Maliro 5:1-22
5 Inu Yehova, kumbukirani zimene zatichitikira.
Tiyangʼaneni kuti muone mmene tikuchitira manyazi.+
2 Cholowa chathu chaperekedwa kwa anthu achilendo. Nyumba zathu zaperekedwa kwa anthu ochokera kudziko lina.+
3 Takhala ana amasiye opanda bambo. Amayi athu akhala ngati akazi amasiye.+
4 Madzi akumwa ndi nkhuni, tikuchita kugula.+
5 Anthu amene akutithamangitsa atsala pangʼono kutigwira.Tatopa koma tilibe mwayi woti tipume.+
6 Kuti tipeze chakudya chokwanira, tikudalira Iguputo+ ndi Asuri.+
7 Makolo athu amene anachimwa anafa, koma ifeyo ndi amene tikuvutika ndi zolakwa zawo.
8 Antchito ndi amene akutilamulira. Palibe amene akutilanditsa mʼmanja mwawo.
9 Kuti tipeze chakudya, timaika moyo wathu pachiswe+ chifukwa cha anthu amene ali ndi malupanga mʼchipululu.
10 Khungu lathu latentha kwambiri ngati ngʼanjo chifukwa cha njala yaikulu.+
11 Achitira zachipongwe* akazi athu amene ali mʼZiyoni ndi anamwali amene ali mʼmizinda ya Yuda.+
12 Akalonga athu anawapachika powamanga dzanja limodzi.+ Anthuwo sankalemekezanso amuna achikulire.+
13 Anyamata akunyamula mphero, ndipo tianyamata tikudzandira chifukwa cholemedwa ndi mitolo ya nkhuni.
14 Amuna achikulire sakupezekanso pageti la mzinda+ ndipo anyamata asiya kuimba nyimbo.+
15 Chisangalalo chamumtima mwathu chatha. Kuvina kwathu kwasanduka kulira maliro.+
16 Chisoti chathu chachifumu chagwa. Tsoka kwa ife chifukwa tachimwa!
17 Chifukwa cha zimenezi, mtima wathu wadwala.+Ndipo chifukwa cha zinthu zimenezi, maso athu achita mdima,+
18 Chifukwa cha Phiri la Ziyoni limene lakhala bwinja+ ndipo tsopano nkhandwe zikuyendayenda mmenemo.
19 Koma inu Yehova mudzakhala pampando wanu wachifumu mpaka kalekale.
Mpando wanu wachifumu udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+
20 Nʼchifukwa chiyani mwatiiwala kwamuyaya nʼkutisiya kwa nthawi yaitali chonchi?+
21 Inu Yehova, tibwezereni kwa inu ndipo ife tibwerera kwa inu mwamsanga.+
Bwezeretsani zinthu zonse kuti zikhale ngati mmene zinalili kale.+
22 Koma inu mwatikanitsitsa.
Mukupitiriza kutikwiyira kwambiri.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Agwiririra.”