Machitidwe a Atumwi 8:1-40

  • Saulo ankazunza anthu (1-3)

  • Utumiki wa Filipo unkayenda bwino ku Samariya (4-13)

  • Petulo ndi Yohane anatumizidwa ku Samariya (14-17)

  • Simoni ankafuna kugula mzimu woyera (18-25)

  • Nduna ya ku Itiyopiya (26-40)

8  Saulo anavomereza zoti Sitefano aphedwe.+ Tsiku limenelo, mpingo umene unali ku Yerusalemu unayamba kuzunzidwa koopsa. Choncho ophunzira onse, kupatula atumwi okha, anabalalika nʼkupita mʼzigawo za Yudeya ndi Samariya.+  Koma anthu ena oopa Mulungu anatenga Sitefano nʼkukamuika mʼmanda, ndipo anamulira kwambiri.  Saulo anayamba kuzunza mpingo mwankhanza. Ankalowa mʼnyumba iliyonse nʼkumakokera panja amuna ndi akazi omwe, ndipo ankawapititsa kundende.+  Komabe, anthu amene anabalalika aja ankalalikira uthenga wabwino wa mawu a Mulungu mʼmadera omwe anapita.+  Filipo anapita mumzinda wa Samariya+ nʼkuyamba kulalikira za Khristu kwa anthu akumeneko.  Anthu ambiri ankamvetsera zimene Filipo ankanena. Onse ankamvetsera ndiponso kuona zizindikiro zimene iye ankachita.  Kumeneko kunali anthu ambiri omwe anali ndi mizimu yoipa ndipo inkafuula nʼkutuluka.+ Anthu ambiri akufa ziwalo ndiponso olumala ankachiritsidwa.  Choncho anthu amumzindawo anasangalala kwambiri.  Mumzindawo munalinso munthu wina dzina lake Simoni. Izi zisanachitike, iye ankachita zamatsenga nʼkumadabwitsa anthu onse a ku Samariya ndipo ankadzitama kwambiri. 10  Anthu onse, ana ndi akulu omwe, ankachita naye chidwi ndipo ankanena kuti: “Munthu uyu ali ndi mphamvu yaikulu ya Mulungu.” 11  Ankachita naye chidwi chifukwa kwa nthawi yaitali anawadabwitsa ndi zamatsenga zakezo. 12  Koma iwo atakhulupirira Filipo, amene ankalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu+ ndiponso wonena za dzina la Yesu Khristu, ankabatizidwa, amuna ndi akazi omwe.+ 13  Simoni uja nayenso anakhala wokhulupirira. Atabatizidwa, sankasiyana ndi Filipo+ kulikonse. Moti ankadabwa poona zizindikiro ndiponso ntchito zamphamvu ndi zazikulu zomwe zinkachitika. 14  Atumwi ku Yerusalemu atamva kuti anthu a ku Samariya alandira mawu a Mulungu,+ anawatumizira Petulo ndi Yohane. 15  Iwo anapitadi kumeneko ndipo anawapempherera kuti alandire mzimu woyera.+ 16  Pa nthawiyi nʼkuti aliyense asanalandire mzimu woyera, koma atangobatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu.+ 17  Choncho atumwiwo anayamba kuwagwira anthuwo pamutu,*+ ndipo analandira mzimu woyera. 18  Ndiyeno Simoni ataona kuti atumwiwo akangowagwira anthuwo ankalandira mzimu woyera, anafuna kuwapatsa ndalama. 19  Iye ananena kuti: “Inenso mundipatseko mphamvu imeneyi, kuti aliyense amene ndingamugwire pamutu* azilandira mzimu woyera.” 20  Koma Petulo anamuuza kuti: “Siliva wakoyo uwonongeke naye limodzi, chifukwa ukuganiza kuti mphatso yaulere ya Mulungu ungaigule ndi ndalama.+ 21  Ntchito imeneyi sikukukhudza ndipo ulibe gawo lililonse chifukwa mtima wako si wowongoka pamaso pa Mulungu. 22  Choncho lapa zoipa zimene wachitazi ndipo upemphe Yehova* mochonderera kuti ngati nʼkotheka, akukhululukire chifukwa cha maganizo oipa amene ali mumtima mwakowa. 23  Ndaona kuti ndiwe poizoni wowawa* ndiponso kapolo wa zinthu zachinyengo.” 24  Simoni anayankha kuti: “Ndipempherereni kwa Yehova* mochonderera kuti zonse zimene mwanenazi zisandichitikire.” 25  Choncho atamaliza kuchitira umboni mokwanira ndiponso kulankhula mawu a Yehova,* anabwerera ku Yerusalemu. Pobwerera ankalengeza uthenga wabwino mʼmidzi yambiri ya ku Samariya.+ 26  Koma mngelo wa Yehova*+ analankhula kwa Filipo kuti: “Nyamuka ndipo upite kumʼmwera, kumsewu wochokera ku Yerusalemu kupita ku Gaza.” (Umenewu ndi msewu wa mʼchipululu.) 27  Choncho, ananyamuka nʼkupita ndipo anakumana ndi nduna ya ku Itiyopiya. Munthuyu anali ndi udindo waukulu ndipo ankathandiza Kandake, mfumukazi ya Itiyopiya. Ankayangʼaniranso chuma chonse cha mfumukaziyo. Iye anapita ku Yerusalemu kukalambira Mulungu.+ 28  Tsopano anali pa ulendo wobwerera kwawo atakhala mʼgaleta lake ndipo ankawerenga mokweza ulosi wa mneneri Yesaya. 29  Ndiyeno mzimu unauza Filipo kuti: “Pita ukayandikire galeta lakelo.” 30  Filipo anathamanga nʼkumayenda mʼmbali mwa galetalo ndipo anamumva akuwerenga mokweza ulosi wa mneneri Yesaya. Filipo anamufunsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazo?” 31  Iye anayankha kuti: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulira?” Choncho anapempha Filipo kuti akwere nʼkukhala naye mʼgaletamo. 32  Mawu a mʼMalemba amene ankawerengawo anali akuti: “Anamutengera kumalo oti akamuphere ngati nkhosa. Ndipo mofanana ndi mwana wa nkhosa amene wangokhala chete pamene akufuna kumumeta ubweya, sanatsegule pakamwa pake.+ 33  Pamene ankamuchititsa manyazi, sanamuchitire zachilungamo.+ Ndi ndani angafotokoze mwatsatanetsatane mʼbadwo wa makolo ake? Chifukwa moyo wake wachotsedwa padziko lapansi.”+ 34  Ndiyeno ndunayo inafunsa Filipo kuti: “Ndiuzeni chonde, kodi mneneriyu akunena za ndani? Za iyeyo kapena za munthu wina?” 35  Zitatero, Filipo anayamba kumuuza uthenga wabwino wonena za Yesu, ndipo anayambira palemba lomweli. 36  Akuyenda choncho mumsewumo, anapeza madzi ambiri ndipo nduna ija inati: “Taonani, Madzitu awo! Chikundiletsa kubatizidwa nʼchiyani?” 37 *⁠—— 38  Atatero analamula kuti galetalo liime. Kenako Filipo ndi nduna ija anatsika nʼkulowa mʼmadzimo, ndipo Filipo anabatiza ndunayo. 39  Atatuluka mʼmadzimo mzimu wa Yehova* unamuchotsapo Filipo mwamsanga ndipo nduna ija sinamuonenso, koma inapitiriza ulendo wake ikusangalala. 40  Koma Filipo anapezeka ali ku Asidodi, ndipo anayamba kulengeza uthenga wabwino mʼmizinda yonse yamʼderali mpaka anakafika ku Kaisareya.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kuwaika manja anthuwo.”
Kapena kuti, “ndingamuike manja.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndulu yowawa.”