Wolembedwa ndi Maliko 3:1-35

  • Munthu wolumala dzanja anachiritsidwa (1-6)

  • Chigulu cha anthu chinali mʼmbali mwa nyanja (7-12)

  • Atumwi 12 (13-19)

  • Kunyoza mzimu woyera (20-30)

  • Mayi komanso azichimwene ake a Yesu (31-35)

3  Kachiwirinso Yesu analowa musunagoge. Mmenemo munali munthu wolumala dzanja.+  Ndiyeno Afarisi ankamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angachiritse munthuyo pa Sabata nʼcholinga choti amuimbe mlandu.  Ndipo iye anauza munthu wolumala dzanjayo kuti: “Nyamuka, bwera pakatipa.”  Kenako anawafunsa kuti: “Kodi malamulo amalola kuchita chiyani pa Sabata, chabwino kapena choipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha?”+ Koma iwo anangokhala chete.  Yesu anawayangʼana mokwiya ndipo anamva chisoni kwambiri chifukwa cha kuuma mtima kwawo.+ Kenako anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi ndipo linakhala labwinobwino.  Ataona zimenezi Afarisiwo anatuluka ndipo nthawi yomweyo anapita kukakonza chiwembu limodzi ndi anthu amene ankatsatira Herode+ kuti amuphe.  Koma Yesu ndi ophunzira ake anachoka nʼkupita kunyanja ndipo chigulu cha anthu ochokera ku Galileya ndi ku Yudeya chinamutsatira.+  Ngakhalenso anthu ambiri ochokera ku Yerusalemu, ku Idumeya, kutsidya la Yorodano komanso ochokera mʼmadera a ku Turo ndi Sidoni, anamva zonse zimene iye ankachita ndipo anapita kwa iye.  Ndipo iye anauza ophunzira ake kuti amubweretsere ngalawa yaingʼono yoti akweremo kuti gulu la anthulo lisamupanikize. 10  Popeza anali atachiritsa anthu ambiri, onse amene anali ndi matenda aakulu anamuunjirira kuti angomukhudza.+ 11  Ngakhalenso mizimu yonyansa,+ inkati ikamuona, inkadzigwetsa pansi pamaso pake nʼkufuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”+ 12  Koma mobwerezabwereza iye anailamula mwamphamvu kuti isamuulule.+ 13  Kenako anakwera phiri nʼkuitana anthu amene ankawafuna+ ndipo iwo anapita kwa iye.+ 14  Ndiyeno anasankha gulu la anthu 12, amenenso anawapatsa dzina lakuti atumwi, kuti aziyenda naye nthawi zonse komanso kuti aziwatuma kukalalikira 15  nʼkuwapatsa mphamvu zoti azitulutsa ziwanda.+ 16  Mʼgulu la anthu 12+ amene anasankha aja munali Simoni, amene anamupatsanso dzina lakuti Petulo,+ 17  Yakobo mwana wa Zebedayo ndi Yohane mchimwene wake wa Yakobo (awiriwa anawapatsanso dzina lakuti Boanege, limene limatanthauza “Ana a Bingu”),+ 18  Andireya, Filipo, Batolomeyo, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alifeyo, Tadeyo, Simoni Kananiya,* 19  ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anadzamʼpereka. Kenako Yesu analowa mʼnyumba. 20  Kumeneko gulu la anthu linasonkhananso, moti sanathe nʼkomwe kudya chakudya. 21  Koma achibale ake atamva zimenezo, anapita kukamugwira chifukwa iwo ankanena kuti: “Wachita misala.”+ 22  Komanso alembi amene anachokera ku Yerusalemu ankanena kuti: “Ali ndi Belezebule,* ndipo amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya wolamulira ziwanda.”+ 23  Choncho atawaitana, anayankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo kuti: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? 24  Ngati ufumu wagawanika, ufumu umenewo sungakhalitse.+ 25  Ndiponso ngati nyumba yagawanika, nyumba yoteroyo singakhalitse. 26  Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana wadziukira yekha ndipo wagawanika, sangakhalitse koma akupita kokatha. 27  Kunena zoona, palibe amene angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu nʼkuba katundu wake ngati choyamba atapanda kumanga munthu wamphamvuyo. Akatero mʼpamene angathe kutenga katundu mʼnyumbamo. 28  Ndithu ndikukuuzani, ana a anthu adzakhululukidwa zinthu zonse, kaya anachita machimo otani kapena analankhula mawu onyoza bwanji. 29  Koma aliyense amene wanyoza mzimu woyera sadzakhululukidwa kwamuyaya,+ koma adzakhala ndi mlandu wa tchimo losatha.”+ 30  Ananena zimenezi chifukwa iwo ankamunena kuti: “Ali ndi mzimu wonyansa.”+ 31  Tsopano panafika mayi ake ndi azichimwene ake+ ndipo anaima panja nʼkutuma munthu kuti akamuitane.+ 32  Gulu la anthu linakhala momuzungulira ndipo anthuwo anamuuza kuti: “Mayi anu ndi azichimwene anu ali panjapa akukufunani.”+ 33  Koma iye anawayankha kuti: “Kodi mayi anga ndi azichimwene anga ndi ndani?” 34  Kenako anayangʼana onse amene anakhala pansi momuzungulira aja nʼkunena kuti: “Onani! Mayi anga ndi azichimwene anga ndi awa.+ 35  Aliyense amene amachita zimene Mulungu amafuna, ameneyo ndi mchimwene wanga, mchemwali wanga ndi mayi anga.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “wakhama.”
Dzina limene Satana, yemwe ndi kalonga kapena kuti wolamulira ziwanda amadziwika nalo.