Malaki 1:1-14

  • Yehova amakonda anthu ake (1-5)

  • Ansembe ankapereka nsembe zosalongosoka (6-14)

    • Dzina la Mulungu lidzakhala lalikulu pakati pa anthu a mitundu ina (11)

1  Uthenga wokhudza Isiraeli: Awa ndi mawu a Yehova opita kwa Isiraeli kudzera mwa Malaki:*  Yehova wanena kuti: “Ine ndimakukondani anthu inu.”+ Koma inu mwanena kuti: “Mwasonyeza bwanji kuti mumatikonda?” “Kodi Esau sanali mchimwene wake wa Yakobo?+ Koma ine ndinakonda Yakobo,” watero Yehova.  “Esau ndinadana naye.+ Mapiri ake ndinawasandutsa bwinja+ ndipo cholowa chake ndinachisandutsa malo okhala mimbulu yamʼchipululu.”+  “Ngakhale kuti Edomu akunena kuti, ‘Ife tawonongedwa, koma tibwerera nʼkukamanga malo athu owonongedwawo,’ Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Iwo apita kukamanga, koma ine ndikagwetsa. Anthu adzatchula malo awowo kuti “dera la zoipa” ndipo iwowo adzatchedwa “anthu okanidwa ndi Yehova mpaka kalekale.”+  Inu mudzaona zimenezi ndi maso anu ndipo mudzati: “Yehova atamandike mʼdera lonse la Isiraeli.”’”  “‘Mwana amalemekeza bambo ake+ ndipo wantchito amalemekeza mbuye wake. Ngati ine ndili bambo,+ ulemu wanga uli kuti?+ Ngati ndili ambuye,* nʼchifukwa chiyani simundiopa?’* ndikutero ine Yehova wa magulu ankhondo akumwamba kwa inu ansembe amene mukunyoza dzina langa.+ ‘Koma inu mukunena kuti: “Kodi dzina lanu talinyoza bwanji?”’  ‘Mwalinyoza popereka nsembe* zodetsedwa paguwa langa lansembe.’ ‘Inu mukunena kuti: “Takudetsani bwanji?”’ ‘Mwandidetsa ponena kuti: “Tebulo la Yehova+ ndi lonyozeka.”  Mukapereka nsembe nyama yakhungu, mumanena kuti: “Palibe cholakwika.” Mukapereka nsembe nyama yolumala kapena yodwala, mumati: “Palibe vuto.”’”+ “Pitani nazo kwa bwanamkubwa wanu. Kodi akakondwera nanu? Kapena kodi akakulandirani bwino?” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.  “Tsopano khazikani pansi mtima wa Mulungu kuti achite chifundo. Kodi nsembe zimene mukuperekazi zingachititse kuti ndisangalale nanu?” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 10  “Ndipo ndani wa inu amene angatseke zitseko za kachisi popanda malipiro?+ Mukayatsa moto paguwa langa lansembe, mumafuna kulandira malipiro.+ Ine sindikukondwera nanu, ndipo nsembe zimene mukundipatsa ngati mphatso sizikundisangalatsa,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 11  “Kuchokera kotulukira dzuwa kukafika kumene limalowera,* dzina langa lidzakwezeka pakati pa anthu a mitundu ina.+ Kulikonse anthu azidzapereka nsembe zautsi ndiponso nsembe zina ngati mphatso zovomerezeka polemekeza dzina langa. Adzachita izi chifukwa dzina langa lidzakwezeka pakati pa anthu a mitundu inawo,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 12  “Koma inu mukulinyoza*+ ponena kuti, ‘Palibe vuto kudetsa tebulo la Yehova, ndipo zopereka kapena kuti chakudya chimene chili pamenepo nʼchonyozeka.’+ 13  Mumanenanso kuti, ‘Koma ndiye nʼzotopetsa bwanji!’ Ndipo mumanunkhiza nsembezo monyansidwa,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. “Inu mumabweretsa nyama zobedwa, zolumala ndi zodwala. Mumabweretsa zimenezi ngati mphatso. Kodi ine ndingalandire nsembe zoterezi?”+ watero Yehova. 14  “Wotembereredwa ndi aliyense wochita zachinyengo, amene ali ndi nyama yabwinobwino yamphongo pa ziweto zake koma amalonjeza nʼkupereka nsembe nyama yachilema kwa Yehova. Ine ndine Mfumu yaikulu+ ndipo dzina langa lidzaopedwa pakati pa anthu a mitundu ina,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza “Mthenga Wanga.”
Kapena kuti, “ambuye wamkulu.”
Kapena kuti, “simundilemekeza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkate.”
Kapena kuti, “Kuchokera kumʼmawa mpaka kumadzulo.”
Mabaibulo ena amati, “mukundinyoza.”