Wolembedwa ndi Luka 22:1-71

  • Ansembe anakonza chiwembu kuti aphe Yesu (1-6)

  • Kukonzekera Pasika womaliza (7-13)

  • Kuyambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye (14-20)

  • “Wondipereka ndili naye limodzi patebulo pompano” (21-23)

  • Anakangana kwambiri za amene anali wamkulu (24-27)

  • Pangano la Yesu la ufumu (28-30)

  • Ananeneratu kuti Petulo adzamukana (31-34)

  • Kufunika kokhala okonzeka; malupanga awiri (35-38)

  • Pemphero la Yesu paphiri la Maolivi (39-46)

  • Yesu anagwidwa (47-53)

  • Petulo anakana Yesu (54-62)

  • Yesu anachitiridwa zachipongwe (63-65)

  • Anamupititsa ku Khoti Lalikulu la Ayuda (66-71)

22  Tsopano Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa, chimene chinkadziwikanso kuti Pasika,+ chinali chitayandikira.+  Komanso ansembe aakulu ndi alembi ankafunafuna njira yabwino yoti aphere Yesu,+ chifukwa ankaopa anthu.+  Koma Satana analowa mwa Yudasi, amene ankadziwika kuti Isikariyoti, mmodzi wa ophunzira 12 aja.+  Iye anapita kukakambirana ndi ansembe aakulu ndi oyangʼanira kachisi za mmene angamuperekere kwa iwo.+  Iwo anasangalala ndipo anagwirizana kuti amupatse ndalama zasiliva.+  Choncho iye anavomereza, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino kuti amupereke kwa iwo popanda gulu la anthu pafupi.  Tsopano tsiku la Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa linafika, tsiku limene nsembe ya Pasika inkayenera kuperekedwa.+  Yesu anatumiza Petulo ndi Yohane nʼkuwauza kuti: “Pitani mukatikonzere Pasika kuti tidye.”+  Iwo anamufunsa kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti?” 10  Iye anawayankha kuti: “Mukalowa mumzinda, mwamuna wina akakumana nanu atasenza mtsuko wa madzi. Mukamutsatire mʼnyumba imene akalowe.+ 11  Ndipo mukauze mwininyumba imeneyo kuti, ‘Mphunzitsi wanena kuti: “Chipinda cha alendo chili kuti mmene ine ndingadyeremo Pasika limodzi ndi ophunzira anga?”’ 12  Ndiyeno munthu ameneyo akakuonetsani chipinda chachikulu chamʼmwamba chokonzedwa bwino. Mukakonzere mmenemo.” 13  Choncho ananyamuka ndipo zinachitikadi ndendende mmene iye anawauzira. Ndipo anakonza zinthu zonse zofunika pa Pasika. 14  Nthawi itakwana, anakhala patebulo la chakudya limodzi ndi atumwi ake.+ 15  Ndiyeno anawauza kuti: “Ndakhala ndikulakalaka kwambiri kuti ndidye Pasika uyu limodzi ndi inu ndisanayambe kuzunzika. 16  Chifukwa ndikukuuzani kuti sindidzadyanso Pasika mpaka zonse zimene Pasikayu akuimira zitakwaniritsidwa mu Ufumu wa Mulungu.” 17  Ndiyeno analandira kapu nʼkuyamika, kenako anati: “Landirani kapu iyi, ndipo nonse mumwe mopatsirana. 18  Ndithu ndikukuuzani, kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa chochokera ku mphesa mpaka Ufumu wa Mulungu utabwera.” 19  Kenako anatenga mkate.+ Atayamika, anaunyemanyema nʼkuwapatsa ndipo anati: “Mkate uwu ukuimira thupi langa+ limene likuperekedwa chifukwa cha inu.+ Muzichita zimenezi pondikumbukira.”+ 20  Anachitanso chimodzimodzi ndi kapu atadya chakudya chamadzulocho. Iye anati: “Kapu iyi ikuimira pangano latsopano+ limene linakhazikitsidwa pogwiritsa ntchito magazi anga,+ amene adzakhetsedwe chifukwa cha inu.+ 21  Koma taonani! Wondipereka ndili naye limodzi patebulo pompano.+ 22  Chifukwa Mwana wa munthu achoka mogwirizana ndi zimene zinanenedweratu.+ Koma tsoka kwa munthu amene akumupereka!”+ 23  Choncho anayamba kukambirana pakati pawo za amene anakonza chiwembu chimenecho.+ 24  Kenako anayamba kukangana kwambiri za amene anali wamkulu kwambiri.+ 25  Koma Yesu anawauza kuti: “Mafumu a anthu a mitundu ina amachita ulamuliro pa anthu awo, ndipo amene ali ndi mphamvu pa anthuwo amadziwika kuti ndi anthu amene amachitira ena zabwino.+ 26  Inu musakhale otero.+ Koma amene ali wamkulu kwambiri pa nonsenu akhale ngati wamngʼono+ kwambiri pa nonsenu, ndipo amene ali mtsogoleri akhale ngati wotumikira. 27  Kodi wamkulu ndi ndani, amene akudya patebulo kapena amene akutumikira? Kodi si amene akudya patebulo? Koma ine ndili pakati panu ngati wotumikira.+ 28  Komabe, inu ndi amene mwakhalabe ndi ine+ mʼmayesero anga.+ 29  Choncho ndikuchita nanu pangano, mofanana ndi mmene Atate wanga wachitira pangano la ufumu ndi ine,+ 30  kuti mukadye ndi kumwa patebulo langa mu Ufumu wanga,+ komanso kuti mukakhale mʼmipando yachifumu+ kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.+ 31  Simoni, Simoni! Ndithu Satana akufuna kuti nonsenu akupeteni ngati tirigu.+ 32  Koma ine ndakupempherera kuti chikhulupiriro chako chisathe.+ Choncho iwenso ukabwerera, ukalimbikitse abale ako.”+ 33  Kenako iye anauza Yesu kuti: “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu limodzi kundende kapena kufa nanu limodzi.”+ 34  Koma iye anati: “Ndikukuuza iwe Petulo, tambala asanalire lero, undikana katatu kuti sukundidziwa.”+ 35  Yesu anauzanso ophunzirawo kuti: “Pamene ndinakutumizani opanda chikwama cha ndalama, thumba la chakudya kapena nsapato,+ kodi munasowa kanthu?” Iwo anati: “Ayi!” 36  Kenako anawauza kuti: “Koma tsopano amene ali ndi chikwama cha ndalama achitenge, chimodzimodzinso thumba la chakudya. Ndipo amene alibe lupanga agulitse malaya ake akunja nʼkugula lupanga. 37  Chifukwa ndikukuuzani kuti zimene zinalembedwa ziyenera kukwaniritsidwa mwa ine, zakuti, ‘Iye anaikidwa mʼgulu la anthu osamvera malamulo.’+ Zili choncho chifukwa zimene zinanenedwa zokhudza ine zikukwaniritsidwa.”+ 38  Ndiyeno iwo anati: “Ambuye, onani! Tili ndi malupanga awiri awa.” Iye anawauza kuti: “Amenewa ndi okwanira.” 39  Atachoka kumeneko anapita kuphiri la Maolivi ngati mmene ankachitira nthawi zonse ndipo ophunzira ake nawonso anamutsatira.+ 40  Atafika pamalowo anauza ophunzirawo kuti: “Pitirizani kupemphera kuti musalowe mʼmayesero.”+ 41  Iye anachoka pamene panali ophunzirawo nʼkuyenda kamtunda, kutalika kwake ngati pamene pangagwere mwala munthu atauponya. Kumeneko anagwada nʼkuyamba kupemphera 42  kuti: “Atate, ngati mukufuna, ndichotsereni kapu iyi. Komatu zimene mukufuna zichitike, osati zofuna zanga.”+ 43  Atatero mngelo wochokera kumwamba anaonekera kwa iye nʼkumulimbikitsa.+ 44  Koma anazunzika koopsa mumtima mwake, moti anapitiriza kupemphera ndi mtima wonse+ ndipo thukuta lake linkaoneka ngati madontho amagazi amene akugwera pansi. 45  Atanyamuka pamene amapempherapo nʼkupita kwa ophunzira aja, anawapeza atagona chifukwa anali atafooka ndi chisoni.+ 46  Iye anawauza kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukugona? Dzukani ndipo mupitirize kupemphera kuti musalowe mʼmayesero.”+ 47  Mawu adakali mʼkamwa, panafika gulu la anthu limodzi ndi Yudasi, mmodzi wa ophunzira 12 aja, akuwatsogolera. Ndiyeno Yudasi anapita pamene panali Yesu kuti akamukise.*+ 48  Koma Yesu anamufunsa kuti: “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa munthu ndi kisi?” 49  Anthu amene anali naye pafupi ataona zimene zinkachitika anati: “Ambuye, kodi tiwateme ndi lupanga?” 50  Mmodzi wa iwo anatemadi kapolo wa mkulu wa ansembe nʼkuduliratu khutu lake lakumanja.+ 51  Koma Yesu anati: “Musachite zimenezi.” Ndipo anagwira khutu lija nʼkumuchiritsa. 52  Ndiyeno Yesu anafunsa ansembe aakulu, oyangʼanira kachisi ndi akulu amene anabwera kudzamugwira kuti: “Bwanji mwabwera ndi malupanga ndi zibonga ngati mukudzalimbana ndi wachifwamba?+ 53  Tsiku ndi tsiku ndinali nanu mʼkachisi+ koma simunandigwire.+ Koma ino tsopano ndi nthawi yanu komanso nthawi ya ulamuliro wamdima.”+ 54  Zitatero anamugwira nʼkumutenga+ ndipo anakamulowetsa mʼnyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petulo ankawatsatira chapatali.+ 55  Atasonkha moto mkati mwa bwalo nʼkukhala pansi onse pamodzi, Petulo nayenso anakhala nawo pamenepo.+ 56  Koma mtsikana wina wantchito atamuona atakhala pafupi ndi moto wowala, anamuyangʼanitsitsa nʼkunena kuti: “Bambo awanso anali naye limodzi.” 57  Koma iye anakana kuti: “Mtsikana iwe, ameneyu ine sindikumudziwa.” 58  Patapita kanthawi pangʼono, munthu wina anamuona nʼkunena kuti: “Iwenso uli mʼgulu la ophunzira ake.” Koma Petulo anati: “Munthu iwe, ayi si ine.”+ 59  Patapita pafupifupi ola limodzi, munthu winanso anayamba kunena motsimikiza kuti: “Ndithu sindikukayika, munthu uyunso anali naye limodzi, komanso iyeyu ndi Mgalileya!” 60  Koma Petulo anati: “Munthu iwe, ine sindikudziwa zimene ukunena.” Nthawi yomweyo mawu ali mʼkamwa, tambala analira. 61  Zitatero Ambuye anacheuka nʼkuyangʼana Petulo, ndipo Petulo anakumbukira mawu amene Ambuye anamuuza aja akuti: “Tambala asanalire lero, undikana katatu.”+ 62  Kenako Petulo anatuluka panja nʼkuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri. 63  Tsopano amuna amene anagwira Yesu aja anayamba kumuchitira zachipongwe+ komanso kumumenya.+ 64  Iwo ankamuphimba kumaso nʼkumamufunsa kuti: “Losera. Wakumenya ndi ndani?” 65  Ndipo anapitiriza kunena zinthu zambiri zomunyoza. 66  Kenako kutacha, bungwe la akulu, kuphatikizapo ansembe aakulu komanso alembi, anasonkhana pamodzi,+ ndipo anamutengera kuholo ya Khoti Lalikulu la Ayuda.* Kumeneko iwo anati: 67  “Tiuze ngati ndiwe Khristu.”+ Koma iye anawayankha kuti: “Ngakhale ndikuuzeni, simukhulupirira. 68  Komanso nditakufunsani, simungathe nʼkomwe kuyankha. 69  Koma kuyambira panopa mpaka mʼtsogolo, Mwana wa munthu+ adzakhala kudzanja lamanja lamphamvu la Mulungu.”+ 70  Atanena zimenezi onse anati: “Kodi ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?” Iye anawayankha kuti: “Inunso mukunena nokha kuti ndine amene.” 71  Iwo anati: “Tifuniranjinso umboni wina? Apatu tadzimvera tokha kuchokera pakamwa pake.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “akamupsompsone.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Sanihedirini.”