Salimo 102:1-28

  • Pemphero la munthu woponderezedwa amene ali pa mavuto

    • “Ndili ngati mbalame imene ili yokhayokha” (7)

    • “Masiku a moyo wanga ali ngati chithunzithunzi chimene chimazimiririka” (11)

    • “Yehova adzamanganso Ziyoni” (16)

    • Yehova adzakhalapo kwamuyaya (26, 27)

Pemphero la munthu woponderezedwa pamene ali pamavuto* ndipo akutula nkhawa zake kwa Yehova.+ 102  Inu Yehova, imvani pemphero langa.+Imvani kufuula kwanga kopempha thandizo.+   Musandibisire nkhope yanu pamene ndili pamavuto aakulu.+ Tcherani khutu lanu kwa ine.*Ndiyankheni mofulumira pamene ndikuitana.+   Chifukwa masiku a moyo wanga akuzimiririka ngati utsi,Ndipo mafupa anga akutentha kwambiri ngati ngʼanjo.+   Mtima wanga wakhala ngati udzu umene wawauka nʼkuuma,+Chifukwa sindikulakalaka kudya chakudya.   Chifukwa chakuti ndikubuula mokweza mawu,+Ndangotsala mafupa okhaokha.+   Ndikufanana ndi mbalame yamʼchipululu yotchedwa vuwo.Ndakhala ngati nkhwezule yamʼmabwinja.   Ndikusowa tulo.Ndili ngati mbalame imene ili yokhayokha padenga.+   Tsiku lonse adani anga amandinyoza.+ Anthu amene amanditonza amagwiritsa ntchito dzina langa potemberera ena.   Ndikudya phulusa ngati chakudya,+Ndipo zakumwa zanga ndi zosakanikirana ndi misozi.+ 10  Izi zili choncho chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanu,Popeza munandikweza mʼmwamba kuti munditaye. 11  Masiku a moyo wanga ali ngati chithunzithunzi chimene chimazimiririka,+Ndipo ndafota ngati udzu.+ 12  Koma inu Yehova, mudzakhalapobe kwamuyaya,+Dzina lanu lidzakhalapobe* ku mibadwo yonse.+ 13  Ndithudi inu mudzanyamuka nʼkusonyeza Ziyoni chifundo,+Chifukwa imeneyi ndi nthawi yoti mumusonyeze kukoma mtima kwanu.+Nthawi yoikidwiratu yakwana.+ 14  Atumiki anu amasangalala ndi miyala ya mpanda wake,+Ndipo amakonda ngakhale fumbi lake.+ 15  Mitundu ya anthu idzaopa dzina lanu, inu Yehova,Ndipo mafumu onse apadziko lapansi adzaopa ulemerero wanu.+ 16  Chifukwa Yehova adzamanganso Ziyoni.+Iye adzaonekera mu ulemerero wake.+ 17  Adzamvetsera pemphero la anthu osauka.+Iye sadzapeputsa pemphero lawo.+ 18  Zimenezi zalembedwera mʼbadwo wamʼtsogolo,+Kuti anthu amene akubwera mʼtsogolo* adzatamande Ya. 19  Iye amayangʼana pansi ali pamalo ake apamwamba omwe ndi oyera,+Yehova amayangʼana dziko lapansi ali kumwamba, 20  Kuti amve kuusa moyo kwa mkaidi,+Komanso kuti amasule anthu amene aweruzidwa kuti akaphedwe.+ 21  Wachita izi kuti dzina la Yehova lilengezedwe mʼZiyoni+Komanso kuti atamandidwe mu Yerusalemu, 22  Pamene mitundu ya anthu komanso maufumuAdzasonkhana pamodzi kuti atumikire Yehova.+ 23  Anandilanda mphamvu zanga nthawi yake isanakwane.Anafupikitsa masiku a moyo wanga. 24  Ine ndinati: “Inu Mulungu wanga,Musachotse moyo wanga ndisanakalambe,Inu amene mudzakhalapo ku mibadwo yonse.+ 25  Munakhazikitsa maziko a dziko lapansi kalekale,Ndipo kumwamba ndi ntchito ya manja anu.+ 26  Zimenezi zidzatha, koma inu mudzakhalapobe.Mofanana ndi chovala, zonsezi zidzatha. Mofanana ndi zovala zimene zatha, mudzapezerapo zina ndipo nazonso zidzatha. 27  Koma inu simusintha ndipo mudzakhalapo mpaka kalekale.+ 28  Ana a atumiki anu adzakhala motetezeka,Ndipo ana awo adzakhala motetezeka pamaso panu.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “pamene wafooka.”
Kapena kuti, “Weramani ndipo mundimvetsere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Chikumbutso chanu chidzakhalapobe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu amene adzalengedwe.”