Maliro 3:1-66
-
Yeremiya anasonyeza mmene akumvera komanso zimene ankayembekezera
א [Aleph]
3 Ine ndine munthu amene ndakumana ndi mavuto chifukwa Mulungu anatikwiyira kwambiri ndipo anatilanga.
2 Iye wandithamangitsa ndipo wachititsa kuti ndiyende mumdima, osati mʼmalo owala.+
3 Ndithudi, iye amandimenya ndi dzanja lake mobwerezabwereza tsiku lonse.+
ב [Beth]
4 Wachititsa kuti mnofu ndi khungu langa ziwonongeke.Iye waphwanya mafupa anga.
5 Wandizungulira kumbali zonse. Wachititsa kuti poizoni wowawa+ komanso mavuto zindizungulire.
6 Wandikakamiza kuti ndikhale mʼmalo amdima, ngati anthu oti anafa kalekale.
ג [Gimel]
7 Wandimangira mpanda kuti ndisathawe,Wandimanga ndi maunyolo olemera akopa.*+
8 Komanso ndikalira modandaula kuti andithandize, iye amakana* pemphero langa.+
9 Watseka njira zanga ndi miyala yosema.Wachititsa njira zanga kuti zikhale zovuta kuyendamo.+
ד [Daleth]
10 Iye wandibisalira ngati chimbalangondo kuti andigwire, wandibisalira ngati mkango.+
11 Wandichotsa panjira zanga ndipo wandikhadzulakhadzula.*Wandichititsa kuti ndikhale wopanda kanthu.+
12 Wakunga* uta wake ndipo wandisandutsa chinthu choti azilasapo mivi yake.
ה [He]
13 Walasa impso zanga ndi mivi* yotuluka mʼkachikwama kake.
14 Ndakhala chinthu choseketsa kwa anthu onse ndipo amandiimba mʼnyimbo yawo nʼkumandinyoza tsiku lonse.
15 Wandikhutitsa zinthu zowawa ndipo wandichititsa kuti ndidye chitsamba chowawa.+
ו [Waw]
16 Wagulula mano anga ndi miyala.Wandiviviniza mʼphulusa.+
17 Inu mwachititsa kuti ndisakhale pamtendere, moti ndaiwala kuti zinthu zabwino zimakhala bwanji.
18 Choncho ndikunena kuti: “Ulemerero wanga ndi chiyembekezo changa mwa Yehova zatha.”
ז [Zayin]
19 Kumbukirani kuti ndikuvutika ndipo ndilibe pokhala.+ Kumbukiraninso kuti ndimadya chitsamba chowawa ndi poizoni wowawa.+
20 Ndithu mudzandikumbukira ndi kundiweramira kuti mundithandize.+
21 Ndikukumbukira zimenezi mumtima mwanga. Pa chifukwa chimenechi, ndidzakhala ndi mtima wodikira.+
ח [Heth]
22 Chifukwa cha chikondi chokhulupirika cha Yehova, ife sitinatheretu,+Ndipo chifundo chake sichitha.+
23 Chifundocho chimakhala chatsopano mʼmawa uliwonse+ ndipo ndinu wokhulupirika kwambiri.+
24 Ine ndanena kuti: “Yehova ndi cholowa changa.+ Pa chifukwa chimenechi, ndidzakhala ndi mtima womudikira.”+
ט [Teth]
25 Yehova ndi wabwino kwa munthu amene akumuyembekezera,+ kwa munthu amene akupitiriza kumufunafuna.+
26 Ndi bwino kuti munthu akhale chete*+ nʼkumayembekezera chipulumutso cha Yehova.+
27 Ndi bwino kuti munthu akumane ndi mavuto ali wamngʼono.+
י [Yod]
28 Mulungu akalola kuti zimenezi zimuchitikire, muloleni akhale payekha ndipo akhale chete.+
29 Iye agonjere ndipo aike nkhope yake mufumbi.+ Mwina pangakhale chiyembekezo choti apulumutsidwa.+
30 Aperekere tsaya lake kwa munthu amene akumumenya. Anyozedwe mokwanira.
כ [Kaph]
31 Chifukwa Yehova sadzatitaya mpaka kalekale.+
32 Ngakhale kuti wachititsa kuti timve chisoni, adzatichitiranso chifundo mogwirizana ndi chikondi chake chokhulupirika chomwe ndi chochuluka.+
33 Chifukwa iye sasangalala ndi kuzunza anthu kapena kuwachititsa kuti amve chisoni.+
ל [Lamed]
34 Mulungu savomereza kuti anthu azipondereza akaidi onse padziko lapansi,+
35 Savomereza kuti munthu alephere kuchitira mnzake chilungamo pamaso pa Wamʼmwambamwamba,+
36 Kapena kuchitira munthu zachinyengo pa mlandu wakeYehova savomereza zimenezi.
מ [Mem]
37 Ndiye ndi ndani amene anganene kuti chinthu chichitike, chinthucho nʼkuchitikadi Yehova asanalamule?
38 Zinthu zoipa komanso zinthu zabwino,Sizitulukira limodzi pakamwa pa Wamʼmwambamwamba.
39 Kodi pali chifukwa chilichonse choti munthu adandaulire ndi zotsatira za tchimo lake?+
נ [Nun]
40 Tiyeni tifufuze ndi kuganizira mozama makhalidwe athu+ ndipo tibwerere kwa Yehova.+
41 Tiyeni tichonderere Mulungu kumwamba ndi mtima wonse, ndipo tikweze manja athu+ nʼkunena kuti:
42 “Ife tachimwa komanso tapanduka+ ndipo inu simunatikhululukire.+
ס [Samekh]
43 Mwadzitchinga ndi mkwiyo wanu kuti tisakufikireni.+Mwatithamangitsa ndipo mwatipha mopanda chifundo.+
44 Mwadzitchinga ndi mtambo kuti pemphero lathu lisafike kwa inu.+
45 Mwatisandutsa nyansi ndi zinyalala pakati pa anthu a mitundu ina.”
פ [Pe]
46 Adani athu onse akutsegula pakamwa pawo nʼkumatinenera zoipa.+
47 Tikungokhala ndi mantha nthawi zonse ndipo tsoka latigwera.+ Tawonongedwa ndipo tatsala mabwinja okhaokha.+
48 Maso anga akungotuluka misozi ngati mitsinje chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.+
ע [Ayin]
49 Maso anga akungotuluka misozi ndipo sikusiya,+
50 Mpaka Yehova atayangʼana pansi nʼkutiona ali kumwamba.+
51 Zimene maso anga aona zachititsa kuti ndikhale wachisoni chifukwa cha zimene zachitikira ana onse aakazi amumzinda wanga.+
צ [Tsade]
52 Adani anga akundisaka ngati mbalame popanda chifukwa.
53 Anandiponya mʼdzenje kuti andiphe ndipo ankandigenda ndi miyala.
54 Ndinamira mʼmadzi moti ndinanena kuti: “Ndifa basi!”
ק [Qoph]
55 Inu Yehova, ndinaitana dzina lanu mofuula ndili mʼdzenje lakuya kwambiri.+
56 Imvani mawu anga. Musatseke khutu lanu pamene ndikulira kupempha kuti mundithandize komanso kuti mundipatse mpumulo.
57 Pa tsiku limene ndinakuitanani, munandiyandikira nʼkundiuza kuti: “Usaope.”
ר [Resh]
58 Inu Yehova, mwandiweruzira milandu yanga. Mwawombola moyo wanga.+
59 Inu Yehova, mwaona zoipa zimene andichitira. Chonde, ndiweruzeni mwachilungamo.+
60 Mwaona zonse zimene achita pondibwezera ndiponso ziwembu zawo zonse zimene andikonzera.
ש [Sin] kapena [Shin]
61 Inu Yehova, mwamva mawu awo onyoza ndipo mwaona ziwembu zawo zonse zimene andikonzera.+
62 Mwamva mawu ochokera pakamwa pa anthu amene akundipondereza. Mwamvanso ziwembu zimene akunongʼonezana tsiku lonse kuti andichitire.
63 Tawaonani, akakhala pansi kapena kuimirira akumandinyoza mʼnyimbo zawo.
ת [Taw]
64 Inu Yehova, mudzawabwezera mogwirizana ndi zochita zawo.
65 Mudzaumitsa mtima wawo, ndipo zimenezi zidzakhala temberero lawo.
66 Inu Yehova, mudzawathamangitsa mutakwiya ndipo mudzawawononga kuti asapezekenso padziko lapansi.