Wolembedwa ndi Luka 17:1-37

  • Kupunthwa, kukhululuka ndi chikhulupiriro (1-6)

  • Akapolo opanda pake (7-10)

  • Anthu 10 akhate anachiritsidwa (11-19)

  • Kubwera kwa Ufumu wa Mulungu (20-37)

    • Ufumu wa Mulungu uli “pakati panu” (21)

    • “Kumbukirani mkazi wa Loti” (32)

17  Kenako Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Nʼzosatheka kuti pakhale popanda zopunthwitsa. Koma tsoka kwa munthu amene zopunthwitsazo zimadzera mwa iye!  Zingamukhalire bwino kwambiri atamumangirira chimwala cha mphero mʼkhosi mwake nʼkumuponya mʼnyanja, kusiyana ndi kuti akhumudwitse mmodzi wa tiana iti.+  Samalani ndithu. Ngati mʼbale wako wachita tchimo umudzudzule+ ndipo akalapa umukhululukire.+  Ngakhale atakuchimwira maulendo 7 pa tsiku, nʼkubwera kwa iwe maulendo 7 kudzanena kuti, ‘Ndalapa ine,’ umukhululukire ndithu.”+  Kenako atumwiwo anauza Ambuye kuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.”+  Ndiyeno Ambuye anawauza kuti: “Mukanakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mukanatha kuuza mtengo wa mabulosi uwu kuti, ‘Zuka pano, kadzidzale mʼnyanjamo!’ ndipo ukanakumverani.+  Ndi ndani wa inu amene angauze kapolo wake yemwe wangofika kumene kuchokera kumunda kapena koweta nkhosa kuti, ‘Bwera kutebulo kuno msanga udzadyeʼ?  Kodi sadzamuuza kuti, ‘Ndikonzere chakudya chamadzulo, uvale epuloni nʼkunditumikira mpaka nditamaliza kudya ndi kumwa, pambuyo pake iwenso udye ndi kumwaʼ?  Munthuyo sangamuyamikire kapoloyo chifukwa zimene wachitazo ndi ntchito yake, si choncho? 10  Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munapatsidwa pa ntchito yanu, muzinena kuti: ‘Ife ndi akapolo opanda pake. Tangochita zimene tinayenera kuchita.’”+ 11  Ndiyeno pamene ankapita ku Yerusalemu, anadutsa mʼmalire a Samariya ndi Galileya. 12  Pamene ankalowa mʼmudzi winawake, anakumana ndi amuna 10 akhate koma iwo anaima chapatali ndithu.+ 13  Kenako anafuula mokweza kuti: “Yesu, Mlangizi, tichitireni chifundo!” 14  Yesu atawaona anawauza kuti: “Pitani mukadzionetse kwa ansembe.”+ Ndiyeno pamene ankapita anayeretsedwa.+ 15  Mmodzi wa iwo ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera akutamanda Mulungu mokweza mawu. 16  Atafika anagwada pamaso pa Yesu nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi, ndipo anamuthokoza. Munthu ameneyu anali Msamariya.+ 17  Yesu ananena kuti: “Kodi amene ayeretsedwa si anthu 10? Nanga anthu ena 9 aja ali kuti? 18  Kodi palibenso wina aliyense amene wabwerera kudzalemekeza Mulungu kupatulapo munthu wa mtundu wina yekhayu?” 19  Ndiyeno Yesu anauza munthuyo kuti: “Nyamuka uzipita. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+ 20  Afarisi atamufunsa kuti Ufumu wa Mulungu udzabwera liti,+ iye anawayankha kuti: “Ufumu wa Mulungu sudzabwera mwa maonekedwe ochititsa chidwi. 21  Ndipo anthu sadzanena kuti, ‘Onani uli kuno!’ kapena, ‘Onani uli uko!’ Chifukwa Ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”+ 22  Kenako anauza ophunzira ake kuti: “Masiku akubwera pamene mudzalakalaka kuona limodzi la masiku a Mwana wa munthu koma simudzaliona. 23  Anthu adzakuuzani kuti, ‘Onani ali uko!’ kapena ‘Onani ali kuno!’ Koma inu musadzapiteko kapena kuwatsatira.+ 24  Chifukwa mofanana ndi mphezi imene imangʼanima kuchokera mbali ina ya thambo kukafika mbali ina ya thambo, zidzakhalanso choncho ndi Mwana wa munthu+ mʼtsiku lake.+ 25  Koma choyamba akuyenera kukumana ndi mavuto ambiri komanso kukanidwa ndi mʼbadwo uwu.+ 26  Komanso mofanana ndi zimene zinachitika mʼmasiku a Nowa,+ zidzachitikanso chimodzimodzi mʼmasiku a Mwana wa munthu.+ 27  Mʼmasiku amenewo anthu ankadya ndi kumwa. Amuna ankakwatira ndipo akazi ankakwatiwa mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchingalawa,+ ndipo Chigumula chinabwera nʼkuwononga anthu onsewo.+ 28  Chimodzimodzinso ndi zimene zinachitika mʼmasiku a Loti.+ Anthu ankadya, kumwa, kugula, kugulitsa, kudzala komanso kumanga. 29  Koma tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu, kumwamba kunagwa moto ndi sulufule ngati mvula nʼkuwononga anthu onse.+ 30  Zidzakhalanso chimodzimodzi pa tsikulo, pamene Mwana wa munthu adzaonekere.+ 31  Pa tsiku limenelo, munthu amene adzakhale padenga la nyumba koma katundu wake ali mʼnyumba, asadzatsike kukatenga katundu wakeyo. Chimodzimodzinso munthu amene adzakhale ali mʼmunda, asadzabwerere ku zinthu zimene wazisiya mʼmbuyo. 32  Kumbukirani mkazi wa Loti.+ 33  Aliyense wofunitsitsa kuteteza moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake adzausunga.+ 34  Ndithu ndikukuuzani, usiku umenewo anthu awiri adzagona limodzi pabedi. Mmodzi adzatengedwa, koma wina adzasiyidwa.+ 35  Akazi awiri adzakhala akupera limodzi pamphero. Mmodzi adzatengedwa, koma winayo adzasiyidwa.” 36  *—— 37  Choncho iwo anamufunsa kuti: “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti Ambuye?” Iye anawauza kuti: “Kumene kuli thupi lakufa, ziwombankhanga zidzasonkhananso komweko.”+

Mawu a M'munsi