Salimo 100:1-5

  • Kuyamikira Mlengi

    • “Tumikirani Yehova mokondwera” (2)

    • ‘Mulungu ndi amene anatipanga’ (3)

Nyimbo yoyamikira. 100  Dziko lonse lapansi lifuulire Yehova mosangalala chifukwa wapambana.+   Tumikirani Yehova mokondwera.+ Bwerani kwa iye mukufuula mosangalala.   Dziwani* kuti Yehova ndi Mulungu.+ Iye ndi amene anatipanga, ndipo ndife ake.+ Ndife anthu ake komanso nkhosa zimene akuweta.+   Lowani pamageti ake mukumuyamikira,+Lowani mʼmabwalo ake mukumutamanda.+ Muyamikeni, tamandani dzina lake.+   Chifukwa Yehova ndi wabwino.+Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale,Ndipo kukhulupirika kwake kudzakhalapo ku mibadwo yonse.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Vomerezani.”