Wolembedwa ndi Maliko 1:1-45

  • Yohane Mʼbatizi ankalalikira (1-8)

  • Kubatizidwa kwa Yesu (9-11)

  • Yesu anayesedwa ndi Satana (12, 13)

  • Yesu anayamba kulalikira ku Galileya (14, 15)

  • Anasankha ophunzira oyambirira (16-20)

  • Anatulutsa mzimu wonyansa (21-28)

  • Yesu anachiritsa anthu ambiri ku Kaperenao (29-34)

  • Anapemphera kumalo opanda anthu (35-39)

  • Munthu wakhate anachiritsidwa (40-45)

1  Chiyambi cha uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu:  Mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la mneneri Yesaya kuti: “(Taona! Ine ndikutumiza mthenga wanga kuti atsogole* kukakukonzera njira.)*+  Winawake akufuula mʼchipululu kuti: ‘Konzani njira ya Yehova!* Muwongole misewu yake.’”+  Yohane Mʼbatizi anali mʼchipululu ndipo ankalalikira za ubatizo monga chizindikiro cha kulapa kuti machimo akhululukidwe.+  Choncho anthu onse amene ankakhala mʼdera la Yudeya komanso onse amene ankakhala mu Yerusalemu ankapita kwa iye. Yohane ankawabatiza* mumtsinje wa Yorodano ndipo anthuwo ankaulula machimo awo poyera.+  Yohane ankavala chovala chaubweya wa ngamila ndi lamba wachikopa mʼchiuno mwake+ ndipo ankadya dzombe ndi uchi.+  Iye ankalalikira kuti: “Pambuyo pangapa pakubwera winawake wamphamvu kuposa ine amene sindili woyenera kuwerama nʼkumasula zingwe za nsapato zake.+  Ine ndakubatizani ndi madzi, koma iye adzakubatizani ndi mzimu woyera.”+  Mʼmasiku amenewo, Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu Yorodano.+ 10  Atangovuuka mʼmadzimo, iye anaona kumwamba kukutseguka ndiponso mzimu ukutsika ngati nkhunda kudzamutera.+ 11  Ndiyeno panamveka mawu ochokera kumwamba akuti: “Iwe ndi Mwana wanga wokondedwa, umandisangalatsa kwambiri.”+ 12  Nthawi yomweyo mzimuwo unamulimbikitsa kuti apite kuchipululu. 13  Choncho iye anakhala mʼchipululumo masiku 40, akuyesedwa ndi Satana.+ Mʼchipululumo munalinso nyama zakutchire ndipo angelo ankamutumikira.+ 14  Yohane atamangidwa, Yesu anapita ku Galileya+ kukalalikira uthenga wabwino wa Mulungu.+ 15  Iye ankanena kuti: “Nthawi yoikidwiratu yakwana ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira. Lapani+ ndipo mukhulupirire uthenga wabwino!” 16  Pamene ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya,* Yesu anaona Simoni ndi Andireya+ mchimwene wake wa Simoniyo, akuponya maukonde awo mʼnyanjamo+ chifukwa anali asodzi.+ 17  Choncho Yesu anawauza kuti: “Nditsatireni ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.”+ 18  Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo nʼkumutsatira.+ 19  Atapita patsogolo pangʼono, anaona Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mchimwene wake Yohane, ali mungalawa yawo ndipo ankasoka maukonde awo.+ 20  Nthawi yomweyo anawaitana. Choncho iwo anasiya bambo awo a Zebedayo mʼngalawamo limodzi ndi anthu aganyu ndipo anamutsatira. 21  Onsewo anachoka nʼkupita ku Kaperenao. Sabata litangoyamba, anakalowa musunagoge nʼkuyamba kuphunzitsa.+ 22  Mmenemo anthu anadabwa kwambiri ndi kaphunzitsidwe kake, chifukwa ankawaphunzitsa monga munthu wokhala ndi ulamuliro, osati ngati alembi.+ 23  Pa nthawiyo, mʼsunagoge mwawomo munali munthu wogwidwa ndi mzimu wonyansa, ndipo munthuyo anafuula kuti: 24  “Kodi mukufuna chiyani kwa ife, inu Yesu Mnazareti?+ Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani bwino kwambiri, ndinu Woyera wa Mulungu!”+ 25  Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye!” 26  Choncho mzimu wonyansawo unamuchititsa kuti aphuphe ndipo unafuula mokweza. Kenako unatuluka mwa munthuyo. 27  Ataona zimenezi, anthu onse anadabwa kwambiri moti anayamba kukambirana kuti: “Kodi chimenechi nʼchiyani? Nʼchiphunzitso chatsopano! Ngakhale mizimu yonyansa akuilamula mwamphamvu ndipo ikumumvera.” 28  Choncho mbiri yake inawanda mofulumira kwambiri mʼchigawo chonse cha Galileya. 29  Zitatero iwo anachoka kusunagogeko nʼkupita kunyumba kwa Simoni ndi Andireya. Yakobo ndi Yohane nawonso anapita nawo.+ 30  Koma apongozi aakazi a Simoni+ anali chigonere, akudwala malungo.* Mwamsanga iwo anamuuza za mayiwo. 31  Choncho iye anapita kumene kunali mayiwo ndipo anawagwira dzanja nʼkuwadzutsa. Atatero malungowo anatheratu moti mayiwo anayamba kuwatumikira. 32  Chakumadzulo dzuwa litalowa, anthu anayamba kumubweretsera anthu onse amene ankadwala komanso ogwidwa ndi ziwanda.+ 33  Ndipo anthu onse amumzindawo anasonkhana pakhomopo. 34  Choncho Yesu anachiritsa anthu ambiri amene ankadwala matenda osiyanasiyana+ ndipo anatulutsa ziwanda zambiri. Koma sanalole kuti ziwandazo zilankhule, chifukwa zinkamudziwa kuti ndi Khristu.* 35  Mʼmawa kwambiri kudakali mdima, Yesu anadzuka nʼkutuluka panja ndipo anapita kumalo kopanda anthu. Kumeneko anayamba kupemphera.+ 36  Koma Simoni ndi ena amene anali naye anamufunafuna 37  ndipo anamupeza nʼkumuuza kuti: “Anthu onse akukufunafunani.” 38  Koma iye anawayankha kuti: “Tiyeni tipite kwina. Tipite kumidzi yapafupi kuti ndikalalikirenso kumeneko, chifukwa ndinabwera kudzachita zimenezi.”+ 39  Iye anapitadi ndipo ankalalikira mʼmasunagoge mwawo mu Galileya monse ndiponso kutulutsa ziwanda.+ 40  Kumenekonso munthu wina wakhate anafika kwa iye ndipo anagwada pansi nʼkumuchonderera kuti: “Ndikudziwa kuti ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”+ 41  Yesu atamva zimenezo, anagwidwa chifundo moti anatambasula dzanja lake nʼkumukhudza ndipo anamuuza kuti: “Inde ndikufuna. Khala woyera.”+ 42  Nthawi yomweyo khate lakelo linatha, ndipo anakhala woyera. 43  Kenako anamupatsa malangizo amphamvu ndipo nthawi yomweyo anamuuza kuti azipita. 44  Anamuuza kuti: “Samala, usauze aliyense zimenezi, koma upite ukadzionetse kwa wansembe ndipo chifukwa chakuti wayeretsedwa, ukapereke zinthu zimene Mose analamula,+ kuti ukhale umboni kwa iwo.”+ 45  Koma atachoka, munthu uja anayamba kulengeza zimenezo paliponse ndi kufalitsa nkhaniyo mʼmadera ena. Zimenezi zinachititsa kuti Yesu asathenso kulowa mumzinda uliwonse moonekera moti ankakhala kunja kopanda anthu. Koma anthu ankabwerabe kwa iye kuchokera kumbali zonse.+

Mawu a M'munsi

Maliko anatenga mawu amene ali mumkutiramawuwa pa Mki 3:1.
Mʼchilankhulo choyambirira, “pamaso pako.”
Kapena kuti, “ankawaviika; ankawamiza.”
MʼBaibulo, “nyanja ya Galileya” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Genesareti komanso nyanja ya Tiberiyo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “atatentha thupi.”
Mabaibulo ena amati, “zinkamudziwa kuti ndi ndani.”