Machitidwe a Atumwi 22:1-30
22 “Anthu inu, abale anga ndi abambo anga, mvetserani mawu anga odziteteza.”+
2 Atamva kuti akulankhula nawo mʼChiheberi, onse anangoti zii, ndipo iye anati:
3 “Inetu ndine Myuda,+ wobadwira ku Tariso wa ku Kilikiya,+ koma ndinaphunzitsidwa ndi Gamaliyeli+ mumzinda womwe uno. Anandiphunzitsa kutsatira kwambiri Chilamulo cha makolo+ athu. Ndipo ndinali wodzipereka potumikira Mulungu ngati mmene nonsenu mulili lero.+
4 Ndinkazunza otsatira Njira imeneyi mpaka kuwapha. Ndinkamanga amuna ndi akazi nʼkukawapereka kundende.+
5 Ndipotu mkulu wa ansembe ndi bungwe lonse la akulu angandichitire umboni. Kwa amenewa nʼkumene ndinapezanso makalata ondiloleza kuti ndikamange abale ku Damasiko. Ndinanyamuka kuti ndikagwire anthu omwe anali kumeneko nʼkuwabweretsa ku Yerusalemu atamangidwa kuti adzapatsidwe chilango.
6 Koma ndili mʼnjira, nditatsala pangʼono kufika ku Damasiko, dzuwa lili pamutu, mwadzidzidzi kunawala kwambiri. Kuwala kumeneku kunali kochokera kumwamba ndipo kunazungulira pamene ine ndinali.+
7 Ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akuti: ‘Saulo! Saulo! Nʼchifukwa chiyani ukundizunza?’
8 Ine ndinayankha kuti, ‘Ndinu ndani Mbuyanga?’ Ndipo anandiuza kuti, ‘Ndine Yesu wa ku Nazareti, amene iwe ukumuzunza.’
9 Amuna amene ndinali nawo anaona kuwalako, koma sanamve mawu amene ankalankhula ndi inewo.
10 Ndiye ine ndinati, ‘Nditani Ambuye?’ Ambuyewo anandiuza kuti, ‘Nyamuka ndipo upite ku Damasiko. Kumeneko ukauzidwa zonse zimene zakonzedwa kuti uchite.’+
11 Koma popeza sindinkatha kuona chilichonse chifukwa cha ulemerero wa kuwalako, anthu amene ndinali nawo aja, anandigwira dzanja mpaka kukafika ku Damasiko.
12 Ndiyeno Hananiya, munthu woopa Mulungu mogwirizana ndi Chilamulo, amene anali ndi mbiri yabwino pakati pa Ayuda onse akumeneko,
13 anabwera. Iye anaima chapafupi nʼkunena kuti: ‘Mʼbale wanga Saulo, yambanso kuona!’ Nthawi yomweyo ndinakweza maso anga nʼkumuona.+
14 Ndiyeno iye anati: ‘Mulungu wa makolo athu wakusankha kuti udziwe chifuniro chake, uone wolungamayo+ ndiponso umve mawu apakamwa pake.
15 Chifukwa udzakhala mboni yake kwa anthu onse pa zinthu zimene waona komanso kumva.+
16 Ndiye ukuchedweranji? Nyamuka ubatizidwe nʼkuchotsa machimo ako+ poitanira pa dzina lake.’+
17 Koma nditabwerera ku Yerusalemu+ nʼkuyamba kupemphera mʼkachisi, ndinaona masomphenya.
18 Mʼmasomphenyawo ndinaona Ambuye akundiuza kuti, ‘Tuluka mu Yerusalemu mwamsanga, chifukwa iwo sadzamva uthenga wako wonena za ine.’+
19 Ndipo ine ndinanena kuti, ‘Ambuye, iwowo akudziwa bwino kuti ndinkapita mʼmasunagoge nʼkumatsekera mʼndende ndiponso kukwapula anthu amene ankakukhulupirirani.+
20 Komanso pamene Sitefano, mboni yanu ankaphedwa, ine ndinali pomwepo ndipo ndinavomereza. Ndi inenso amene ndinkayangʼanira malaya akunja a anthu amene ankamuphawo.’+
21 Koma anandiuzabe kuti, ‘Nyamuka, chifukwa ndidzakutumiza kutali kwa anthu a mitundu ina.’”+
22 Iwo ankamumvetsera mpaka pa mawu amenewa. Koma kenako anafuula kuti: “Munthu ameneyu asapezekenso padziko lapansi! Sakuyenera kukhala ndi moyo!”
23 Koma popeza ankafuula komanso kuponya mʼmwamba malaya awo akunja ndi fumbi,+
24 mkulu wa asilikali analamula kuti alowe naye kumpanda wa asilikali. Iye anati ayenera kumufunsa mafunso kwinaku akumʼkwapula kuti adziwe chimene chachititsa kuti anthu azimukuwiza* choncho.
25 Koma atamugoneka kuti amukwapule, Paulo anafunsa mtsogoleri wa asilikali amene anaima pamenepo kuti: “Kodi malamulo amakulolani kukwapula nzika ya Roma mlandu wake usanazengedwe?”+
26 Mtsogoleri wa asilikaliyo atamva zimenezi, anapita kwa mkulu wa asilikali nʼkukamuuza kuti: “Mukufuna kuchita chiyani? Munthuyutu ndi nzika ya Roma.”
27 Zitatero mkulu wa asilikaliyo anabwera nʼkunena kuti: “Tandiuza, kodi nʼzoona kuti ndiwe nzika ya Roma?” Iye anati: “Inde.”
28 Mkulu wa asilikaliyo anati: “Ine ndinagula ufulu wokhala nzika ndi ndalama zambiri.” Paulo anati: “Koma ine wanga ndinachita kubadwa nawo.”+
29 Nthawi yomweyo amuna amene ankafuna kumufunsa mafunso, uku akumukwapula, anachoka nʼkumusiya. Nayenso mkulu wa asilikali uja anachita mantha atadziwa kuti munthu amene anamumangayo ndi nzika ya Roma.+
30 Tsiku lotsatira, pofuna kudziwa chenicheni chimene Ayudawo ankamuimbira mlandu, anamutulutsa. Atatero analamula ansembe aakulu ndi Khoti Lalikulu la Ayuda kuti asonkhane. Ndiyeno anabweretsa Paulo nʼkumuimika pakati pawo.+
Mawu a M'munsi
^ Ena amati, “kumukuwa kapena kumuwowoza.”