Malaki 3:1-18

  • Ambuye woona anabwera kudzayeretsa kachisi (1-5)

    • Mthenga wa pangano (1)

  • Anawalimbikitsa kuti abwerere kwa Yehova (6-12)

    • Yehova sasintha (6)

    • “Bwererani kwa ine ndipo ine ndidzabwerera kwa inu” (7)

    • ‘Bweretsani chakhumi chonse ndipo Yehova adzakudalitsani’ (10)

  • Anthu olungama ndiponso anthu oipa (13-18)

    • Buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pa Mulungu (16)

    • Kusiyana pakati pa wolungama ndi woipa (18)

3  “Taonani! Ine ndikutumiza mthenga wanga ndipo adzandikonzera njira.+ Mwadzidzidzi, Ambuye woona, amene anthu inu mukumufunafuna, adzabwera kukachisi wake.+ Ndiponso mthenga wa pangano amene mukumuyembekezera mosangalala adzabwera. Iye adzabwera ndithu,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 2  “Ndani adzapirire pa tsiku limene adzabwere? Ndipo ndani adzaimirire iye akadzaonekera? Iye adzakhala ngati moto wa woyenga zitsulo komanso ngati sopo+ wa ochapa zovala. 3  Iye adzakhala pansi ngati woyenga zitsulo ndiponso ngati woyeretsa siliva.+ Adzayeretsa ana a Levi ndipo adzawayeretsa ngati golide ndi siliva. Akamadzapereka nsembe zawo ngati mphatso, Yehova adzaona kuti nsembe zawozo akuzipereka molungama. 4  Nsembe zimene Yuda ndi Yerusalemu adzapereke monga mphatso, zidzasangalatsa Yehova, ngati mmene zinalili kalekale ndiponso nthawi zamakedzana.+ 5  Ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni. Sindidzazengereza kupereka umboni wotsutsa amatsenga,+ achigololo, olumbira monama+ komanso amene amachitira zachinyengo munthu waganyu,+ mkazi wamasiye ndi mwana wamasiye*+ komanso amene amakana kuthandiza alendo.+ Anthu amenewa sakundiopa,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 6  “Ine ndine Yehova ndipo sindisintha.*+ Inu ndinu ana a Yakobo ndipo simunatheretu. 7  Kuyambira mʼmasiku a makolo anu mwakhala mukupatuka pa malamulo anga ndipo simunawatsatire.+ Bwererani kwa ine ndipo ine ndidzabwerera kwa inu,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Koma inu mukunena kuti: “Tingabwerere bwanji?” 8  “Kodi munthu wamba angabere Mulungu? Komatu inu mukundibera.” Inu mukunena kuti: “Takuberani bwanji?” “Mukundibera pa nkhani ya chakhumi ndi zopereka. 9  Ndinu otembereredwa* chifukwa mukundibera. Mtundu wanu wonsewu ukuchita zimenezi. 10  Bweretsani gawo limodzi pa magawo 10 alionse* a zinthu zanu nʼkuziika mosungiramo zinthu zanga,+ kuti mʼnyumba mwanga mukhale chakudya.+ Ndiyeseni chonde pa nkhani imeneyi, kuti muone ngati sindidzakutsegulirani mageti akumwamba+ nʼkukukhuthulirani madalitso mpaka simudzasowa kanthu,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 11  “Ine sindidzalola kuti dzombe lizidzawononga mbewu zamʼmunda mwanu. Mitengo ya mpesa ya mʼmunda mwanu izidzabereka nthawi zonse,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 12  “Mitundu ina yonse ya anthu idzanena kuti ndinu osangalala,+ chifukwa mudzakhala dziko losangalatsa,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 13  “Inu mwandinenera mawu achipongwe,” watero Yehova. Ndipo mukunena kuti: “Ife takunenerani zachipongwe zotani?”+ 14  “Inu mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu nʼkopanda phindu.+ Tapindula chiyani chifukwa chomutumikira ndiponso chifukwa choyenda mwachisoni pamaso pa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba? 15  Panopa tikuona kuti anthu odzikuza akusangalala. Komanso anthu ochita zoipa, zinthu zikuwayendera bwino.+ Iwo amayesa Mulungu koma sakulandira chilango.’” 16  Pa nthawi imeneyo anthu oopa Yehova ankalankhulana, aliyense ndi mnzake, ndipo Yehova anatchera khutu nʼkumamvetsera. Buku la chikumbutso, lonena za anthu oopa Yehova ndi anthu amene ankaganizira za dzina lake,* linayamba kulembedwa pamaso pake.+ 17  “Iwo adzakhala anthu anga,+ pa tsiku limene ndidzawasandutse chuma chapadera,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. “Ndidzawachitira chifundo ngati mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira.+ 18  Ndipo mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa+ ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sakumutumikira.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mwana wopanda bambo.”
Kapena kuti, “sindinasinthe.”
Mabaibulo ena amati, “Mukunditemberera.”
Kapena kuti, “chakhumi chonse.”
Kapena kuti, “ankasinkhasinkha.” Mabaibulo ena amati, “ankaona kuti dzina lake ndi lamtengo wapatali.”