.* Ukatero uwaperekere nsembe anthuwa+ nʼkuwaphimbira machimo awo,+ mogwirizana ndi zimene Yehova walamula.”  Nthawi yomweyo Aroni anapita kuguwa lansembe nʼkupha ngʼombe yaingʼono kuti ikhale nsembe yake+ yamachimo.  Ndiyeno ana ake anamubweretsera magazi+ a ngʼombeyo ndipo iye anaviika chala chake mʼmagaziwo nʼkuwapaka panyanga za guwa lansembe. Magazi otsala anawathira pansi pa guwa lansembelo.+ 10  Ndipo mafuta, impso ndi mafuta apachiwindi zimene anazitenga panyama ya nsembe yamachimo anaziwotcha paguwa lansembe, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.+ 11  Koma nyama ndi chikopa chake anaziwotcha kunja kwa msasa.+ 12  Ndiyeno Aroni anapha nyama ya nsembe yopsereza ndipo ana ake anamupatsa magazi a nyamayo. Atatero iye anawaza magaziwo mbali zonse za guwa lansembe.+ 13  Kenako anamʼpatsa nyama yoduladula ya nsembe yopsereza pamodzi ndi mutu ndipo anaziwotcha paguwa lansembe. 14  Atatero anatsuka matumbo komanso ziboda, nʼkuziwotcha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza. 15  Ndiyeno anaperekera nsembe anthu. Anatenga mbuzi yoperekera anthu nsembe yamachimo ndipo anaipha, nʼkuipereka monga nsembe yamachimo, mmene anachitira ndi nyama yoyamba ija. 16  Atatero anapereka nsembe yopsereza motsatira ndondomeko yake.+ 17  Kenako anapereka nsembe yambewu.+ Anatapako nsembeyo kudzaza dzanja lake nʼkuiwotcha paguwa lansembe, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya mʼmawa.+ 18  Ndiyeno Aroni anapha ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yamgwirizano yoperekera anthuwo. Kenako ana ake anamupatsa magazi a nyamazo ndipo iye anawaza magaziwo mbali zonse za guwa lansembe.+ 19  Koma mafuta a ngʼombeyo,+ mchira wa mafuta wa nkhosa, mafuta okuta ziwalo za mʼmimba, impso ndi mafuta apachiwindi,+ 20  ana a Aroni anaika mafuta amenewo pamwamba pa zidale za nyamazo. Kenako anawotcha mafutawo paguwa lansembe.+ 21  Koma Aroni anayendetsa uku ndi uku zidalezo ndi mwendo wakumbuyo wakumanja pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zimene Mose analamula.+ 22  Kenako Aroni anakweza manja ake nʼkuloza anthuwo ndipo anawadalitsa.+ Atatero anatsika kuguwa lansembe atamaliza kupereka nsembe yamachimo, nsembe yopsereza ndi nsembe zamgwirizano. 23  Pamapeto pake Mose ndi Aroni analowa mʼchihema chokumanako, kenako anatulukamo nʼkudalitsa anthuwo.+ Atatero ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse,+ 24  ndipo moto unatsika kuchokera kwa Yehova+ nʼkunyeketsa nsembe yopsereza ndiponso mafuta, zimene zinali paguwa lansembe. Anthu onse ataona zimenezi anayamba kufuula mokondwera ndipo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “a fuko lako.”