Wolembedwa ndi Luka 20:1-47

  • Anthu anakayikira ulamuliro wa Yesu (1-8)

  • Fanizo la alimi opha anthu (9-19)

  • Mulungu komanso Kaisara (20-26)

  • Funso lokhudza kuuka kwa akufa (27-40)

  • Kodi Khristu ndi mwana wa Davide? (41-44)

  • Anachenjeza anthu kuti asamale ndi alembi (45-47)

20  Tsiku lina akuphunzitsa anthu mʼkachisi komanso kulengeza uthenga wabwino, kunabwera ansembe aakulu, alembi limodzi ndi akulu  nʼkudzamufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndi ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu?”+  Yesu anawayankha kuti: “Inenso ndikufunsani funso limodzi ndipo mundiyankhe:  Kodi ubatizo umene Yohane ankachita unachokera kumwamba kapena kwa anthu?”  Choncho iwo anayamba kukambirana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ iye atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’  Koma tikanena kuti, ‘Unachokera kwa anthu,’ anthu onsewa atiponya miyala, chifukwa iwo amakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yohane anali mneneri.”+  Choncho anayankha kuti sakudziwa kumene unachokera.  Yesu anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani amene anandipatsa ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.”  Ndiyeno iye anayamba kuuza anthuwo fanizo ili: “Munthu wina analima munda wa mpesa+ ndipo anausiya mʼmanja mwa alimi nʼkupita kudziko lina kumene anakhalako nthawi yaitali ndithu.+ 10  Ndiye nyengo ya zipatso itakwana, anatumiza kapolo wake kwa alimiwo kuti akamupatseko zina mwa zipatso zamʼmunda wa mpesawo. Koma alimiwo anamumenya nʼkumubweza chimanjamanja.+ 11  Koma iye anawatumiziranso kapolo wina. Ameneyonso anamumenya nʼkumuchitira zachipongwe,* ndipo anamubweza chimanjamanja. 12  Anatumizanso wachitatu. Ameneyunso anamuvulaza nʼkumuponya kunja. 13  Zitatero mwiniwake wa munda wa mpesa uja anati, ‘Ndichite chiyani tsopano? Chabwino, nditumiza mwana wanga wokondedwa.+ Mosakayikira mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’ 14  Alimiwo atamuona anayamba kukambirana kuti, ‘Eyaa, uyu ndi amene adzalandire cholowa. Tiyeni timuphe kuti cholowacho chikhale chathu.’ 15  Choncho anamutulutsa mʼmunda wa mpesawo nʼkumupha.+ Ndiye kodi mwiniwake wa munda wa mpesawo adzachita chiyani kwa alimiwo? 16  Iye adzabwera nʼkupha alimiwo ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa ena.” Atamva zimenezi iwo anati: “Ayi zisatero ndithu!” 17  Koma iye anawayangʼanitsitsa nʼkunena kuti: “Paja malemba amanena kuti, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana, wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.’*+ Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani? 18  Aliyense amene adzagwere pamwala umenewo adzaphwanyika.+ Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere, adzanyenyeka.” 19  Alembi ndi ansembe aakulu aja atazindikira kuti mufanizolo akunena za iwowo, anayesetsa kupeza mpata kuti amugwire ola lomwelo, koma ankaopa anthu.+ 20  Ndiyeno ataonetsetsa zochita zake, anatuma aganyu mwachinsinsi kuti akadzionetse ngati olungama, nʼcholinga choti akamupezere zifukwa pa zimene angalankhule,+ kuti akamupereke kuboma ndi kwa bwanamkubwa. 21  Choncho iwo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti zimene mumanena ndi kuphunzitsa ndi zolondola ndipo mulibe tsankho, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi. 22  Kodi nʼzololeka* kuti ife tizipereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?” 23  Koma Yesu anazindikira ndale zawo ndipo anawauza kuti: 24  “Ndionetseni khobidi la dinari.* Kodi nkhope ndi mawu ali pamenepo ndi za ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” 25  Iye anawauza kuti: “Choncho perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara,+ koma za Mulungu kwa Mulungu.”+ 26  Iwo analephera kumutapa mʼkamwa pa zimene ananenazi pamaso pa anthu, koma anadabwa ndi yankho lake moti anangokhala chete kusowa chonena. 27  Koma Asaduki ena, amene amanena kuti akufa sadzaukitsidwa,+ anabwera nʼkumufunsa kuti:+ 28  “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti, ‘Ngati mwamuna wamwalira nʼkusiya mkazi koma sanabereke ana, mchimwene wake akuyenera kutenga mkazi wamasiyeyo nʼkuberekera mchimwene wake uja ana.’+ 29  Ndiyeno panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira mkazi, koma anamwalira asanabereke mwana. 30  Wachiwirinso chimodzimodzi. 31  Kenako wachitatu anamukwatira. Zinachitika chimodzimodzi kwa amuna onse 7 aja, onse anamwalira osasiya ana. 32  Pamapeto pake mkazi uja anamwaliranso. 33  Kodi pamenepa, akufa akadzaukitsidwa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anamukwatira.” 34  Yesu anawayankha kuti: “Ana a mʼnthawi* ino amakwatira ndi kukwatiwa. 35  Koma amene aonedwa kuti ndi oyenerera kudzapeza moyo pa nthawi imeneyo nʼkudzaukitsidwa kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa.+ 36  Komanso iwo sadzafanso, chifukwa adzakhala ngati angelo. Iwo adzakhalanso ana a Mulungu pokhala ana a kuuka kwa akufa. 37  Koma zakuti akufa amaukitsidwa ngakhalenso Mose anafotokoza munkhani ya chitsamba cha minga, pamene ananena kuti Yehova* ndi ‘Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.’+ 38  Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, chifukwa kwa iye* onsewa ndi amoyo.”+ 39  Poyankha, ena mwa alembiwo ananena kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino.” 40  Ananena zimenezi chifukwa sanathenso kulimba mtima kuti amufunse funso lina ngakhale limodzi. 41  Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+ 42  Chifukwa Davideyo ananena mʼbuku la Masalimo kuti, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 43  mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”’+ 44  Choncho Davide anamutchula kuti Ambuye. Ndiye zikutheka bwanji kuti akhale mwana wake?” 45  Kenako anthu onse akumvetsera, iye anauza ophunzira akewo kuti: 46  “Chenjerani ndi alembi amene amakonda kuyendayenda atavala mikanjo komanso amakonda kupatsidwa moni mʼmisika. Amakondanso kukhala mʼmipando yakutsogolo* mʼmasunagoge komanso mʼmalo olemekezeka kwambiri pachakudya chamadzulo.+ 47  Iwo amalanda chuma cha akazi* amasiye ndipo amapereka mapemphero ataliatali pofuna kudzionetsera.* Anthu amenewa adzalandira chilango chowawa kwambiri.”*

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anamumenya nʼkumunyoza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu wa kona.”
Kapena kuti, “nʼzoyenera.”
Kapena kuti, “chifukwa iye amaona kuti.”
Kapena kuti, “mʼmipando yabwino kwambiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Iwo amadya nyumba za akazi.”
Kapena kuti, “ataliatali mwachiphamaso.”
Kapena kuti, “chilango champhamvu.”