Wolembedwa ndi Maliko 2:1-28

  • Yesu anachiritsa munthu wakufa ziwalo (1-12)

  • Yesu anaitana Levi (13-17)

  • Funso lokhudza kusala kudya (18-22)

  • Yesu ndi ‘Mbuye wa Sabata’ (23-28)

2  Koma patapita masiku angapo, Yesu analowanso mu Kaperenao ndipo anthu anamva kuti ali panyumba.+  Choncho anthu ambiri anasonkhana kumeneko moti panalibenso malo okhala, chifukwa anthu anadzaza mpaka pakhomo ndipo anayamba kuwauza uthenga wabwino.+  Ndiyeno kunafika anthu amene anamubweretsera munthu wakufa ziwalo ndipo ananyamulidwa ndi anthu 4.+  Koma sakanatha kumufikitsa kwa Yesu chifukwa cha kuchuluka kwa anthu. Choncho anasasula denga pamene Yesu anali, ndipo ataboola padengapo, anatsitsirapo machira a munthu wakufa ziwalo uja.  Yesu ataona chikhulupiriro chawo,+ anauza wakufa ziwaloyo kuti: “Mwanawe, machimo ako akhululukidwa.”+  Tsopano alembi ena anali pomwepo ndipo anayamba kuganiza mʼmitima mwawo+ kuti:  “Nʼchifukwa chiyani munthu ameneyu akulankhula chonchi? Akunyozatu Mulungu ameneyu. Ndi ndaninso wina amene angakhululukire machimo, si Mulungu yekha basi?”+  Koma nthawi yomweyo Yesu anazindikira mumtima mwake kuti iwo ankaganiza zimenezo, ndipo anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuganiza zinthu zimenezi mʼmitima mwanu?+  Chosavuta nʼchiti, kuuza wakufa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka ndipo nyamula machira ako uyendeʼ? 10  Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu+ ali ndi mphamvu padziko lapansi zokhululukira machimo—”+ kenako anauza wakufa ziwalo uja kuti: 11  “Ndikunena ndi iwe, Nyamuka, tenga machira akowa ndipo uzipita kwanu.” 12  Zitatero munthuyo ananyamuka ndipo nthawi yomweyo ananyamula machira akewo nʼkuyenda yekha pamaso pa anthu onse. Choncho onsewo anadabwa kwambiri ndipo anatamanda Mulungu kuti: “Zoterezi sitinazionepo.”+ 13  Kenako iye anapitanso mʼmbali mwa nyanja. Gulu lonse la anthu linapitiriza kupita kwa iye ndipo anayamba kuwaphunzitsa. 14  Akudutsa anaona Levi mwana wa Alifeyo atakhala mu ofesi yokhomeramo msonkho ndipo anamuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” Nthawi yomweyo ananyamuka nʼkumutsatira.+ 15  Nthawi inayake, ankadya chakudya* mʼnyumba mwa Levi ndipo anthu ambiri okhometsa msonkho komanso ochimwa ankadya limodzi ndi Yesu ndiponso ophunzira ake. Kumeneko kunali anthu ambiri amene ankamutsatira.+ 16  Koma alembi a Afarisi, ataona kuti Yesu akudya limodzi ndi anthu ochimwa ndi okhometsa msonkho, anayamba kufunsa ophunzira ake kuti: “Bwanji akudya limodzi ndi okhometsa msonkho komanso anthu ochimwa?” 17  Yesu atamva zimenezi anawayankha kuti: “Anthu amphamvu safunikira dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna. Sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.”+ 18  Ophunzira a Yohane ndi Afarisi ankasala kudya. Choncho iwo anabwera kwa iye nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma ophunzira anu sasala kudya?”+ 19  Yesu anawayankha kuti: “Anzake a mkwati+ safunika kusala kudya ngati mkwatiyo ali nawo limodzi, si choncho kodi? Ngati mkwatiyo ali nawo limodzi sangasale kudya. 20  Koma masiku akubwera pamene mkwatiyo adzachotsedwa pakati pawo+ ndipo pa tsiku limenelo adzasala kudya. 21  Palibe amene amasokerera chigamba cha nsalu yatsopano pamalaya akunja akale. Akachita zimenezo, chigamba chatsopanocho chimakoka nʼkungʼamba malaya akalewo ndipo kungʼambikako kumawonjezereka kwambiri.+ 22  Ndiponso, palibe munthu amene amathira vinyo watsopano mʼmatumba achikopa akale. Akachita zimenezo, vinyoyo amaphulitsa matumbawo. Kenako vinyoyo amatayika ndipo matumbawo amawonongeka. Koma anthu amathira vinyo watsopano mʼmatumba achikopa atsopano.” 23  Yesu akudutsa mʼminda ya tirigu pa tsiku la Sabata, ophunzira ake anayamba kubudula ngala za tirigu nʼkumadya.+ 24  Choncho Afarisi anamuuza kuti: “Taona! Nʼchifukwa chiyani akuchita zinthu zimene ndi zosayenera kuchita pa Sabata?” 25  Koma iye anawayankha kuti: “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita, iyeyo ndi amuna omwe anali naye atamva njala ndipo analibiretu chilichonse?+ 26  Nkhani yonena za Abiyatara+ wansembe wamkulu imanena kuti, Davide analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo anadya mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu,* umene aliyense sankayenera kudya malinga ndi malamulo koma ansembe okha.+ Iye anatenga mitanda ina ya mkatewo nʼkupatsa amuna amene anali naye limodzi. Kodi inu simunawerenge nkhani imeneyi?” 27  Kenako anawauza kuti: “Sabata linakhalako chifukwa cha munthu,+ osati munthu chifukwa cha Sabata. 28  Choncho Mwana wa munthu ndi Mbuye wa Sabata.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “atakhala patebulo.”
Kapena kuti, “mkate wachionetsero.”