Salimo 111:1-10

  • Tamandani Yehova chifukwa cha ntchito zake zazikulu

    • Dzina la Mulungu ndi loyera komanso lochititsa mantha (9)

    • Kuopa Yehova ndi nzeru (10)

111  Tamandani Ya!*+ א [Aleph] Ndidzatamanda Yehova ndi mtima wanga wonse+ב [Beth]Pamsonkhano wa anthu owongoka mtima komanso mumpingo. ג [Gimel]   Ntchito za Yehova ndi zazikulu,+ד [Daleth]Anthu onse amene amasangalala nazo amaziphunzira.+ ה [He]   Zochita zake zimasonyeza ulemerero ndi ulemu,ו [Waw]Ndipo chilungamo chake chidzakhalapobe kwamuyaya.+ ז [Zayin]   Iye amachititsa kuti ntchito zake zodabwitsa zizikumbukiridwa.+ ח [Heth] Yehova ndi wokoma mtima* ndiponso wachifundo.+ ט [Teth]   Iye amapereka chakudya kwa anthu amene amamuopa.+ י [Yod] Amakumbukira pangano lake mpaka kalekale.+ כ [Kaph]   Waululira anthu ake ntchito zake zamphamvuל [Lamed]Powapatsa cholowa cha anthu a mitundu ina.+ מ [Mem]   Ntchito za manja ake zimadziwika ndi choonadi ndiponso chilungamo.+נ [Nun]Malamulo onse amene amapereka ndi odalirika.+ ס [Samekh]   Ndi odalirika* nthawi zonse, kuyambira panopa mpaka kalekale.ע [Ayin]Maziko ake ndi choonadi komanso chilungamo.+ פ [Pe]   Wawombola anthu ake.+ צ [Tsade] Walamula kuti pangano lake likhalepo mpaka kalekale. ק [Qoph] Dzina lake ndi loyera komanso lochititsa mantha.+ ר [Resh] 10  Chiyambi cha nzeru ndi kuopa Yehova.+ ש [Sin] Onse otsatira malamulo ake amasonyeza kuti ndi ozindikira.+ ת [Taw] Iye ayenera kutamandidwa mpaka kalekale.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “wachisomo.”
Kapena kuti, “Ali pa maziko olimba.”