Salimo 101:1-8

  • Wolamulira wochita zinthu mokhulupirika

    • ‘Wodzikweza sindidzamulekerera’ (5)

    • “Ndidzayangʼana anthu okhulupirika” (6)

Nyimbo ndi Salimo la Davide. 101  Ndidzaimba za chikondi chokhulupirika komanso chilungamo chanu. Inu Yehova, ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani.   Ndidzachita zinthu mwanzeru komanso mosalakwitsa kanthu.* Kodi mudzandithandiza liti? Ndidzayenda mʼnyumba yanga ndi mtima wokhulupirika.+   Sindidzayangʼana chinthu chilichonse choipa.* Ndimadana ndi zochita za anthu amene asiya kuchita zinthu zabwino.+Sindidzalola kuti zochita zawozo zindikhudze.   Aliyense wopotoka maganizo, ali kutali ndi ine.Sindidzalola* kuchita zinthu zoipa.   Aliyense wonenera mnzake miseche,+Ndidzamukhalitsa chete.* Aliyense amene ali ndi mtima wonyada komanso wodzikweza,Sindidzamulekerera.   Ndidzayangʼana anthu okhulupirika kwa inu padziko lapansi,Kuti azikhala ndi ine. Amene akuyenda mosalakwitsa kanthu* adzanditumikira.   Mʼnyumba yanga simudzakhala munthu wachinyengo,Ndipo wabodza aliyense sadzaima pamaso panga.   Mʼmawa uliwonse ndidzawononga* oipa onse apadziko lapansi,Ndidzapha onse ochita zoipa nʼkuwachotsa mumzinda wa Yehova.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “komanso mokhulupirika.”
Kapena kuti, “chopanda pake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Sindidzadziwa.”
Kapena kuti, “Ndidzathana naye.”
Kapena kuti, “akuyenda mokhulupirika.”
Kapena kuti, “ndidzathana ndi.”