Salimo 105:1-45

  • Zimene Yehova anachitira anthu ake posonyeza kuti ndi wokhulupirika

    • Mulungu amakumbukira pangano lake (8-10)

    • “Musakhudze odzozedwa anga” (15)

    • Mulungu anagwiritsa ntchito Yosefe amene anali kapolo (17-22)

    • Zozizwitsa zimene Mulungu anachita ku Iguputo (23-36)

    • Ulendo wa Aisiraeli wochoka ku Iguputo (37-39)

    • Mulungu anakumbukira zimene analonjeza Abulahamu (42)

105  Yamikani Yehova,+ itanani pa dzina lake,Dziwitsani mitundu ya anthu ntchito zake.+   Muimbireni, muimbireni nyimbo zomutamanda,Ganizirani mozama* ntchito zake zonse zodabwitsa.+   Nyadirani dzina lake loyera.+ Mitima ya anthu ofunafuna Yehova isangalale.+   Funafunani Yehova+ ndipo muzidalira mphamvu zake. Nthawi zonse muzimupempha kuti akuthandizeni.*   Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,Kumbukirani zozizwitsa zake ndi ziweruzo zimene wapereka,+   Inu mbadwa* za Abulahamu mtumiki wake,+Inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.+   Iye ndi Yehova Mulungu wathu.+ Ziweruzo zake zili padziko lonse lapansi.+   Amakumbukira pangano lake mpaka kalekale,+Lonjezo limene anapereka* ku mibadwo 1,000.+   Wakumbukira pangano limene anapangana ndi Abulahamu,+Komanso lumbiro limene analumbira kwa Isaki,+ 10  Limene analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,Komanso monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli, 11  Pamene anati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani+Kuti likhale cholowa chako.”+ 12  Pamene ananena zimenezi, nʼkuti iwo ali ochepa.+Nʼkuti ali ochepa kwambiri komanso ali alendo mʼdzikolo.+ 13  Iwo ankayendayenda kuchokera ku mtundu wina kupita ku mtundu wina,Komanso kuchokera mu ufumu wina kupita kwa anthu a mtundu wina.+ 14  Mulungu sanalole kuti munthu aliyense awapondereze,+Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.+ 15  Iye anati: “Musakhudze odzozedwa anga,Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.”+ 16  Iye anagwetsa njala yaikulu mʼdzikomo,+Iye anachititsa kuti asathenso kupeza chakudya.* 17  Mulungu anatsogoza Yosefe,Munthu amene anagulitsidwa kuti akhale kapolo.+ 18  Kumeneko anamanga* mapazi ake mʼmatangadza,+Khosi lake analiika mʼzitsulo 19  Mpaka nthawi imene zimene Mulungu ananena zinakwaniritsidwa,+Mawu a Yehova ndi amene anamuyenga. 20  Mfumu inalamula kuti amutulutse mʼndende,+Wolamulira mitundu ya anthu anatulutsa Yosefe mʼndende. 21  Anamupatsa udindo woyangʼanira banja lakeKomanso woyangʼanira chuma chake chonse.+ 22  Anamupatsa mphamvu zolamulira* akalonga ake mmene akufuniraKomanso kuti akuluakulu aziwaphunzitsa zinthu za nzeru.+ 23  Kenako Isiraeli anapita ku Iguputo+Ndipo Yakobo anakhala monga mlendo mʼdziko la Hamu. 24  Mulungu anachititsa kuti anthu ake aberekane kwambiri,+Iye anawachititsa kuti akhale amphamvu kwambiri kuposa adani awo.+ 25  Analola adaniwo kuti asinthe mitima yawo nʼkuyamba kudana ndi anthu ake,Komanso kukonzera chiwembu atumiki akewo.+ 26  Ndiyeno anatumiza Mose mtumiki wake,+Ndi Aroni+ amene anamusankha. 27  Iwowa anachita zizindikiro za Mulungu pamaso pa Aiguputo,Anachita zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.+ 28  Mulungu anachititsa kuti mʼdziko la Iguputo mukhale mdima.+Iwo* sanapandukire mawu ake. 29  Anasandutsa madzi a Aiguputo kukhala magazi,Ndipo anapha nsomba zawo.+ 30  Mʼdziko lawo munadzaza achule,+Ngakhalenso mʼzipinda za mafumu awo. 31  Analamula kuti pagwe ntchentche zoluma,Komanso tizilombo touluka toyamwa magazi,* mʼmadera awo onse.+ 32  Anawagwetsera matalala mʼmalo mwa mvula,Anagwetsa mphezi* mʼdziko lawo.+ 33  Anawononga mitengo yawo ya mpesa ndi ya mkuyuNdipo anakhadzula mitengo mʼdziko lawo. 34  Analamula kuti pagwe dzombe,Dzombe lingʼonolingʼono losawerengeka.+ 35  Dzombelo linadya zomera zonse mʼdziko lawo,Linadyanso mbewu zonse zamʼmunda mwawo. 36  Kenako Mulungu anapha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko lawo,+Chiyambi cha mphamvu zawo zobereka. 37  Anatulutsa anthu ake atatenga siliva ndi golide.+Ndipo pakati pa mafuko ake panalibe amene anapunthwa panjira. 38  Aiguputo anasangalala Aisiraeli atatuluka mʼdzikolo,Chifukwa ankawaopa kwambiri.+ 39  Mulungu anatumiza mtambo kuti uwateteze+ Komanso moto kuti uziwaunikira usiku.+ 40  Anapempha nyama ndipo anawapatsa zinziri,+Ankawadyetsa chakudya chochokera kumwamba.+ 41  Anatsegula thanthwe ndipo panatuluka madzi ambiri.+Madziwo anayenda ngati mtsinje kudutsa mʼchipululu.+ 42  Chifukwa iye anakumbukira lonjezo lake loyera limene analonjeza mtumiki wake Abulahamu.+ 43  Choncho Mulungu anatulutsa anthu ake mʼdzikomo anthuwo akusangalala,+Anatulutsa osankhidwa ake akufuula mokondwera. 44  Anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina,+Anatenga zinthu zimene mitundu ina ya anthu inapeza itagwira ntchito mwakhama,+ 45  Anachita zimenezi kuti asunge malangizo ake,+Komanso kusunga malamulo ake. Tamandani Ya!*

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “Nenani zokhudza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nthawi zonse muzifunafuna nkhope yake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Lamulo limene anapereka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Anathyola ndodo zonse zopachikapo mkate.” Nʼkutheka kuti izi ndi ndodo zimene ankazigwiritsa ntchito posunga mkate.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anazunza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zomanga.”
Nʼkutheka kuti akunena Mose ndi Aroni.
Timeneti ndi tizilombo tingʼonotingʼono ta ku Iguputo timene timaluma ngati udzudzu.
Kapena kuti, “malawi a moto.”
Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.