Wolembedwa ndi Maliko 13:1-37

  • MAPETO A NTHAWI INO (1-37)

    • Nkhondo, zivomerezi, kusowa kwa chakudya (8)

    • Uthenga wabwino ukuyenera kulalikiridwa (10)

    • Chisautso chachikulu (19)

    • Kubwera kwa Mwana wa munthu (26)

    • Fanizo la mtengo wamkuyu (28-31)

    • Khalani maso (32-37)

13  Yesu akutuluka mʼkachisi, mmodzi wa ophunzira ake anamuuza kuti: “Mphunzitsi, taonani mmene miyala ndi nyumbazi zikukongolera!”+  Koma Yesu anamuuza kuti: “Kodi waziona nyumba zapamwamba zimenezi? Pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa mwala unzake umene sudzagwetsedwa.”+  Atakhala pansi mʼphiri la Maolivi, kachisi akuonekera bwino, Petulo, Yakobo, Yohane ndi Andireya anamufunsa ali paokha kuti:  “Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti ndipo chizindikiro chosonyeza kuti zinthu zonsezi zikufika kumapeto nʼchiyani?”+  Choncho Yesu anayamba kuwauza kuti: “Samalani kuti munthu asakusocheretseni.+  Ambiri adzabwera mʼdzina langa nʼkunena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasocheretsa anthu ambiri.  Komanso mukadzamva phokoso la nkhondo ndi malipoti a nkhondo, musadzachite mantha. Zimenezi zikuyenera kuchitika ndithu, koma mapeto adzakhala asanafikebe.+  Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.+ Kudzakhala zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana ndiponso kudzakhala njala.+ Zimenezi ndi chiyambi cha mavuto aakulu.*+  Koma inu khalani ochenjera. Anthu adzakutengerani kumakhoti aangʼono+ ndipo adzakukwapulani mumasunagoge+ nʼkukuimikani pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa ndinu otsatira anga, kuti iwowo aphunzire za ine.+ 10  Komanso choyamba uthenga wabwino ukuyenera kulalikidwa kwa anthu amitundu yonse.+ 11  Koma pamene akupita nanu kukakuperekani, musafulumire kuda nkhawa kuti mukanena chiyani. Zimene mukapatsidwe mu ola lomwelo, mukanene zomwezo chifukwa wolankhula si inu, koma mzimu woyera.+ 12  Komanso munthu adzapereka mʼbale wake kuti aphedwe ndipo bambo adzapereka mwana wake. Ana adzaukira makolo awo ndipo adzachititsa kuti aphedwe.+ 13  Ndipo anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.+ Koma amene adzapirire* mpaka mapeto+ ndi amene adzapulumuke.+ 14  Koma mukadzaona chinthu chonyansa chobweretsa chiwonongeko+ chitaima pamalo amene sichikuyenera kuima (wowerenga adzazindikire), pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri.+ 15  Munthu amene ali padenga la nyumba asadzatsike kapena kulowa mkati kukatenga chilichonse mʼnyumba mwakemo. 16  Ndipo munthu amene ali mʼmunda asadzabwerere ku zinthu zimene wazisiya mʼmbuyo kukatenga malaya ake akunja. 17  Tsoka kwa akazi oyembekezera komanso oyamwitsa ana mʼmasiku amenewo!+ 18  Pitirizani kupemphera kuti zisadzachitike mu nyengo yachisanu. 19  Chifukwa masiku amenewo adzakhala masiku a chisautso+ chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu analenga kudzafika nthawi imeneyo ndipo sichidzachitikanso.+ 20  Kunena zoona, Yehova* akanapanda kufupikitsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwa amene iye anawasankha, wafupikitsa masikuwo.+ 21  Komanso pa nthawiyo, munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’ kapena, ‘Onani! Ali uko,’ musadzakhulupirire zimenezo.+ 22  Chifukwa kudzabwera anthu onamizira kuti ndi Khristu ndiponso aneneri abodza+ ndipo adzachita zizindikiro komanso zodabwitsa kuti ngati nʼkotheka, adzasocheretse osankhidwawo. 23  Choncho inuyo musamale.+ Ine ndakuuziranitu zinthu zonse. 24  Koma mʼmasiku amenewo, chisautso chimenecho chikadzangotha, dzuwa lidzachita mdima ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake.+ 25  Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba ndipo mphamvu zimene zili kumwamba zidzagwedezeka. 26  Kenako anthu adzaona Mwana wa munthu+ akubwera mʼmitambo ndi mphamvu yaikulu ndiponso ulemerero.+ 27  Ndiyeno iye adzatumiza angelo ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera kumphepo 4, kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kukafika kumalekezero amumlengalenga.+ 28  Tsopano phunzirani zokhudza mtengo wa mkuyu kuchokera pa fanizo ili: Nthambi yake yanthete ikaphuka nʼkuchita masamba, mumadziwa kuti chilimwe chili pafupi.+ 29  Chimodzimodzi inunso, mukadzaona zinthu zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti iye ali pafupi, ali pakhomo penipeni.+ 30  Ndithu ndikukuuzani kuti mʼbadwo uwu sudzatha wonse kufa, mpaka zinthu zonsezi zitachitika.+ 31  Kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka,+ koma mawu anga adzakhalapo mpaka kalekale.+ 32  Kunena za tsiku limenelo kapena ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo kumwamba kapenanso Mwana, kupatulapo Atate wokha.+ 33  Khalani maso, khalani tcheru,+ chifukwa simukudziwa kuti nthawi yoikidwiratu idzafika liti.+ 34  Ndi zofanana ndi munthu amene akupita kudziko lina, amene wasiya nyumba mʼmanja mwa akapolo ake,+ aliyense pantchito yake, nʼkulamula mlonda wapageti kuti azikhala tcheru.+ 35  Choncho khalanibe maso chifukwa simukudziwa nthawi imene mwininyumba adzabwere.+ Simukudziwa ngati adzabwere madzulo, pakati pa usiku, mʼmbandakucha* kapena mʼmamawa,+ 36  kuti akadzafika mwadzidzidzi, asadzakupezeni mukugona.+ 37  Koma zimene ndikuuza inuzi ndikuuza onse: Khalani maso.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “chiyambi cha mavuto aakulu ngati ululu umene mzimayi amamva akatsala pangʼono kubereka.”
Kapena kuti, “amene wapirira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “atambala akulira.”