Salimo 114:1-8

  • Kupulumutsidwa kwa Aisiraeli kuchoka ku Iguputo

    • Nyanja inathawa (5)

    • Mapiri anadumphadumpha ngati nkhosa zamphongo (6)

    • Mwala wa nsangalabwi unakhala kasupe (8)

114  Isiraeli atatuluka mu Iguputo,+Nyumba ya Yakobo itatuluka pakati pa anthu olankhula chilankhulo chachilendo,   Yuda anakhala malo ake opatulika,Ndipo Isiraeli linakhala dziko limene ankalilamulira.+   Nyanja inaona zimenezi ndipo inathawa,+Yorodano anabwerera mʼmbuyo.+   Mapiri anadumphadumpha ngati nkhosa zamphongo,+Zitunda zinadumphadumpha ngati ana a nkhosa.   Nʼchiyani chinakupangitsa kuti uthawe, nyanja iwe?+ Nʼchifukwa chiyani iwe Yorodano unabwerera mʼmbuyo?+   Nanga inu mapiri, nʼchifukwa chiyani munkadumphadumpha ngati nkhosa zamphongo?Inunso zitunda, nʼchifukwa chiyani munkadumphadumpha ngati ana a nkhosa?   Iwe dziko lapansi, njenjemera chifukwa cha Ambuye,Chifukwa cha Mulungu wa Yakobo,+   Amene amasintha thanthwe kukhala dambo la madzi,Komanso mwala wa nsangalabwi kukhala akasupe a madzi.+

Mawu a M'munsi