Maliro 4:1-22
א [Aleph]
4 Golide amene anali wowala komanso woyengedwa bwino,+ sakuwalanso.
Miyala yopatulika+ yamwazika pamphambano zonse za misewu.+
ב [Beth]
2 Ana okondedwa a Ziyoni amene anali amtengo wapatali ngati golide woyengedwa bwino,Tsopano akuonedwa ngati mitsuko ikuluikulu yadothi,Ntchito ya manja a munthu woumba mbiya.
ג [Gimel]
3 Ngakhale mimbulu imapereka bere kwa ana ake kuti ayamwe,Koma mwana wamkazi wa anthu anga wakhala wankhanza+ ngati nthiwatiwa zamʼchipululu.+
ד [Daleth]
4 Lilime la mwana woyamwa lamamatira kummero chifukwa cha ludzu.
Ana akupempha chakudya+ koma palibe amene akuwapatsa.+
ה [He]
5 Anthu amene ankadya chakudya chabwino agona mʼmisewu chifukwa cha njala.+
Anthu amene ankavala zovala zamtengo wapatali+ kuyambira ali ana, agona pamilu yaphulusa.
ו [Waw]
6 Chilango chimene mwana wamkazi wa anthu anga walandira nʼchachikulu kuposa chimene mzinda wa Sodomu unalandira chifukwa cha machimo ake.+Mzinda umenewu unawonongedwa mʼkanthawi kochepa, ndipo panalibe dzanja limene linauthandiza.+
ז [Zayin]
7 Anaziri ake+ anali oyera kwambiri, anali oyera kuposa mkaka.
Anali ofiira kuposa miyala yamtengo wapatali ya korali. Anali onyezimira ngati miyala ya safiro.
ח [Heth]
8 Tsopano ayamba kuoneka akuda kuposa makala.Anthu sakuthanso kuwazindikira mʼmisewu.
Khungu lawo lafota moti lamamatira kumafupa awo.+ Langoti gwaa ngati mtengo wouma.
ט [Teth]
9 Amene anaphedwa ndi lupanga aliko bwino kusiyana ndi amene anafa ndi njala.+Amenewa anafooka nʼkufa chifukwa chosowa chakudya ndipo anafa ngati abayidwa ndi lupanga.
י [Yod]
10 Azimayi amene amakhala achifundo, aphika ana awo ndi manja awo.+
Anawo akhala chakudya chawo pa nthawi yachisoni pamene mwana wamkazi wa anthu anga wawonongedwa.+
כ [Kaph]
11 Yehova wasonyeza ukali wake.Wakhuthula mkwiyo wake woyaka moto.+
Ndipo iye wayatsa moto mʼZiyoni, umene wawotcha maziko ake.+
ל [Lamed]
12 Mafumu apadziko lapansi ndiponso anthu onse okhala panthaka ya dziko lapansi,Sanayembekezere kuti mdani angadzalowe pamageti a Yerusalemu.+
מ [Mem]
13 Zimenezi zinachitika chifukwa cha machimo a aneneri ake ndi zolakwa za ansembe ake,+Amene anakhetsa magazi a anthu olungama mumzindawo.+
נ [Nun]
14 Ansembe ndi aneneriwo akungoyendayenda mʼmisewu ngati anthu akhungu.+
Aipitsidwa ndi magazi,+Moti palibe amene angathe kukhudza zovala zawo.
ס [Samekh]
15 Anthu akuwafuulira kuti: “Chokani! Anthu odetsedwa inu! Chokani! Chokani! Musatikhudze!”
Iwo alibe pokhala ndipo akungoyendayenda.
Anthu a mitundu ina akunena kuti: “Sitilola kuti amenewa azikhala ndi ife kuno.*+
פ [Pe]
16 Yehova wawabalalitsa+Ndipo sadzawakomeranso mtima.
Anthu sadzalemekezanso ansembe+ kapena kuchitira chifundo amuna achikulire.”+
ע [Ayin]
17 Ngakhale panopa maso athu afooka chifukwa choyembekezera thandizo lomwe silikubwera.+
Tinafufuza thandizo ku mtundu wa anthu umene sukanatha kutipulumutsa.+
צ [Tsade]
18 Akutisakasaka kulikonse kumene tikupita,+ moti sitingathenso kuyenda mʼmabwalo a mizinda yathu.
Mapeto a moyo wathu ayandikira. Masiku athu atha chifukwa mapeto a moyo wathu afika.
ק [Qoph]
19 Anthu amene ankatithamangitsa anali aliwiro kuposa ziwombankhanga zouluka mʼmwamba.+
Iwo anatithamangitsa mʼmapiri. Anatibisalira mʼchipululu.
ר [Resh]
20 Wodzozedwa wa Yehova,+ amene ndi mpweya wotuluka mumphuno mwathu, wagwidwa mʼdzenje lawo lalikulu.+Ponena za ameneyu, ife tinkanena kuti: “Tidzakhala mumthunzi wake pakati pa mitundu ya anthu.”
ש [Sin]
21 Kondwa ndipo usangalale, iwe mwana wamkazi wa Edomu,+ amene ukukhala mʼdziko la Uzi.
Koma iwenso kapu ya tsoka idzakupeza.+ Udzaledzera ndipo udzavula nʼkukhala maliseche.+
ת [Taw]
22 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,* chilango chimene anakupatsa chifukwa cha zolakwa zako chatha.
Sadzakutenganso kupita nawe ku ukapolo.+
Koma Mulungu adzatembenukira kwa iwe, mwana wamkazi wa Edomu, kuti aone zolakwa zako.
Machimo ako adzawaika poyera.+