Salimo 106:1-48
106 Tamandani Ya!*
Yamikani Yehova chifukwa iye ndi wabwino.+Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+
2 Ndi ndani amene anganene za ntchito zonse zazikulu za Yehova,Kapena kulengeza zochita zake zonse zotamandika?+
3 Osangalala ndi anthu amene amachita zinthu mwachilungamo,Amene amachita zinthu zolungama nthawi zonse.+
4 Ndikumbukireni inu Yehova, pamene mukusonyeza anthu anu kukoma mtima.+
Ndisamalireni ndi kundipulumutsa,
5 Kuti ndisangalale ndi ubwino umene mumasonyeza osankhidwa anu,+Kuti ndikondwere limodzi ndi mtundu wanu,Ndiponso kuti ndikutamandeni monyadira pamodzi ndi cholowa chanu.
6 Tachimwa mofanana ndi makolo athu.+Tachita zinthu zolakwika, tachita zinthu zoipa.+
7 Makolo athu ku Iguputo, sanayamikire* ntchito zanu zodabwitsa.
Sanakumbukire chikondi chanu chokhulupirika chomwe ndi chochuluka,Koma anapanduka panyanja, pafupi ndi Nyanja Yofiira.+
8 Koma Mulungu anawapulumutsa kuti dzina lake lilemekezedwe,+Kuti mphamvu zake zidziwike.+
9 Iye analamula* ndipo Nyanja Yofiira inauma.Anatsogolera anthu ake kudutsa pakati pa madzi akuya ngati akudutsa mʼchipululu.+
10 Anawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amene ankadana nawo+Ndipo anawawombola mʼmanja mwa mdani.+
11 Madzi anamiza adani awo,Moti panalibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.*+
12 Zitatero anakhulupirira zimene anawalonjeza.+Anayamba kumuimbira nyimbo zomutamanda.+
13 Koma mofulumira anaiwala zimene Mulungu anachita.+Sanadikire kuti Mulungu awapatse malangizo.
14 Iwo anasonyeza mtima wadyera mʼchipululu,+Ndipo anayesa Mulungu mʼchipululumo.+
15 Mulungu anawapatsa zimene anapempha,Koma anawagwetsera matenda amene anawachititsa kuti awonde kwambiri.+
16 Mumsasa, iwo anayamba kuchitira nsanje MoseNdiponso Aroni,+ woyera wa Yehova.+
17 Kenako dziko lapansi linatseguka ndipo linameza Datani,Nʼkukwirira anthu onse amene anali kumbali ya Abiramu.+
18 Moto unayaka pakati pa gulu lawo.Malawi amoto anapsereza oipa.+
19 Iwo anapanga mwana wa ngʼombe ku Horebe,Ndipo anagwadira fano lachitsulo.*+
20 Anasinthanitsa ulemerero wangaNdi chifaniziro cha ngʼombe yamphongo yodya udzu.+
21 Iwo anaiwala Mulungu,+ Mpulumutsi wawo,Amene anachita zinthu zazikulu ku Iguputo,+
22 Amene anachita zodabwitsa mʼdziko la Hamu,+Amene anachita zochititsa mantha pa Nyanja Yofiira.+
23 Iye anangotsala pangʼono kulamula kuti awonongedwe,Koma Mose wosankhidwa wake, anamuchonderera*Kuti asawagwetsere mkwiyo wake wowononga.+
24 Pa nthawiyo iwo ananyoza dziko losiririka,+Ndipo analibe chikhulupiriro pa zimene anawalonjeza.+
25 Anapitiriza kungʼungʼudza mʼmatenti awo.+Iwo sanamvere mawu a Yehova.+
26 Choncho Mulungu anawalumbirira atakweza dzanja lake,Kuti adzachititsa kuti afere mʼchipululu.+
27 Adzachititsa kuti mbadwa zawo ziphedwe ndi anthu a mitundu ina,Ndiponso kuwamwaza mʼmayiko osiyanasiyana.+
28 Kenako iwo anayamba kulambira* Baala wa ku Peori,+Ndipo anadya nsembe zoperekedwa kwa akufa.*
29 Iwo anamukwiyitsa chifukwa cha zochita zawo,+Ndipo pakati pawo panagwa mliri.+
30 Koma Pinihasi ataimirira nʼkuchitapo kanthu,Mliriwo unatha.+
31 Ndipo Pinihasi ankaonedwa kuti ndi wolungamaKu mibadwo yonse mpaka kalekale.+
32 Iwo anamukwiyitsanso pa madzi a ku Meriba,*Moti Mose sizinamuyendere bwino chifukwa cha anthu amenewa.+
33 Iwo anamukwiyitsaNdipo Mose analankhula mosaganiza bwino.+
34 Iwowa sanawononge mitundu ina ya anthu,+Ngati mmene Yehova anawalamulira.+
35 Koma anayamba kusakanikirana ndi anthu a mitundu ina,+Nʼkuyamba* kuchita zinthu ngati mmene iwo ankachitira.+
36 Ankatumikira mafano awo,+Ndipo mafanowo anakhala msampha kwa iwo.+
37 Ankapereka nsembe ana awo aamunaKomanso ana awo aakazi kwa ziwanda.+
38 Ankakhetsa magazi a anthu osalakwa,+Magazi a ana awo aamuna komanso a ana awo aakazi,Amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani.+Ndipo dzikolo linaipa ndi magazi amene iwo anakhetsa.
39 Iwo anakhala odetsedwa chifukwa cha ntchito zawo.Anachita uhule ndi milungu ina chifukwa cha zochita zawo.+
40 Choncho mkwiyo wa Yehova unayakira anthu ake,Ndipo iye anayamba kunyansidwa ndi cholowa chake.
41 Mobwerezabwereza ankawapereka mʼmanja mwa anthu a mitundu ina,+Kuti anthu amene ankadana nawo aziwalamulira.+
42 Adani awo ankawapondereza,Ndipo anali pansi pa ulamuliro wawo.
43 Nthawi zambiri ankawapulumutsa,+Koma iwo ankamupandukira komanso sankamvera,+Ndipo ankawonongedwa chifukwa cha zolakwa zawo.+
44 Koma Mulungu ankaona mavuto amene akukumana nawo+Ndipo ankamva kulira kwawo kopempha thandizo.+
45 Pofuna kuwathandiza iye ankakumbukira pangano lake,Ndipo ankawamvera chisoni* chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika chomwe ndi chachikulu.*+
46 Iye ankachititsa kuti anthu onse amene anawagwira ukapolo+Awamvere chisoni.
47 Tipulumutseni inu Yehova Mulungu wathu,+Ndi kutisonkhanitsa pamodzi kuchokera mʼmitundu ina,+Kuti titamande dzina lanu loyera,Komanso kuti tikutamandeni mosangalala.+
48 Atamandike Yehova, Mulungu wa Isiraeli,Mpaka kalekale.*+
Ndipo anthu onse anene kuti, “Ame!”
Tamandani Ya,*
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
^ Kapena kuti, “sanamvetse tanthauzo la.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anadzudzula.”
^ Kapena kuti, “amene anatsala.”
^ Kapena kuti, “anagwadira chitsulo chosungunula.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anaima pamalo ogumuka pamaso pa Mulungu.”
^ Kapena kuti, “kudzipereka kwa.”
^ Zimenezi ndi nsembe zimene mwina ankapereka kwa anthu akufa kapena milungu yopanda moyo.
^ Kutanthauza, “Kukangana.”
^ Kapena kuti, “Nʼkuphunzira.”
^ Kapena kuti, “chochuluka.”
^ Kapena kuti, “Ndipo ankasintha maganizo.”
^ Kapena kuti, “Kuyambira kalekale mpaka kalekale.”
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.