Wolembedwa ndi Maliko 16:1-8

  • Yesu anaukitsidwa (1-8)

16  Tsiku la Sabata+ litatha, Mariya wa ku Magadala, Mariya+ mayi wa Yakobo ndi Salome anagula zonunkhiritsa kuti akapake thupi la Yesu.+  Mʼmawa kwambiri tsiku loyamba la mlunguwo, iwo anafika kumandawo* dzuwa litatuluka.+  Iwo ankafunsana kuti: “Ndi ndani amene akatigubuduzire chimwala chija pakhomo la mandawo?”  Koma atayangʼanitsitsa, anaona kuti mwalawo wagubuduzidwa kale ngakhale kuti unali waukulu kwambiri.+  Atalowa mʼmandamo, anaona mnyamata atakhala pansi mbali yakumanja, atavala mkanjo woyera ndipo iwo anadabwa kwambiri.  Iye anawauza kuti: “Musadabwe choncho.+ Ndikudziwa kuti mukufuna Yesu Mnazareti, amene anaphedwa popachikidwa pamtengo. Iyetu waukitsidwa kwa akufa,+ muno mulibe. Taonani, pamene anamugoneka paja si apa!+  Inuyo pitani mukauze ophunzira ake komanso Petulo kuti, ‘Watsogola kupita ku Galileya.+ Kumeneko mukamuona, mogwirizana ndi zimene anakuuzani.’”+  Iwo atatuluka mʼmandawo anayamba kuthawa akunjenjemera komanso kunthunthumira kwambiri. Ndipo sanauze munthu aliyense zimene zinachitikazo chifukwa anali ndi mantha.*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kumanda achikumbutsowo.”
Mogwirizana ndi mipukutu yodalirika yakale, Uthenga Wabwino wa Maliko ukuthera muvesi 8. Onani Zakumapeto A3.