Maliro 2:1-22

  • Yehova anakwiyira Yerusalemu

    • Sanamve chisoni (2)

    • Yehova anakhala ngati mdani wake (5)

    • Kulirira Ziyoni (11-13)

    • Anthu odutsa mumsewu ananyoza mzinda umene poyamba unali wokongola (15)

    • Adani anasangalala chifukwa cha kuwonongedwa kwa Ziyonil (17)

א [Aleph] 2  Yehova waphimba mwana wamkazi wa Ziyoni* mumtambo wa mkwiyo wake. Iye waponya pansi kukongola kwa Isiraeli kuchokera kumwamba kupita padziko lapansi.+ Sanakumbukire chopondapo mapazi ake+ pa tsiku la mkwiyo wake. ב [Beth]   Yehova wameza mopanda chifundo malo onse amene Yakobo ankakhala. Mokwiya kwambiri, iye wagwetsa mipanda yolimba kwambiri ya mwana wamkazi wa Yuda.+ Iye wagwetsera pansi komanso kuipitsa ufumu+ ndi akalonga ake.+ ג [Gimel]   Iye wathetsa mphamvu zonse za* Isiraeli atakwiya kwambiri. Adani athu atatiukira, iye sanatithandize,+Ndipo mkwiyo wakewo unapitiriza kuyakira Yakobo ngati moto umene wawononga chilichonse chimene chili pafupi.+ ד [Daleth]   Wakunga* uta wake ngati mdani. Wakweza dzanja lake lamanja kuti atiukire ngati ndife adani ake.+Iye anapitiriza kupha anthu onse ofunika kwambiri.+ Anakhuthulira ukali wake ngati moto+ mutenti ya mwana wamkazi wa Ziyoni.+ ה [He]   Yehova wakhala ngati mdani.+Wameza Isiraeli. Iye wameza nsanja zonse za Isiraeli.Wawononga malo ake onse okhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Ndipo wachititsa kuti paliponse pakhale maliro komanso kulira mumzinda wa mwana wamkazi wa Yuda. ו [Waw]   Iye wapasula msasa wake+ ngati chisimba chamʼmunda. Iye wathetsa zikondwerero zake.+ Yehova wachititsa kuti zikondwerero ndi sabata ziiwalike mu Ziyoni,Ndipo chifukwa cha mkwiyo wake waukulu sakuganiziranso za mfumu ndi wansembe.+ ז [Zayin]   Yehova wakana guwa lake lansembe.Iye wasiya malo ake opatulika.+ Wapereka mʼmanja mwa adani makoma a nsanja zake zotetezeka.+ Adaniwo afuula mʼnyumba ya Yehova+ ngati pa tsiku lachikondwerero. ח [Heth]   Yehova watsimikiza kuti awononge mpanda wa mwana wamkazi wa Ziyoni.+ Watambasula chingwe choyezera.+ Sanabweze dzanja lake kuti lisabweretse chiwonongeko. Wachititsa kuti malo okwera omenyerapo nkhondo ndi mpanda zilire. Zonse pamodzi zachititsidwa kuti zisakhalenso ndi mphamvu. ט [Teth]   Mageti ake amira munthaka.+ Wawononga ndi kuthyolathyola mipiringidzo yake. Mfumu yake ndi akalonga ake ali pakati pa anthu a mitundu ina.+ Anthu sakutsatira malamulo.* Ndipo ngakhale aneneri ake sakuona masomphenya ochokera kwa Yehova.+ י [Yod] 10  Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi ndipo akhala chete.+ Iwo athira fumbi pamitu yawo ndipo avala ziguduli.+ Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa mitu yawo mpaka pansi. כ [Kaph] 11  Maso anga atopa ndi kugwetsa misozi.+ Mʼmimba mwanga mukubwadamuka. Chiwindi changa chakhuthulidwa pansi chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga,+Ndiponso chifukwa chakuti ana ndi makanda akukomoka mʼmabwalo a mzinda.+ ל [Lamed] 12  Iwo ankafunsa amayi awo kuti: “Kodi chakudya ndi vinyo zili kuti?”+ Pamene ankakomoka mʼmabwalo a mzinda ngati munthu amene wavulazidwa,Ndiponso pamene moyo wawo unkachoka ali mʼmanja mwa mayi awo. מ [Mem] 13  Kodi ndikupatse umboni wotani,Kapena kodi ndingakuyerekezere ndi chiyani, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu?* Kodi ndikufananitse ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwali iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Chifukwa kuwonongeka kwako kwafalikira ngati kukula kwa nyanja.+ Ndani angakuchiritse?+ נ [Nun] 14  Masomphenya amene aneneri anu anaona ndi abodza komanso achabechabe,+Ndipo sanaulule zolakwa zanu nʼcholinga choti musatengedwe kupita ku ukapolo,+Koma ankaona masomphenya abodza komanso okusocheretsani.+ ס [Samekh] 15  Anthu onse odutsa mumsewu akakuona, akuwomba mʼmanja monyoza.+ Akuimba mluzu modabwa+ ndipo akupukusira mitu yawo mwana wamkazi wa Yerusalemu. Iwo akunena kuti: “Kodi uwu ndi mzinda umene ankaunena kuti, ‘Ndi wokongola kwambiri ndipo anthu padziko lonse lapansi amasangalala nawoʼ?”+ פ [Pe] 16  Adani ako onse atsegula pakamwa pawo. Akuimba mluzu ndi kukukuta mano nʼkumanena kuti: “Ameneyu tamumeza.+ Lero ndi tsiku limene takhala tikuliyembekezera.+ Lafika ndipo taliona!”+ ע [Ayin] 17  Yehova wachita zimene ankafuna.+ Wakwaniritsa zimene ananena,+Zimene analamula kalekale.+ Wakuwononga mopanda chisoni.+ Wachititsa kuti adani ako asangalale chifukwa cha zimene zakuchitikira. Wawonjezera mphamvu* za adani ako. צ [Tsade] 18  Anthu akulirira Yehova ndi mtima wawo wonse, iwe mpanda wa mwana wamkazi wa Ziyoni. Misozi iyende ngati mtsinje masana ndi usiku. Usapume ndipo diso* lako lisasiye kulira. ק [Qoph] 19  Nyamuka! Lira mofuula usiku, pa nthawi yoyamba ulonda. Khuthula mtima wako pamaso pa Yehova ngati madzi. Pemphera utakweza manja ako kwa iye chifukwa cha ana ako,Amene akukomoka ndi njala pamphambano za misewu yonse.+ ר [Resh] 20  Inu Yehova, yangʼanani kuti muone amene mwamulanga mwaukali. Kodi azimayi azidya ana awo amene* abereka, ana awo athanzi?+Kapena kodi ansembe ndi aneneri aziphedwa mʼmalo opatulika a Yehova?+ ש [Shin] 21  Anyamata ndi amuna okalamba afa ndipo mitembo yawo ili pansi mʼmisewu.+ Anamwali* anga ndi anyamata anga aphedwa ndi lupanga.+ Mwawapha pa tsiku la mkwiyo wanu. Mwawapha mopanda chisoni.+ ת [Taw] 22  Munaitana zoopsa kuchokera kumbali zonse ngati kuti mukuitana anthu pa tsiku lachikondwerero.+ Pa tsiku la mkwiyo wa Yehova panalibe aliyense amene anathawa kapena kupulumuka.+Ana onse amene ndinabereka komanso kuwalera, mdani wanga anawapha.+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga iliyonse ya.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Waponda.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Yerusalemu” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mwana wamkazi wa diso.”
Kapena kuti, “zipatso zawo zimene.”
Kapena kuti, “Atsikana.”