Wolembedwa ndi Luka 21:1-38

  • Timakobidi tiwiri ta mkazi wamasiye (1-4)

  • CHIZINDIKIRO CHA ZINTHU ZAMʼTSOGOLO (5-36)

    • Nkhondo, zivomerezi zamphamvu, miliri, kusowa kwa chakudya (10, 11)

    • Yerusalemu adzazunguliridwa ndi magulu ankhondo (20)

    • Nthawi yoikidwiratu ya anthu amitundu ina (24)

    • Kubwera kwa Mwana wa munthu (27)

    • Fanizo la mtengo wa mkuyu (29-33)

    • Khalani maso (34-36)

  • Yesu anaphunzitsa mʼkachisi (37, 38)

21  Tsopano atakweza maso anaona anthu olemera akuponya zopereka zawo moponyera zopereka.*+  Kenako anaona mkazi wina wamasiye wosauka akuponya timakobidi tiwiri tatingʼono, tochepa mphamvu kwambiri.*+  Ndipo iye anati: “Ndithu ndikukuuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu, waponya zochuluka kuposa ena onse amene aponya ndalama zawo.+  Chifukwa onsewa aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene zikanamuthandiza pa moyo wake.”+  Nthawi ina, pamene anthu ena ankalankhula za kachisi, mmene anamukongoletsera ndi miyala yabwino kwambiri komanso mphatso zoperekedwa kwa Mulungu,+  iye ananena kuti: “Kunena za zinthu zimene mukuzionazi, masiku adzafika pamene sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa mwala unzake umene sudzagwetsedwa.”+  Ndiyeno anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti kwenikweni, ndipo chizindikiro chosonyeza kuti nthawi yoti zinthu zimenezi zichitike yatsala pangʼono chidzakhala chiyani?”+  Iye anayankha kuti: “Samalani kuti asadzakusocheretseni,+ chifukwa ambiri adzabwera mʼdzina langa nʼkumanena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ komanso adzanena kuti, ‘Nthawi ija yayandikira.’ Musadzawatsatire.+  Komanso, mukadzamva phokoso la nkhondo ndi zipolowe,* musadzachite mantha. Chifukwa zimenezi zikuyenera kuchitika choyamba, koma mapeto sadzafika nthawi yomweyo.”+ 10  Kenako anawauza kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina+ ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.+ 11  Kudzachitika zivomerezi zamphamvu ndipo kudzakhala miliri+ ndi njala mʼmalo osiyanasiyana. Kudzaoneka zinthu zoopsa ndipo kumwamba kudzaoneka zizindikiro zodabwitsa. 12  Koma zinthu zonsezi zisanachitike, anthu adzakugwirani nʼkukuzunzani+ ndipo adzakuperekani kumasunagoge ndi kundende. Adzakupititsani kwa mafumu ndi abwanamkubwa chifukwa cha dzina langa.+ 13  Zimenezi zidzakupatsani mpata woti muchitire umboni. 14  Choncho tsimikizirani mʼmitima yanu kuti musachite kukonzekera zoti mukayankhe podziteteza,+ 15  chifukwa ine ndidzakuuzani mawu oti munene komanso ndidzakupatsani nzeru zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.+ 16  Komanso makolo anu enieniwo, azichimwene anu, achibale anu komanso anzanu, adzakuperekani ndipo adzapha ena a inu.+ 17  Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.+ 18  Komatu ngakhale tsitsi limodzi lokha lamʼmutu mwanu silidzawonongeka.+ 19  Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.+ 20  Koma mukadzaona magulu ankhondo atazungulira Yerusalemu,+ mudzadziwe kuti mzindawu watsala pangʼono kuwonongedwa.+ 21  Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri,+ ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Amene ali mʼmadera akumidzi asadzalowe mumzindawo, 22  chifukwa amenewa ndi masiku opereka chiweruzo* kuti zonse zimene zinalembedwa zikwaniritsidwe. 23  Tsoka kwa akazi oyembekezera komanso oyamwitsa ana mʼmasiku amenewo!+ Chifukwa mʼdzikoli mudzakhala mavuto aakulu komanso mkwiyo pa anthu awa. 24  Anthu adzaphedwa ndi lupanga ndiponso kutengedwa ukapolo kupita nawo ku mitundu ina yonse.+ Anthu a mitundu ina adzapondaponda Yerusalemu mpaka nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu inawo zitakwanira.+ 25  Komanso padzakhala zizindikiro padzuwa, mwezi ndi nyenyezi.+ Padziko lapansi anthu a mitundu ina adzazunzika chifukwa chothedwa nzeru poona kuti nyanja ikuchita mkokomo komanso kuwinduka. 26  Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha komanso chifukwa choyembekezera zimene zichitikire dziko lapansi kumene kuli anthu, popeza mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. 27  Kenako adzaona Mwana wa munthu+ akubwera mumtambo ndi mphamvu ndiponso ulemerero waukulu.+ 28  Koma zinthu zimenezi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chikuyandikira.” 29  Atanena zimenezi, anawauza fanizo kuti: “Onetsetsani mtengo wa mkuyu ndi mitengo ina yonse.+ 30  Mukaona mitengo ikuphukira, mumadziwa ndithu kuti tsopano chilimwe chili pafupi. 31  Chimodzimodzi inunso, mukadzaona zinthu zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira. 32  Ndithu ndikukuuzani kuti mʼbadwo uwu sudzatha wonse kufa, mpaka zinthu zonse zitachitika.+ 33  Kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mawu anga adzakhalapo mpaka kalekale.+ 34  Koma samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri+ komanso nkhawa za moyo,+ kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa 35  ngati msampha.+ Chifukwa lidzafikira onse okhala padziko lonse lapansi. 36  Choncho khalani maso+ ndipo muzipemphera mopembedzera nthawi zonse,+ kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyenera kuchitika, komanso kuti mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.”+ 37  Masana Yesu ankaphunzitsa mʼkachisi, koma usiku ankapita kukagona kuphiri la Maolivi. 38  Ndipo anthu onse ankalawirira mʼmawa kwambiri kupita kwa iye kukachisi kuti akamumvetsere.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mʼbokosi la zopereka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “malepitoni awiri.” Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “zipwirikiti.”
Kapena kuti, “masiku obwezera chilango.”