Malaki 4:1-6

  • Eliya adzabwera tsiku la Yehova lisanafike (1-6)

    • ‘Dzuwa la chilungamo lidzawala’ (2)

4  “Taonani! Tsiku loyaka ngati ngʼanjo likubwera,+ ndipo anthu onse odzikuza ndi onse ochita zoipa adzakhala ngati mapesi. Pa tsikulo iwo adzawonongedwa moti sipadzatsala mizu kapena nthambi zawo,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.  “Koma inu amene mukulemekeza* dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakuwalirani ndipo kuwala kwake* kudzakhala ndi mphamvu yochiritsa. Mudzadumphadumpha ngati ana a ngʼombe amphongo onenepa.”  “Mudzapondaponda anthu oipa. Iwo adzakhala ngati fumbi kuphazi kwanu pa tsiku limene ndidzachitepo kanthu,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.  “Kumbukirani Chilamulo cha Mose mtumiki wanga. Kumbukirani malamulo ndi ziweruzo zomwe ndinamupatsa ku Horebe kuti Aisiraeli onse azitsatira.+  Tamverani! Tsiku la Yehova lalikulu ndi lochititsa mantha lisanafike,+ ndidzakutumizirani mneneri Eliya.+  Iye adzachititsa mitima ya abambo kubwerera kwa ana awo+ ndi mitima ya ana kubwerera kwa abambo awo.* Adzachita zimenezi kuti ine ndisabwere kudzawononga dziko lapansi.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mukuopa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmapiko mwake.”
Kapena kuti, “adzachititsa mitima ya abambo kuti ikhale ngati ya ana ndipo mitima ya ana kuti ikhale ngati ya abambo.”